Lk. 20

20
Afunsa Yesu za ulamuliro wake
(Mt. 21.23-27; Mk. 11.27-33)
1Tsiku lina Yesu ankaphunzitsa anthu m'Nyumba ya Mulungu nkumalalika Uthenga Wabwino. Tsono akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndiponso akulu a Ayuda adabwera 2namufunsa kuti, “Mutiwuze, kodi mphamvu zoti muzichita zimenezi mudazitenga kuti? Kaya ndani adakupatsani mphamvu zimenezi?” 3Yesu adati, “Nanenso ntakufunsani funso limodzi. Tandiwuzani, 4kodi Yohane Mbatizi kuti azibatiza, mphamvu zake adaazitenga kwa yani, kwa Mulungu kapena kwa anthu?” 5Iwo aja adayamba kukambirana nkumati, “Tikati adaazitenga kwa Mulungu, Iyeyu anena kuti, ‘Nanga bwanji tsono sumudamkhulupirire?’ 6Komanso tikati adaazitenga kwa anthu, anthu onseŵa atiponya miyala, chifukwa mumtima mwao amatsimikiza kuti Yohane adaali mneneri.” 7Ndiye adangomuyankha kuti, “Kaya, ife sitikudziŵa kumene adaazitenga.” 8Apo Yesu adati, “Nanenso tsono sindikuuzani kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.”
Fanizo la antchito olima m'munda wamphesa
(Mt. 21.33-46; Mk. 12.1-12)
9 # Yes. 5.1 Pamenepo Yesu adaphera anthu aja fanizo lina. Adati, “Munthu wina adaalima munda wamphesa. Adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina, nakakhalako nthaŵi yaitali. 10Nyengo yothyola zipatso itafika, munthu uja adatuma wantchito wake kwa alimi aja, kuti akampatsireko zipatso za m'munda muja. Koma alimiwo adammenya, nkumubweza osampatsa kanthu. 11Adatumanso wantchito wina. Nayenso alimi aja adammenya, namchita chipongwe, nkumubweza osampatsa kanthu. 12Adatumanso wachitatu, koma uyunso alimiwo adamuvulaza, namtaya kunja. 13Pambuyo pake mwini munda uja adati, ‘Ndichite chiyani tsopano? Ndidzatuma mwana wanga amene ndimamkonda uja. Mwina mwake iye yekhayu akamchitira ulemu.’ 14Koma alimi aja atamuwona, adayamba kuuzana kuti, ‘Uyu ndiye amene adzamsiyire chumachi. Tiyeni timuphe kuti chidzakhale chathu.’ 15Tsono adamuponya kunja kwa mundawo, namupha. Kodi mwini munda wamphesa uja adzaŵatani alimi aja? 16Ndithu adzabwera naŵapha alimiwo, munda uja nkuubwereka ena.”
Anthu aja atamva zimenezi adati, “Ai, msatero.”
17 # Mas. 118.22 Koma Yesu adaŵayang'ana nati, “Nanga tsono tanthauzo lake nchiyani Malembo aŵa akuti,
“ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana,
womwewo wasanduka mwala wapangodya,
wofunika koposa?’
18Aliyense wogwera pa mwala umenewo adzathyokathyoka. Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere, udzangomutswanyiratu.”
Za kukhoma msonkho
(Mt. 22.15-22; Mk. 12.13-17)
19Aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a ansembe adaadziŵa kuti fanizolo Yesu ankaphera iwowo. Nchifukwa chake ankafuna kumugwira nthaŵi yomweyo, koma ankaopa anthu. 20Tsono iwo ankangomuŵenda, choncho adatuma anthu omuzonda, odziwonetsa ngati anthu olungama, kuti akamutape m'kamwa. Ankafuna kukamneneza kwa bwanamkubwa, pakuti iyeyo ndiye anali ndi mphamvu ndi ulamuliro wonse. 21Ozondawo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumalankhula ndi kuphunzitsa molungama, simuyang'anira kuti uyu ndani. Mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona. 22Kodi Malamulo a Mulungu amatilola kuti tizikhoma msonkho kwa Mfumu ya ku Roma, kapena ai?” 23Koma Yesu podziŵa maganizo ao andale adati, 24“Tandiwonetsani ndalama. Kodi ili ndi nkhope ya yani, ndipo ili ndi dzina la yani?” 25Iwo aja adati, “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.” Apo Yesu adaŵauza kuti, “Tsono perekani kwa Mfumu zake za Mfumu, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulungu.” 26Choncho adalephera kumutapa m'kamwa pamaso pa anthu pa zimene Iye adalankhula. Iwo adathedwa nzeru ndi zimene Yesu adaayankha, nkungoti chete.
Za kuuka kwa akufa
(Mt. 22.23-33; Mk. 12.18-27)
27 # Ntc. 23.8 Asaduki ena adadza kwa Yesu. Paja iwo amati akufa sadzauka. Adamufunsa Yesu kuti, 28#Deut. 25.5 “Aphunzitsi, Mose adatilembera lamulo lakuti, ‘Ngati munthu amwalira, nasiya mkazi wake, koma opanda ana, mbale wake wa womwalirayo aloŵe chokolo, kuti amuberekere ana mbale wake uja.’ 29Tsono padaali anthu asanu ndi aŵiri pachibale pao. Woyamba adaakwatira mkazi, koma adamwalira osamsiyira mwana. 30Chimodzimodzinso wachiŵiri, 31ndipo wachitatu nayenso adaloŵa chokolo. Onse aja asanu ndi aŵiri adachita chimodzimodzi, koma onse adamwalira osamsiyira ana mkaziyo. 32Potsiriza pake mai uja nayenso adamwalira. 33Nanga tsono pa tsiku lodzauka akufa, mwini mkaziyo adzakhala utiwuti, popeza kuti abale asanu ndi aŵiri onse aja adaamkwatirapo?”
34Yesu adaŵayankha kuti, “Anthu okhala pansi pano amakwatira ndi kukwatiwa. 35Koma amene amaŵayesa oyenera kukakhala ndi moyo kutsogoloko, anthu atauka kwa akufa, sadzakwatiranso kapena kukwatiwa ai. 36Iwo adzakhala ngati angelo, mwakuti sangafenso ai. Iwo ndi ana a Mulungu popeza kuti Iye adaŵaukitsa kwa akufa. 37#Eks. 3.6 Koma zakuti anthu adzauka kwa akufa, Mose yemwe adaanenapo kale. Paja pa mbiri ija ya chitsamba choyaka moto, iye akuŵatchula Ambuye kuti, ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe.’ 38Ndiye kutitu sali Mulungu wa anthu akufa ai, koma wa anthu amoyo, chifukwa kwa Iye anthu onsewo ndi amoyo.”
39Apo ena mwa aphunzitsi a Malamulo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, mwanena bwino.” 40Adaatero popeza kuti Asaduki aja sadalimbenso mtima kuti amufunse mafunso ena.
Za Mpulumutsi wolonjezedwa uja
(Mt. 22.41-46; Mk. 12.35-37)
41Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi inu, bwanji amati Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndi mwana wa Davide? 42#Mas. 110.1 Paja Davide yemwe m'buku la Masalimo akuti,
“ ‘Chauta adauza Mbuye wanga kuti:
Khala ku dzanja langa lamanja
43mpaka nditasandutsa adani ako
kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’
44“Davide akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake. Tsono angakhale mwana wakenso bwanji?”
Yesu achenjeza anthu za aphunzitsi a Malamulo
(Mt. 23.1-36; Mk. 12.38-40; Lk. 11.37-54)
45Pamene anthu onse ankamvetsera zimene Yesu ankalankhula, Iye adauza ophunzira ake kuti, 46“Chenjera nawoni aphunzitsi a Malamulo. Amakonda kuyenda atavala mikanjo yaitali, ndi kuti anthu aziŵalonjera mwaulemu pa misika. Amakonda mipando yaulemu kwambiri m'nyumba zamapemphero ndiponso malo olemekezeka pa maphwando. 47Koma amaŵadyera chuma chao azimai amasiye, nkumapemphera mapemphero ataliatali monyengezera. Anthu ameneŵa adzalangidwa koposa.”

ಪ್ರಸ್ತುತ ಆಯ್ಕೆ ಮಾಡಲಾಗಿದೆ:

Lk. 20: BLY-DC

Highlight

ಶೇರ್

ಕಾಪಿ

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in