Yoh. 13

13
Yesu atsuka mapazi a ophunzira ake
1Chikondwerero cha Paska chili pafupi, Yesu adaadziŵiratu kuti nthaŵi yake yafika yakuti achoke pansi pano kupita kwa Atate. Iye ankaŵakonda amene anali ake pansi pano, ndipo adaaŵakonda kotheratu.
2Tsono Yesu ndi ophunzira ake ankadya chakudya chamadzulo. Satana nkuti ataika kale mumtima mwa Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, maganizo akuti akapereke Yesu kwa adani ake. 3Yesu ankadziŵa kuti Atate adapereka zinthu zonse m'manja mwake. Ankadziŵanso kuti adachokera kwa Mulungu, ndipo kuti akubwerera kwa Mulungu. 4Choncho pamene analikudya, Yesu adaimirira, adavula mwinjiro wake, natenga nsalu yopukutira nkuimanga m'chiwuno. 5Atatero adathira madzi m'beseni, nayamba kutsuka mapazi a ophunzira ake, nkumaŵapukuta ndi nsalu yopukutira ija imene adaaimanga m'chiwuno.
6Pamene adafika pa Simoni Petro, iyeyo adati, “Ambuye, Inuyo nkundisambitsa ine mapazi?” 7Yesu adamuyankha kuti, “Zimene ndikuchitazi, sukuzidziŵa tsopano, koma udzazidziŵa m'tsogolo muno.” 8Petro adati, “Simudzandisambitsa konse mapazi.” Yesu adamuyankha kuti, “Ngati sindikusambitsa, ndiye kuti chako palibe.” 9Simoni Petro adati, “Ambuye, ngati ndi choncho, mutsuke osati mapazi anga okha, komanso manja anga ndi mutu womwe.” 10Yesu adamuuza kuti, “Munthu amene wasamba, wayera yense. Palibe chifukwa choti asambenso, koma kungosamba mapazi okha basi. Tsono inu mwayera, koma osati nonsenu ai.” 11Yesu ankamudziŵa munthu wodzampereka kwa adani ake, nchifukwa chake adaati, “Si nonsenu muli oyera.”
12 # Lk. 22.27 Yesu atatsuka mapazi a ophunzira ake, adavalanso mwinjiro wake nakakhalanso podyera paja. Kenaka adaŵafunsa kuti, “Kodi mwazimvetsa zimene ndakuchitiranizi? 13Paja inu mumanditchula kuti, ‘Aphunzitsi’ ndiponso, ‘Ambuye.’ Apo mumalondola, pakuti ndine amene. 14Tsono ngati Ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi. 15Ndakupatsani chitsanzo, kuti inunso muzichita monga momwe Ine ndakuchitirani inu. 16#Mt. 10.24; Lk. 6.40; Yoh. 15.20Kunena zoona, wantchito saposa mbuye wake, nthumwinso siiposa woituma. 17Ngati mudziŵa zimenezi, ndinu odala mukamazichita.
18 # Mas. 41.9 “Mauŵa sindikunenera nonsenu ai. Ndikuŵadziŵa amene ndaŵasankha. Koma ziyenera kuchitikadi zimene Malembo adanena kuti, ‘Amene ankadya nane pamodzi, yemweyo ndiye adandiwukira.’ 19Ndikukuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire kuti Ine ndinedi Ndilipo. 20#Mt. 10.40; Mk. 9.37; Lk. 9.48; 10.16Ndithu ndikunenetsa kuti wolandira aliyense amene ndamtuma, amalandira Ine. Ndipo wondilandira Ine, amalandira Iye amene adandituma.”
Yesu anenereratu zakuti adzaperekedwa
(Mt. 26.20-25; Mk. 14.17-21; Lk. 22.21-23)
21Yesu atanena zimenezi, adayamba kuvutika mu mtima ndipo adati, “Ndinene poyera pano: mmodzi mwa inu andipereka kwa adani anga.” 22Ophunzira aja adayamba kupenyetsetsana, osadziŵa konse kuti akunena yani. 23Wophunzira wina, yemwe Yesu ankamukonda kwambiri, adaakhala pambali pa Yesu. 24Tsono Simoni Petro adamkodola nati, “Taŵafunsa, kodi akunena yani?” 25Pamenepo iyeyo adatsamira pachifukwa pa Yesu, namufunsa kuti, “Ambuye, mukunena yani kodi?” 26Yesu adati, “Yemwe ndimusunsire nkumupatsa mkate umene ndimunyemere ndi ameneyo.” Tsono atasunsa mkate wonyemawo adaupatsa Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote.
27Yudasi atangolandira mkatewo, Satana adaloŵa mwa iye. Yesu adamuuza kuti, “Zimene ufuna kuchita, kachite mwamsanga.” 28Koma mwa amene ankadyawo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adaamvetsa zimene adaamuuzazo. 29Popeza kuti Yudasi ankasunga thumba la ndalama, anzake ankayesa kuti Yesu akumuuza kuti, “Kagule zofunika paphwando pano,” kapena kuti akapereke kanthu kwa osauka. 30Yudasi atalandira mkate uja, pompo adatuluka. Nthaŵiyo nkuti kutada kale.
Lamulo latsopano
31Yudasi atatuluka, Yesu adati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwa. 32Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iyeyu, Mulungu Mwini nayenso adzamlemekeza Iye, ndipo achita zimenezi tsopano apa. 33#Yoh. 7.34Ana anga, ndili nanube kanthaŵi pang'ono. Mudzandifunafuna, koma ndikukuuzani tsopano, monga ndidauziranso akulu a Ayuda kuti, ‘Kumene ndikupita Ine, inu simungathe kufikako.’ 34#Yoh. 15.12, 17; 1Yoh. 3.23; 2Yoh. 1.5Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. 35Mukamakondana, anthu onse adzadziŵa kuti ndinudi ophunzira anga.”
Yesu aneneratu kuti Petro adzamkana
(Mt. 26.20-25; Mk. 14.17-21; Lk. 22.21-23)
36Simoni Petro adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, mukupita kuti?” Yesu adati, “Kumene ndikupita, sungathe kunditsatira tsopano ai, koma udzanditsatira bwino lino.” 37Petro adamufunsa kuti, “Ambuye, chifukwa chiyani sindingathe kukutsatirani tsopano? Inetu nditha kutaya ngakhale moyo wanga chifukwa cha Inu.” 38Apo Yesu adati, “Iweyo kutaya moyo wako chifukwa cha Ine! Ndithu ndikunenetsa kuti tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.”

ಪ್ರಸ್ತುತ ಆಯ್ಕೆ ಮಾಡಲಾಗಿದೆ:

Yoh. 13: BLY-DC

Highlight

ಶೇರ್

ಕಾಪಿ

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in