Tsono Yesu adatenga buledi uja, ndipo atayamika Mulungu, adagaŵira anthu amene adaakhala pansiwo. Adateronso ndi tinsomba tija, naŵagaŵira monga momwe anthuwo ankafunira. Anthu onsewo atakhuta, Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Tolani zotsala kuti pasatayikepo kanthu.”