YOHANE Mau Oyamba
Mau Oyamba
Mu buku la Yohane akumuonetsa Yesu monga Mau amuyaya a Mulungu, amene “anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife.” (1.14) Monga momwe bukuli likunenera, Uthengawo unalembedwa owerenga akhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m'dzina lake (20.31).
Atatha kunena mau oyamba amene akufanizira Yesu ndi mau osatha a Mulungu, gawo loyamba la Uthengawu likutionetsa zozizwitsa zosiyanasiyana zimene zikutitsimikizirra kuti Yesu ndiye Mpulumutsi Wolonjezedwa uja, amene ali Mwana wa Mulungu. Kenaka izi zikutsatidwa ndi maneno osiyanasiyana amene akufotokoza tanthauzo la zozizwitsazo. Pa ndime zimenezi, afotokozanso kuti anthu ena anakhulupirira Yesu namutsata, pamene ena sanafune kumkhulupirira. Mutu 13 mpaka 17 anena mwachimvekere za chiyanjano chozama chimene chinalipo pakati pa Yesu ndi ophunzira ake pa usiku umene iye anagwidwa, komanso mawu achilimbikitso amene Iye anawauza asanakhomedwe pamtanda mawa lake. Mitu yotsirizira inena za kugwidwa, kuzengedwa mlandu ndi kupachikidwa pamtanda komanso kuukanso kwa Yesu, ndiponso pamene Iye anaonekera kwa ophunzira ake ataukitsidwa.
Yohane akutsindika za mphatso ya moyo wosatha mwa Yesu, ndipo mphatso imeneyi imayamba panopa ndi kuperekedwa kwa anthu amene avomera Yesu monga njira, choonadi ndi moyo (14.6). Chinthu chimene chofunikira kwambiri mu buku la Yohane ndicho kufotokozera zinthu zauzimu pogwiritsidwa ntchito zinthu zimene timazidziwa masiku onse monga madzi, chakudya, kuwala, mbusa ndi nkhosa zake, mphesa ndi zipatso zake. Ndipo kuchokera pa zinthu zoonekazo, bukuli limathandiza anthu okhulupirira kuti azindikire ndi kukopeka ndi zabwino zobisika zokhudza Mulungu ndi ufumu wake.
Za mkatimu
Chiyambi 1.1-18
Yohane Mbatizi ndi ophunzira oyamba a Yesu 1.19-51
Utumiki wa Yesu 2.1—12.50
Masiku omaliza mu Yerusalemu ndi madera oyandikira 13.1—17.26
Yesu agwidwa, nazengedwa mlandu, nafa pamtanda 18.1—19.42
Yesu auka kwa akufa naonekera ophunzira ake 20.1-31
Mau otsiriza: Yesu aonekeranso ophunzira ake ku Galileya 21.1-25
Pašlaik izvēlēts:
YOHANE Mau Oyamba: BLPB2014
Izceltais
Dalīties
Kopēt
Vai vēlies, lai tevis izceltie teksti tiktu saglabāti visās tavās ierīcēs? Reģistrējieties vai pierakstieties
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi