Lk. 15

15
Fanizo la nkhosa yotayika
(Mt. 18.12-14)
1 # Lk. 5.29, 30 Anthu onse okhometsa msonkho ndi Ayuda enanso onyozera Malamulo ankabwera kwa Yesu kudzamva mau ake. 2Tsono Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo adayamba kuŵinya nkumanena kuti, “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa, nkumadya nawo pamodzi.”
3Tsono Yesu adaŵaphera fanizo ili, adati, 4“Ndani mwa inu ali ndi nkhosa 100, imodzi itatayikapo, sangasiye nkhosa zina zonse 99 zija ku busa, nkukafunafuna yotayikayo mpaka ataipeza? 5Ndipo ataipeza, amaisenza pamapewa pake mokondwa. 6Pofika kwao, amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, naŵauza kuti, ‘Mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndaipeza nkhosa yanga idaatayika ija.’ ” 7Yesu adapitiriza mau kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti momwemonso Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima, kuposa anthu olungama 99 amene alibe chifukwa chotembenukira mtima.”
Fanizo la ndalama yotayika
8“Mwinanso mai amakhala ndi tindalama khumi, kamodzi nkutayika. Kodi suja amayatsa nyale nasesasesa m'nyumba nkufunafuna mosamala mpaka atakapeza? 9Atakapeza amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, naŵauza kuti, ‘Mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndakapeza kandalama kanga kaja kadaatayikaka.’ ” 10Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.”
Fanizo la mwana wotayika
11Yesu adatinso, “Munthu wina adaali ndi ana aamuna aŵiri. 12Wamng'ono adapempha bambo wake kuti, ‘Atate, bwanji mugaŵiretu tsopano chuma chanu, ine mundipatsiretu chigawo changa.’ Bamboyo adaŵagaŵiradi ana ake aja chuma chake. 13Patangopita masiku oŵerengeka wamng'ono uja adagulitsa chigawo chake chonse, nachoka kwaoko ndi ndalama zake kupita ku dziko lakutali. Kumeneko adamwaza chuma chakecho ndi mayendedwe oipa. 14Chitamthera chuma chake chonse, mudaloŵa njala yaikulu m'dziko limeneli, mwakuti iye yemwe adayamba kusauka. 15Pamenepo adapita kukakhala nao kwa nzika ina ya m'dzikomo. Nzikayo idamtuma ku busa kukaŵeta nkhumba zake. 16Mnyamata uja ankalakalaka kudya makoko amene nkhumba zinkadya, koma panalibe munthu wompatsako ngakhale makokowo.
17“Atakhalakhala adadzidzimuka mumtima mwake, ndipo adati, ‘Achulukirenji antchito a bambo wanga amene ali ndi chakudya chokwanira mpaka kutsalako, pamene ine kuno ndikufa ndi njala. 18Basi ndinyamuka, ndipita kwa bambo wanga, ndipo ndikanena kuti: Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. 19Sindili woyenera kutchedwanso mwana wanu. Mundilole ndisanduke mmodzi mwa antchito anu.’
20“Choncho adanyamukadi napita kwa bambo wake. Koma akubwera patali, bambo wake adamuwona, namumvera chisoni. Adamthamangira, namkumbatira, nkumamumpsompsona. 21Mwanayo adati, ‘Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kuchedwanso mwana wanu.’ 22Koma bambo wake adauza antchito ake kuti, ‘Thamangani mukatenge mkanjo wabwino kwambiri, mumuveke. Mumuvekenso mphete ku chala, ndi nsapato ku mapazi. 23Ndipo katengeni mwanawang'ombe wonenepa uja, muphe kuti tidye, tikondwere. 24Chifukwa mwana wangayu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka.’ Ndiye pompo chikondwerero chidayamba.
25“Koma mwana wake wamkulu uja anali ku munda. Pochokera kumundako, atafika pafupi ndi nyumba, adamva anthu akuimba ndi kuvina. 26Adaitana wantchito mmodzi namufunsa kuti, ‘Kodi kwagwanji?’ 27Iye adati, ‘Mng'ono wanu uja wabwera, ndiye bambo apha mwanawang'ombe wonenepa uja chifukwa amlandira ali wamoyo.’ 28Atamva zimenezo mwana wamkuluyo adapsa mtima, nakana kuloŵa. Apo bambo wake adatuluka, nkumupempha mopemba kuti aloŵe. 29Koma iye adayankha bambo akewo kuti, ‘Ine zaka zonsezi ndakhala ndikukugwirirani ntchito ndipo sindidalakwirepo lamulo lanu. Komabe inu simudandipatsepo ndi katonde komwe kuti ndikondwere pamodzi ndi anzanga. 30Koma mwana wanuyu, chuma chanu chonse adaonongera akazi achiwerewere, ndipo pamene wabwera, mwamuphera mwanawang'ombe wonenepa uja!’
31“Bambo wakeyo adamuyankha kuti, ‘Mwana wanga, iwe uli ndi ine nthaŵi zonse, ndipo zanga zonse nzako. 32Kunayenera kuti tikondwere ndi kusangalala, chifukwa mng'ono wakoyu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka.’ ”

ಪ್ರಸ್ತುತ ಆಯ್ಕೆ ಮಾಡಲಾಗಿದೆ:

Lk. 15: BLY-DC

Highlight

ಶೇರ್

ಕಾಪಿ

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in