Yoh. 5
5
Yesu achiritsa munthu ku Betesida
1Pambuyo pake kunali chikondwerero chachipembedzo cha Ayuda, ndipo Yesu adapitako ku Yerusalemuko. 2Kumeneko kuli dziŵe, dzina lake pa Chiyuda ndi Betesida. Dziŵeli lili pafupi ndi Chipata cha Nkhosa,#5.2: Chipata cha Nkhosa: Ndi chipata china m'linga lozungulira Yerusalemu. Zoŵeta zoti azipereka nsembe zinkaloŵera pa chipata chimenechi m'Yerusalemu (Neh. 3.1;12.39) ndipo nlozingidwa ndi makonde asanu. 3M'makondemo munkagona anthu ambiri odwala, akhungu, opunduka miyendo ndi opuwala ziwalo. [Iwoŵa ankadikira kuti madzi agwedezeke. 4Pakuti nthaŵi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira m'dziŵemo nkuvundula madziwo. Woyamba kuloŵamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji.] 5Pakati pa anthu odwalawo panali wina amene adaadwala zaka 38. 6Yesu adamuwona ali gone, nadziŵa kuti adaadwala nthaŵi yaitali. Tsono adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuchira?” 7Wodwalayo adati, “Ambuye, ndilibe munthu wondiloŵetsa m'dziŵemu madzi akavundulidwa. Ndikati ndiloŵemo, wina waloŵa kale.” 8Yesu adamlamula kuti, “Dzuka, tenga mphasa yako, yamba kuyenda.” 9Pompo munthuyo adachiradi, nanyamula mphasa yake nkuyamba kuyenda.
Tsikulo linali la Sabata. 10#Neh. 13.19; Yer. 17.21Choncho Ayuda adauza munthu amene adachirayo kuti, “Lero mpa Sabata. Malamulo athu sakulola kunyamula mphasa yako.” 11Koma iye adati, “Amene wandichiritsa ndiye wandiwuza kuti, ‘Nyamula mphasa yako, yenda.’ ” 12Iwo adamufunsa kuti, “Munthuyo ndani amene wakuuza kuti unyamule mphasa yako, uyende?” 13Koma wochirayo sadamdziŵe, popeza kuti Yesu anali ataloŵerera m'kati mwa anthu ambiri amene anali pamenepo.
14Pambuyo pake Yesu adapeza wochira uja m'Nyumba ya Mulungu, namuuza kuti, “Ona, wachira tsopano. Usakachimwenso, kuti chingakugwere choopsa china kuposa pamenepa.” 15Munthuyo adapita nakauza Ayuda kuti Yesu ndiye amene wamchiritsa.
16Popeza kuti linali tsiku la Sabata pamene Yesu adaachita zimenezi, Ayuda adayamba kumuvutitsa. 17Koma Yesu adaŵauza kuti, “Atate anga akugwira ntchito mpaka tsopano, nanenso ndikugwira ntchito.” 18#Lun. 2.16Pamenepo ndiye Ayuda adankirankira kufuna kumupha. Ankati Yesu akuphwanya lamulo lokhudza Sabata, ndiponso ponena kuti Mulungu ndi Atate ake, ankadzilinganiza ndi Mulungu.
Ulamuliro wa Mwana wa Mulungu
19Tsono Yesu adati, “Kunena zoona Ine Mwanane sindingathe kuchita kanthu pandekha. Ndimangochita zimene ndikuwona Atate anga akuchita. Zimene Atate amachita, Mwana amachitanso zomwezo. 20Pakuti Atate amakonda Mwana, namuwonetsa zonse zimene Iwo akuchita. Atate adzamuwonetsanso ntchito zoposa zimenezi, kuti inu muzizwe. 21Monga Atate amaukitsa akufa, naŵapatsa moyo, moteronso Mwana amapatsa moyo kwa amene Iye afuna. 22Atate saweruza munthu aliyense, koma adaika Mwana wake kuti akhale woweruza pa zonse. 23Atate amafuna kuti anthu onse azilemekeza Mwana, monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana, salemekezanso Atate amene adamtuma.
24“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo. 25Ndikunenetsanso kuti ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu amene ali ngati akufa adzamva mau a Mwana wa Mulungu, ndipo amene adzaŵakhulupirira adzakhala ndi moyo. 26Monga Atate ali gwelo la moyo, momwemonso adaika Mwana wake kuti nayenso akhale gwelo la moyo. 27Ndipo adapatsa Mwanayo mphamvu ya kuweruza anthu, chifukwa ndi Mwana wa Munthu. 28Musadabwe nazo zimenezi, pakuti ikudza nthaŵi pamene anthu onse amene ali m'manda adzamva mau ake nadzatuluka. 29#Dan. 12.2Anthu amene adachita zabwino, adzauka kuti akhale ndi moyo, koma amene adachita zoipa, adzauka kuti azengedwe mlandu.”
Ochitira Yesu umboni
30“Ine sindingathe kuchita kanthu pandekha. Ndimaweruza monga momwe Atate amandiwuzira. Ndipo ndimaweruza molungama, popeza kuti sinditsata zimene ndifuna Ineyo, koma zimene afuna Atate amene adandituma.
31“Ngati ndidzichitira ndekha umboni, umboni wangawo ngwosakwanira. 32Pali wina wondichitira umboni, ndipo ndikudziŵa kuti umboni umene iye amandichitirawo ngwoona. 33#Yoh. 1.19-27; 3.27-30Inu nomwe mudaatuma amithenga anu kwa Yohane Mbatizi, ndipo iye adachitira umboni choona. 34Sikuti Ine ndikudalira umboni wa munthu, koma ndikunena izi kuti inu mupulumuke. 35#Mphu. 48.1Yohane anali ngati nyale yoyaka ndi yoŵala, ndipo inu mudafuna kukondwerera kuŵala kwakeko pa kanthaŵi. 36Koma Ine ndili ndi umboni woposa wa Yohane. Atate adandipatsa ntchito zimene ndiyenera kuzichita, ndipo ntchito ndikuchitazi zikutsimikiza kuti Atate ndiwo adandituma. 37#Mt. 3.17; Mk. 1.11; Lk. 3.22Ndipo Atate omwewo amene adandituma, adandichitira umboni. Koma inu simudamve konse liwu lao, maonekedwe aonso simudaŵaone. 38Mau ao sakhala mwa inu, chifukwa simumkhulupirira amene Atatewo adamtuma. 39#Bar. 4.1Mumaphunzira Malembo mozama, chifukwa mumaganiza kuti mupezamo moyo wosatha. Ndipotu ndi Malembo omwewo amene akundichitira umboni! 40Komabe inu simufuna kudza kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.
41“Sindikufunafuna ulemu wa anthu ai. 42Koma ndikukudziŵani, mulibe chikondi cha Mulungu mumtima mwanu. 43Ine ndidadza m'dzina la Atate anga, ndipo inu simukundilandira. Koma wina atabwera m'dzina la iye yekha, iyeyo ndiye mungamlandire. 44Mukamapatsana ulemu nokhanokha mumasangalala, koma simufuna konse kulandira ulemu wochokera kwa amene Iye yekha ndiye Mulungu. Nanga mungakhulupirire bwanji? 45Musayese kuti ndine amene ndidzakunenezeni kwa Atate, ai. Wodzakunenezani alipo. Ndi Mose yemwe uja amene inu mumamdalira. 46Mukadakhulupirira Mose moona, bwenzi mutakhulupiriranso Ine, pakuti iye adaalemba za Ine. 47Koma ngati simukhulupirira zimene iyeyo adalemba, nanga mungakhulupirire bwanji mau anga?”
ಪ್ರಸ್ತುತ ಆಯ್ಕೆ ಮಾಡಲಾಗಿದೆ:
Yoh. 5: BLY-DC
Highlight
ಶೇರ್
ಕಾಪಿ
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi