Gen. 18

18
Lonjezo la kubadwa kwa Isaki
1Chauta adaonekera Abrahamu ku mitengo ya thundu ya ku Mamure ija. Abrahamuyo atakhala pa khomo la hema lake nthaŵi yamasana kutatentha, 2#Ahe. 13.2 mwadzidzidzi adangoona anthu atatu ataimirira potero. Atangoŵaona, adanyamuka mwamsanga kukaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu, 3nati, “Mbuyanga, ngati ndapeza kuyanja pamaso panu, chonde musapitirire pakhomo pa mtumiki wanu. 4Ndikupatseni madzi kuti mutsuke mapazi. Mungathe kubapuma patsinde pa mtengo pano. 5Ine tsopano ndikatenga chakudya, kuti mukadya mupeze mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Mwabwera pakhomo panga pano, motero ndiyenera kukutumikirani.” Anthuwo adayankha kuti, “Chabwino, uchite monga waneneramo.” 6Abrahamu adaloŵa msangamsanga m'hema, nauza Sara kuti “Utenge msanga nsengwa zitatu za ufa wosalala, uukande ndi kupanga buledi.” 7Pamenepo Abrahamu adathamanga nakatenga mwanawang'ombe wonenepa, nampereka kwa wantchito kuti akonze mwamsanga. 8Kenaka adatenga chambiko ndi mkaka wokama chatsopano, ndi nyama yokonzakonza ija naŵapatsa zonsezo. Iye adakhala potero pamene anthuwo analikudya patsinde pa mtengo.
9Tsono anthuwo adafunsa Abrahamu kuti, “Kodi mkazi wako Sara ali kuti?” Abrahamu adayankha kuti, “Ali m'hemamu.” 10#Aro. 9.9 Chauta adati, “Ndikukulonjeza kuti pakapita miyezi isanu ndi inai ndidzabweranso, ndipo mkazi wako adzakhala ali ndi mwana wamwamuna.” Sara ankangomvetsera ali kuseri kwa chitseko cha hema. 11Abrahamu pamodzi ndi Sara anali nkhalamba zokhazokha, ndipo nthaŵi imeneyo nkuti Sara ataleka kusamba monga amachitira akazi. 12#1Pet. 3.6 Motero Sara adangoseka, namati, “Ha, monga ndakalambira inemu, kodi nkuthekanso kuti ndikondwe ndi mwamuna wanga? Komanso mwamuna wanga ndi wokalamba zedi.” 13Chauta adafunsa Abrahamu kuti, “Chifukwa chiyani Sara amaseka ndi kunena kuti, ‘Ine monga ndakalambiramu kungatheke bwanji kukhala ndi mwana?’ 14#Lk. 1.37 Kodi chilipo china choti chingakanike Chauta? Tsono pa nthaŵi yake, ndidzachitadi zimene ndalonjezazi, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.” 15Apo Sara adakana chifukwa cha mantha, adati, “Sindidaseke.” Koma Iye adati, “Inde, unaseka.”
Abrahamu apempherera Sodomu
16Tsono anthuwo adachoka, nafika pamalo pamene anali kupenya Sodomu. Abrahamu adapita nawo limodzi, naŵalozera njira. 17Ndipo Chauta adanena mwa Iye yekha kuti, “Abrahamuyu sindingamubisire chomwe ndikuti ndichite. 18Zidzukulu zake zidzakhala mtundu waukulu wamphamvu. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadalitsidwa chifukwa cha iye. 19Ndamsankha iyeyu kuti alamule ana ake ndi mabanja ake akutsogolo kuti azidzamvera mau anga, pochita zabwino ndi zolungama. Choncho ndidzachita zonse zimene ndidamlonjeza.” 20Tsono Chauta adauza Abrahamu kuti, “Pali zolakwa zoopsa zokhudza Sodomu ndi Gomora, ndipo tchimo lao ndi lalikulu kwambiri. 21Choncho ndikuti nditsikireko kuti ndikaone ngati zolakwa zimene ndamvazo ndi zoona. Ngati si choncho, ndidzadziŵa.” 22Anthu aja adachoka, napita ku Sodomu, koma Abrahamu adatsarira ndi Chauta. 23Apo Abrahamu adayandikira kwa Chauta namufunsa kuti, “Kodi monga mudzaonongadi anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa? 24Nanga patakhala kuti pali anthu 50 osachimwa mumzindamo, kodi mudzaonongabe mzinda wonse? Kodi simudzauleka kuti musunge anthu 50 amenewo? 25Ndithu simudzaononga anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa. Chimenechi nchosatheka ndipo simungachite. Mukadatero bwenzi anthu osachimwa akulangidwira kumodzi ndi ochima. Kutalitali, Inu simungachite zotere! Kodi Muweruzi wa dziko lonse lapansi nkupanda chilungamo?” 26Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 50 osachimwa m'Sodomu, ndidzauleka mzinda wonsewo osauwononga, chifukwa cha anthu 50 amenewo.” 27Abrahamu adalankhulanso, adati, “Chonde, ndalimba mtima pakulankhula nanu chotere, Ambuye. Inetu ndine munthu chabe pamaso panu. 28Nanga pa chiŵerengero cha 50 pakangopereŵera anthu asanu okha, bwanji? Kodi mudzaononga mzindawo popeza kuti asoŵa asanu okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 45 olungama, sindidzaononga mzindawo.” 29Abrahamu adafunsanso kuti, “Nanga pakapezeka anthu olungama 40 okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 40, sindidzauwononga.” 30Apo Abrahamu adati, “Chonde ndapota nanu, musapse mtima, Ambuye, tsopano ndifunsanso. Nanga mutapezeka anthu olungama 30?” Chauta adati, “Ndikapeza anthu 30, sindidzauwononga.” 31Tsono Abrahamu adati, “Ndapota nanu, khululukireni kulimba mtima chotere polankhula ndi Inu Ambuye. Nanga mutapezeka olungama 20?” Chauta adati, “Ndikapeza anthu olungama 20, sindidzauwononga mzindawo.” 32Abrahamu adati, “Chonde, musandikwiyire Ambuye, koma ndilankhule kamodzi kokhaka. Nanga mutapezeka khumi okha?” Aponso Chauta adati, “Ndikapeza olungama khumi, sindidzauwononga mzindawo.” 33Chauta atatha kulankhula ndi Abrahamu, adachokapo, Abrahamuyo nkumabwerera kwao.

ಪ್ರಸ್ತುತ ಆಯ್ಕೆ ಮಾಡಲಾಗಿದೆ:

Gen. 18: BLY-DC

Highlight

ಶೇರ್

ಕಾಪಿ

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in