YOHANE 7
7
Abale a Yesu samvomereza
1 #
Yoh. 5.16, 18 Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda m'Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda m'Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye. 2#Lev. 23.34Koma chikondwerero cha Ayuda cha Misasa, linayandikira. 3Chifukwa chake abale ake anati kwa Iye, Chokani pano, mumuke ku Yudeya, kuti ophunzira anunso akapenye ntchito zanu zimene muchita. 4Pakuti palibe munthu achita kanthu mobisika, nafuna yekha kukhala poyera. Ngati muchita izi, dzionetsereni eni nokha kwa dziko lapansi. 5Pakuti angakhale abale ake sanakhulupirira Iye. 6#Yoh. 8.20Chifukwa chake Yesu ananena nao, Nthawi yanga siinafike; koma nthawi yanu yakonzeka masiku onse. 7#Yoh. 15.19Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa. 8#Yoh. 7.6Kwerani inu kunka kuphwando; sindikwera Ine kuphwando ili tsopano apa; pakuti nthawi yanga siinakwanire. 9Ndipo m'mene adanena nao zimenezi anakhalabe m'Galileya.
Yesu aphunzitsa m'Kachisi. Ayesa kumgwira
10Koma pamene abale ake adakwera kunka kuchikondwerero, pomwepo Iyenso anakwera, si poonekera, koma monga mobisalika. 11Pomwepo Ayuda analikumfuna Iye pachikondwerero, nanena, Ali kuti uja? 12#Yoh. 9.16Ndipo kunali kung'ung'udza kwambiri za Iye m'makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, Iai, koma asocheretsa khamu la anthuwo. 13Chinkana anatero panalibe munthu analankhula za Iye poyera, chifukwa cha kuopa Ayuda.
14Koma pamene padafika pakati pa chikondwerero, Yesu anakwera nalowa m'Kachisi, naphunzitsa. 15#Mat. 13.54Chifukwa chake Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira? 16#Yoh. 8.28Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine. 17Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha. 18Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama. 19#Eks. 24.3; Mat. 12.14Si Mose kodi anakupatsani inu chilamulo, ndipo kulibe mmodzi mwa inu achita chilamulo? Mufuna kundipha chifukwa ninji? 20#Yoh. 8.48, 52Khamu la anthu linayankha, Muli ndi chiwanda: afuna ndani kukuphani Inu? 21Yesu anayankha nati kwa iwo, Ndinachita ntchito imodzi, ndipo muzizwa monse. 22#Gen. 17.10; Lev. 12.3Chifukwa cha ichi Mose anakupatsani inu mdulidwe (si kuti uchokera kwa Mose, koma kwa makolo); ndipo mudula munthu tsiku la Sabata. 23#Yoh. 5.8-9, 16Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti chilamulo cha Mose chingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, chifukwa ndamchiritsadi munthu tsiku la Sabata? 24Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama.
25Pamenepo ena a iwo a ku Yerusalemu ananena, Kodi suyu amene afuna kumupha? 26Ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa Iye. Kapena kodi akulu adziwa ndithu kuti ndiye Khristu ameneyo? 27#Mat. 13.55Koma ameneyo tidziwa uko achokera: koma Khristu pamene akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko achokera. 28#Yoh. 5.43Pamenepo Yesu anafuula m'Kachisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndichokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma Iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona. 29#Mat. 11.27Ine ndimdziwa Iye; chifukwa ndili wochokera kwa Iye, nandituma Ine Iyeyu. 30#Mrk. 11.18Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike. 31#Yoh. 8.30Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo? 32Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za Iye; ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire Iye. 33#Yoh. 13.33Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndili ndi inu, ndipo ndimuka kwa Iye wondituma Ine. 34#Yoh. 13.33Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo. 35Chifukwa chake Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza Iye? Kodi adzamuka kwa Agriki obalalikawo, ndi kuphunzitsa Agriki? 36Mau awa amene ananena ndi chiyani, Mudzandifunafuna osandipeza Ine: ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo?
Yesu aneneratu za Mzimu Woyera
37 #
Lev. 23.36; Yes. 55.1; Chiv. 22.17 Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe. 38#Yoh. 4.14Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake. 39#Yes. 44.3; Yow. 2.28Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.
Anthu atsutsana za Iye
40 #
Deut. 18.15, 18 Pamenepo ena a khamulo pakumva mau awa, ananena, Mneneriyo ndi uyu ndithu. 41#Yoh. 4.42Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka m'Galileya? 42#Yes. 23.5; Mik. 5.2Kodi sichinati chilembo kuti Khristu adza kutuluka mwa mbeu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davide? 43#Yoh. 7.12Kudakhala tsono kusiyana m'khamulo chifukwa cha Iye. 44#Yoh. 7.30Koma ena mwa iwo anafuna kumgwira Iye; koma palibe munthu anamgwira kumanja.
45Pamenepo anyamatawo anadza kwa ansembe aakulu ndi Afarisi; ndipo iwowa anati kwa iwo, Simunamtenga Iye bwanji? 46#Mat. 7.29Anyamatawo anayankha, Nthawi yonse palibe munthu analankhula chotero. 47Pamenepo Afarisi anayankha iwo, Kodi mwasokeretsedwa inunso? 48#Yoh. 12.42Kodi wina wa akulu anakhulupirira Iye, kapena wa Afarisi? 49Koma khamu ili losadziwa chilamulo, likhala lotembereredwa. 50#Yoh. 3.1-2Nikodemo ananena kwa iwo, amene uja adadza kwa Iye kale, ali mmodzi wa iwo, 51Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene achita? 52Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli wotuluka m'Galileya? Santhula, nuone kuti m'Galileya sanauke mneneri. 53Ndipo anamuka munthu yense kunyumba yake.
ಪ್ರಸ್ತುತ ಆಯ್ಕೆ ಮಾಡಲಾಗಿದೆ:
YOHANE 7: BLPB2014
Highlight
ಶೇರ್
ಕಾಪಿ
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi