GENESIS Mau Oyamba
Mau Oyamba
Dzina lakuti Genesis litanthauza “chiyambi”. Bukuli likukamba za kulengedwa kwa dziko, chiyambi cha mtundu wa anthu, gwero la uchimo komanso mavuto m'dzikoli, komanso zimene Mulungu anachita pofuna kuwathandiza anthu. Buku la Genesis likhoza kugawidwa m'magawo awiri: Gawo loyamba ndilo kulengedwa kwa dziko ndi mbiri ya anthu oyamba. M'menemu timvamo za Adamu ndi Heva, Kaini ndi Abele, Nowa ndi nkhani ya chigumula komanso nsanja ya ku Babele (mutu 1—11). Gawo lachiwiri ndilo mbiri ya makolo oyamba a Aisraele. Oyambirira wa iwo ndiye Abrahamu, amene adziwika bwino chifukwa cha chikhulupiriro chake ndi kumvera kwake. Kenaka timva za mwana wake Isake, komanso mdzukulu wake Yakobo (amene adziwikanso ndi dzina loti Israele), ndiponso za ana 12 a Yakobo amene pa iwo mafuko 12 a Israele amangikapo. Pa nkhaniyi wolembayo akukhazikika kwambiri pa mmodzi mwa ana a Yakobo, dzina lake Yosefe. Akukamba za zonse zimene zinachitika kufikira pamene Yakobo ndi ana ake anapita kukakhala ku Ejipito pamodzi ndi mabanja ao (mutu 12—50).
Ngakhale bukuli likukamba za anthu, komabe mfundo yaikulu imene bukuli likunena ndi zomwe Mulungu anachita. Likuyamba ndi kutsimikiza kuti Mulungu ndi amene analenga dziko lapansi, ndipo likumaliza ndi lonjezo lakuti Mulungu adzapitirizabe kusamalira anthu ake. Mulungu ndiye mwininkhani m'buku lonseli, ndipo Iye ndi amene amaweruza ndi kulanga onse amene achita zoipa, amatsogolera ndi kuthandiza anthu ake, nawongolera zochitika zonse. Wolemba Bukuli amafuna kuti Aisraele azidzakumbukira za m'mene makolo ao ankakhulupirira Mulungu, ndi kuti nawonso moyo wao udzakhazikike pa chikhulupiriro chomwecho.
Za mkatimu
Kulengedwa kwa kumwamba ndi dziko lapansi komanso kwa munthu 1.1—2.25
Gwero la uchimo ndi masautso 3.1-24
Mibadwo kuchokera pa Adamu kufika pa Nowa 4.1—5.32
Mbiri ya Nowa ndi chigumula 6.1—10.32
Nsanja ya Babele 11.1-9
Mibadwo kuchokera pa Semu kufika pa Abramu 11.10-32
Mbiri ya makolo akale: Abrahamu, Isake ndi Yakobo 12.1—35.29
Mbumba ya Esau 36.1-43
Mbiri ya Yosefe ndi abale ake 37.1—45.28
Aisraele ku Ejipito 46.1—50.26
ಪ್ರಸ್ತುತ ಆಯ್ಕೆ ಮಾಡಲಾಗಿದೆ:
GENESIS Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
ಶೇರ್
ಕಾಪಿ
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi