Lk. 22

22
Upo wopangana za kupha Yesu
(Mt. 26.1-5, 14-16; Mk. 14.1-2, 10-11; Yoh. 11.45-53)
1 # Eks. 12.1-27 Nthaŵi yochitira chikondwerero cha buledi wosafufumitsa inkayandikira. Chikondwererocho chimatchedwa Paska. 2Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti aphere Yesu. Paja iwo ankaopa anthu.
Yudasi apangana ndi akulu a Ayuda za kupereka Yesu
(Mt. 26.14-16; Mk. 14.10-11)
3Tsono Satana adamuloŵa Yudasi wotchedwa Iskariote, amene anali mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja a Yesu. 4Yudasiyo adapita kukapangana ndi akulu a ansembe ndi atsogoleri a alonda a ku Nyumba ya Mulungu za njira yoti aperekere Yesu kwa iwo. 5Iwo adakondwa, nalonjeza kumpatsa ndalama. 6Yudasi adavomera, nayamba kufunafuna mpata woti amuperekere kwa iwo, anthu onse osadziŵa.
Yesu akonzekera kuchita phwando la Paska
(Mt. 26.17-25; Mk. 14.12-21; Yoh. 13.21-30)
7Tsiku la buledi wosafufumitsa lidafika, ndiye kuti tsiku limene anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska. 8Yesu adatuma Petro ndi Yohane naŵauza kuti, “Pitani mukatikonzere phwando la Paska kuti tikadye.” 9Koma iwo adamufunsa kuti, “Kodi tikakonzere kuti?” 10Yesu adati, “Mvetsani! Mukangoloŵa m'mudzimu, mukumana ndi munthu wamwamuna atasenza mtsuko wa madzi. Mukamtsatire mpaka kunyumba kumene akaloŵe. 11Mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda chimene Iwowo adzadyeremo phwando la Paska ndi ophunzira ao?’ 12Iyeyo akakuwonetsani chipinda chachikulu cham'mwamba, momwe akonzamo zonse zofunikira. M'menemo mukatikonzere chakudya.” 13Tsono iwo adapita nakachipezadi monga momwe adaaŵauzira, ndipo adakonza phwando la Paska.
Za mgonero wa Ambuye
(Mt. 26.26-30; Mk. 14.22-26; 1 Ako. 11.23-25)
14Nthaŵi itakwana, Yesu adakakhala podyera pamodzi ndi atumwi ake aja. 15Tsono adaŵauza kuti, “Ndafunitsitsa kudya phwando ili la Paska pamodzi ndi inu ndisanayambe kumva zoŵaŵa. 16Pakuti kunena zoona, sindidzadyanso konse Paska, mpaka Paskayi itadzafika pake penipeni mu Ufumu wa Mulungu.”
17Atatero Yesu adatenga chikho, ndipo atathokoza Mulungu, adati, “Kwayani, imwani nonsenu. 18Ndithu ndikunenetsa kuti kuyambira tsopano sindidzamwanso konse chakumwa cha mtengo wamphesa, mpaka Mulungu atadzakhazikitsa ufumu wake.”
19Kenaka Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.” 20#Yer. 31.31-34Atatha kudya, adaŵapatsanso chikho, nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chimene magazi anga, omwe akukhetsedwa chifukwa cha inu, akuchitsimikizira.
21 # Mas. 41.9 “Koma ndithudi wondipereka kwa adani akudya nane pamodzi pompano. 22Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Mulungu adazikonzeratu kale. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo.” 23Apo onse adayamba kumafunsana kuti, “Kodi ndani mwa ife angachite zotere?”
Ophunzira atsutsana za ukulu
24 # Mt. 18.1; Mk. 9.34; Lk. 9.46 Tsono ophunzira aja adayamba kutsutsana kuti, “Kodi mwa ife amati wamkulu ndani?” 25Yesu adaŵauza kuti, “Pakati pa anthu akunja, mafumu amadyera anthu ao masuku pa mutu, ndipo amene amaŵaonetsa mphamvu zao, amatchedwa mfulu zopatsa.” 26#Mt. 23.11; Mk. 9.35#Mt. 20.25-27; Mk. 10.42-44Koma pakati pa inu zisamatero ai. Kwenikweni wamkulu mwa inu azikhala ngati wamng'ono mwa onse, ndipo mtsogoleri azikhala ngati wotumikira. 27#Yoh. 13.12-15Kodi wamkulu ndani? Ndi amene alikudya, kapena amene akumtumikira? Si amene alikudyayo nanga? Koma Ine ndili pakati panu ngati wotumukira.
28“Inu ndinu amene mwakhala ndi Ine pa masautso anga onse. 29Nchifukwa chake, monga Atate anga adandipatsa ufumu, Inenso ndikukupatsani ufumu. 30#Mt. 19.28Ndikadzaloŵa mu ufumu wanga, muzidzadya ndi kumwa pamodzi nane, ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu nkumaweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israele.”
Yesu aneneratu kuti Petro adzamkana
(Mt. 26.31-35; Mk. 14.27-31; Yoh. 13.36-38)
31“Simoni, Simoni, chenjera! Mulungu walola Satana kuti akupeteni nonse ngati tirigu. 32Koma Ine ndakupempherera, kuti usaleke kundikhulupirira. Ndipo iweyo utatembenuka mtima, ukaŵalimbitse abale akoŵa.” 33Apo Petro adati, “Ambuye, ndili wokonzeka kupita nanu ku ndende, ngakhale kufa kumene.” 34Koma Yesu adamuyankha kuti, “Ndikukuuza, iwe Petro, kuti lero lomwe lino, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.”
Za kutenga matumba ndiponso lupanga
35 # Mt. 10.9, 10; Mk. 6.8, 9; Lk. 9.3; 10.4 Yesu adaŵafunsa kuti, “Nthaŵi ina ndidaakutumani opanda thumba la ndalama, kapena thumba lapaulendo, kapenanso nsapato. Kodi pamene paja mudaasoŵapo kanthu?” Iwo adati, “Iyai.” 36Yesu adaŵauza kuti, “Koma tsopano amene ali ndi thumba la ndalama, asalisiye. Chimodzimodzinso thumba lake lapaulendo. Ndipo amene alibe lupanga, agulitse mwinjiro wake nkugula lupanga. 37#Yes. 53.12 Ndithu ndikunenetsa kuti ziyenera kuchitikadi mwa Ine zimene Malembo adanena kuti, ‘Ankamuyesa mmodzi mwa anthu ophwanya malamulo.’ Ndipo zonse zimene zidalembedwa za Ine zikuchitikadi.” 38Ophunzirawo adati, “Ambuye, aŵa malupanga, tili nawo kale aŵiri.” Yesu adaŵauza kuti, “Chabwino, basi.”
Pemphero la Yesu pa Phiri la Olivi
(Mt. 26.36-46; Mk. 14.32-42)
39Pambuyo pake Yesu adatuluka mu mzinda napita ku Phiri la Olivi monga adaazoloŵera. Ndipo ophunzira ake adapita naye. 40Pamene adafika kumeneko, Yesu adaŵauza kuti, “Pempherani, kuti mungagwe m'zokuyesani.” 41Tsono adapatukana nawo kadera, kutalika kwake ngati pamene mwala ungafike munthu atauponya. Apo adagwada pansi nayamba kupemphera. 42Adati, “Atate, ngati mukufuna, mundichotsere chikho chamasautsochi. Komabe muchite zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.” 43[Pamenepo mngelo wochokera Kumwamba adamuwonekera namlimbitsa mtima. 44Koma Yesu adavutikabe koopsa mu mtima, nkumapemphera kolimba kuposa kale. Ndipo thukuta limene ankadza linali ngati madontho akuluakulu a magazi ogwera pansi.]
45Atapemphera, adaimirira napita kwa ophunzira ake. Adaŵapeza ali m'tulo chifukwa cha chisoni, 46ndipo adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukugona? Dzukani ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani.”
Yesu agwidwa
(Mt. 26.47-56; Mk. 14.43-50; Yoh. 18.3-11)
47Yesu akulankhula choncho, padabwera khamu la anthu. Amene ankaŵatsogolera anali Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Iyeyu adadza pafupi ndi Yesu kuti amumpsompsone. 48Koma Yesu adamufunsa kuti, “Yudasi, mongadi ukupereka Mwana wa Munthu kwa adani pakumumpsompsona?”#22.48: pakumumpsompsona: Kwa mitundu ina ya anthu kumpsompsona ndi chizindikiro cha chikondi chenicheni polonjerana. 49Ophunzira amene anali pafupi ndi Yesu ataona zimene zinalikudzachitika, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi tiŵateme ndi lupanga?” 50Apo mmodzi mwa iwo adatemadi wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu la ku dzanja lamanja. 51Koma Yesu adati, “Basi, lekani zimenezi.” Atatero adakhudza khutu la munthuyo namchiritsa.
52Kenaka Yesu adalankhula nawo onse amene adaabwera kudzamugwira, akulu a ansembe ndi atsogoleri a alonda a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso akulu a Ayuda. Adaŵafunsa kuti, “Bwanji mwachita kunditengera malupanga ndi zibonga ngati kuti ndine chigaŵenga? 53#Lk. 19.47; 21.37Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m'Nyumba ya Mulungu, inuyo osandigwira. Koma ino ndi nthaŵi yanu ndiponso ya mphamvu za mdima.”
Petro akana Yesu
(Mt. 26.57-58, 69-75; Mk. 14.53-54, 66-72; Yoh. 18.12-18, 25-27)
54Anthu aja adamugwira Yesu, napita naye ku nyumba ya mkulu wa ansembe onse. Petro ankaŵatsatira chapatali. 55Iwo adasonkha moto m'kati mwa bwalo la nyumbayo, nakhala pansi pamodzi. Petro nayenso adakakhala pakati pao. 56Mtsikana wina wantchito adamuwona atakhala nao pamotopo. Adamuyang'anitsitsa, nati, “Aŵansotu anali naye.” 57Koma Petro adakana, adati, “Mai iwe, sindimdziŵa ameneyu.” 58Patapita kanthaŵi pang'ono, munthu wina pomuwona adati, “Akulu inu, ndinunso mmodzi mwa iwo aja.” Koma Petro adati, “Munthu iwe, ai ndithu sindine.” 59Patapita ngati ora limodzi, munthu winanso adanenetsa kuti, “Ndithudi akulu aŵanso anali naye, pakuti ndi a ku Galileya.” 60Koma Petro adati, “Munthu iwe, sindikuzidziŵa zimene ukunenazi.” Ndipo pompo, akulankhulabe, tambala adalira. 61Ambuye adacheuka nayang'ana Petro. Pamenepo Petro adakumbukira mau aja amene Ambuye adaamuuza kuti, “Lero lomwe lino, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu.” 62Pamenepo adatuluka, nakalira kwambiri chifukwa cha chisoni chachikulu.
Aseka Yesu nkumamumenya
(Mt. 26.67-68; Mk. 14.65)
63Tsono anthu amene ankalonda Yesu aja adayamba kumseka ndi kumammenya. 64Adammanga nsalu m'maso nkumamufunsa kuti, “Lota, wakumenya ndani?” 65Ndipo adamnenanso mau ena ambiri achipongwe.
Yesu ku Bwalo Lalikulu la Ayuda
(Mt. 26.59-66; Mk. 14.55-64; Yoh. 18.19-24)
66Kutacha, a m'Bungwe Lalikulu la Ayuda adasonkhana, ndiye kuti akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Adatenga Yesu napita naye ku Bwalo lao. 67Adamuuza kuti, “Ngati ndiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, utiwuze mosabisa.” Koma Iye adaŵayankha kuti, “Ngakhale ntakuuzani, simungandikhulupirire konse, 68ndipo nditakufunsani funso, inu simungaliyankhe. 69Koma kuyambira tsopano Mwana wa Munthune ndidzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu#22.69: ku dzanja lamanja la Mulungu: Ameneŵa ndiwo malo a mphamvu ndi ulemu. wamphamvuzonse.” 70Apo onse aja adati, “Tsono ndiye kutitu ndiwe Mwana wa Mulungu, ati?” Yesu adati, “Mwanena nokha kuti ndine amene.” 71Pamenepo iwo aja adati, “Tikufuniranji umboni wina? Tadzimvera tokha mau akeŵa.”

ಪ್ರಸ್ತುತ ಆಯ್ಕೆ ಮಾಡಲಾಗಿದೆ:

Lk. 22: BLY-DC

Highlight

ಶೇರ್

ಕಾಪಿ

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in