Yohane 4
4
Yesu Acheza ndi Mayi wa ku Samariya
1Yesu atazindikira kuti Afarisi amva zoti Iye ankapeza ndi kubatiza ophunzira ambiri kupambana Yohane, 2(ngakhale kuti Yesuyo sankabatiza, koma ophunzira ake). 3Iye anachoka ku Yudeya ndi kubwereranso ku Galileya.
4Ndipo Iye anayenera kudutsa mu Samariya. 5Iye anafika mʼmudzi wa Asamariya wotchedwa Sukari, pafupi ndi malo amene Yakobo anapatsa mwana wake Yosefe. 6Chitsime cha Yakobo chinali pamenepo ndipo Yesu atatopa ndi ulendo anakhala pansi pambali pa chitsimecho. Nthawi inali pafupifupi ora lachisanu ndi chimodzi masana.
7Mayi wa Chisamariya atabwera kudzatunga madzi, Yesu anati kwa iye, “Kodi ungandipatse madzi akumwa.” 8(Ophunzira ake nʼkuti atapita mʼmudzi kukagula chakudya).
9Mayiyo anati kwa Iye, “Inu ndinu Myuda ndipo ine ndine Msamariya. Bwanji mukundipempha madzi akumwa?” (Popeza Ayuda ndi Asamariya sankayanjana).
10Yesu anamuyankha kuti, “Koma iwe ukanadziwa mphatso ya Mulungu ndi Iye amene akukupempha madzi akumwa, ukanamupempha ndipo akanakupatsa madzi amoyo.”
11Mayiyo anati, “Ambuye, Inu mulibe kanthu kotungira madzi ndipo chitsime ndi chakuya. Kodi madzi amoyowo mungawatenge kuti? 12Kodi Inu ndinu wamkulu kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi ndipo iye ankamwanso monga anachita ana ake ndi ziweto zake?”
13Yesu anayankha kuti, “Aliyense amene amamwa madzi awa amamvanso ludzu, 14koma aliyense amene adzamwa madzi amene Ine ndidzamupatsa sadzamvanso ludzu. Ndithudi, madzi amene ndidzamupatsa adzakhala kasupe wamadzi wotumphukira ku moyo wosatha.”
15Mayiyo anati kwa Iye, “Ambuye, patseni madzi amenewo kuti ndisadzamvenso ludzu ndi kumabwerabe kuno kudzatunga madzi.”
16Iye anamuwuza kuti, “Pita kayitane mwamuna wako ndipo ubwere naye.”
17Iye anayankha kuti, “Ine ndilibe mwamuna.”
Yesu anati kwa iye, “Wakhoza ponena kuti ulibe mwamuna. 18Zoona nʼzakuti iwe wakhala pa banja ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene uli naye tsopano si wako. Zimene wanenazi ndi zoona.”
19Mayiyo anati, “Ambuye, ine ndazindikira kuti Inu ndinu mneneri. 20Makolo athu ankapembedza mʼphiri ili koma inu Ayuda mumati malo amene tiyenera kupembedzera ali ku Yerusalemu.”
21Yesu anati, “Mayi inu khulupirira Ine. Nthawi ikubwera pamene inu simudzapembedza Atate mʼphiri ili kapena mu Yerusalemu. 22Inu Asamariya mumapembedza chimene simukuchidziwa. Ife timapembedza chimene tikuchidziwa, pakuti chipulumutso nʼchochokera kwa Ayuda. 23Koma nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano pamene opembedza woona adzapembedza Atate mu mzimu ndi mʼchoonadi, pakuti opembedza otere ndiwo amene Atate akuwafuna. 24Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi.”
25Mayiyo anati, “Ine ndikudziwa kuti Mesiya (wotchedwa Khristu) akubwera. Akabwera, Iye adzafotokoza zonse kwa ife.”
26Ndipo Yesu anamuwuza kuti, “Amene ndikukuyankhulane, ndine amene.”
Ophunzira Abweranso kwa Yesu
27Pa nthawi yomweyo ophunzira ake anabwerera ndipo anadabwa kupeza Iye akuyankhula ndi mayi. Koma palibe amene anamufunsa kuti, “Kodi mukufuna chiyani?” kapena, “Nʼchifukwa chiyani mukuyankhula naye?”
28Kenaka mayiyo anasiya mtsuko wamadzi, nabwerera ku mzinda ndipo anati kwa anthu, 29“Tiyeni mukaone munthu amene wandiwuza ine zilizonse zimene ndinazichita. Kodi ameneyu sangakhale Khristu?” 30Iwo anatuluka mʼmudziwo ndi kupita kumene kunali Iye.
31Pa nthawi imeneyi ndi kuti ophunzira ake akumukakamiza kuti, “Rabi idyani.”
32Koma Iye anawawuza kuti, “Ine ndili ndi chakudya choti ndidye chimene inu simukuchidziwa.”
33Ndipo ophunzira ake anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi alipo wina amene anamubweretsera Iye chakudya?”
34Yesu anati, “Chakudya changa ndikuchita chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi kumaliza ntchito yake. 35Kodi inu simunena kuti, ‘Kwatsala miyezi inayi ndipo kenaka kukolola?’ Ine ndikukuwuzani kuti, tsekulani maso anu ndipo muyangʼane mʼminda! Mbewu zacha kale kuti zikololedwe. 36Ngakhale tsopano amene akukolola akulandira malipiro ake, ndipo akututa mbewu ku moyo wosatha kuti wofesa ndi wokolola asangalale pamodzi. 37Nʼchifukwa chake mawu akuti, ‘Wina amafesa ndipo wina amakolola’ ndi woona. 38Ine ndinakutumani kukakolola zimene simunagwirire ntchito. Ena anagwira ntchito yolemetsa ndipo inu mwatuta phindu la ntchito yawo.”
Asamariya Ambiri Akhulupirira
39Asamariya ambiri ochokera mʼmudziwo anakhulupirira Iye chifukwa cha umboni wa mayiyo wakuti, “Iye anandiwuza ine zonse ndinazichita.” 40Choncho Asamariya atabwera kwa Iye, anamuwumiriza Iye kuti akhale nawo, ndipo Iye anakhala nawo masiku awiri. 41Ndipo chifukwa cha mawu ake, ena ambiri anakhulupirira.
42Iwo anati kwa mayiyo, “Ife sitikukhulupirira chifukwa cha mawu ako okha, koma tsopano ife tadzimvera tokha, ndipo tikudziwa kuti munthu uyu ndithu ndi Mpulumutsi wa dziko lapansi.”
Yesu Achiritsa Mwana wa Nduna ya Mfumu
43Patatha masiku awiri Iye anachoka napita ku Galileya. 44(Tsopano Yesu mwini ananena kale kuti mneneri salandira ulemu mʼdziko lake). 45Iye atafika ku Galileya, Agalileya anamulandira. Iwo anali ataona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pa phwando la Paska, pakuti iwonso anali komweko.
46Iye anakafikanso ku Kana wa ku Galileya, kumene anasanduliza madzi kukhala vinyo. Ndipo kumeneko kunali nduna ina ya mfumu imene mwana wake wamwamuna anali chigonere akudwala ku Kaperenawo. 47Munthu uyu atamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, anapita kwa Iye, namupempha kuti apite akachiritse mwana wakeyo, amene anali pafupi kufa.
48Yesu anawawuza iwo kuti, “Anthu inu pokhapokha mutaona zizindikiro zodabwitsa, simudzakhulupirira.”
49Nduna ya mfumuyo inati, “Ambuye tiyeni mwana wanga asanafe.”
50Yesu anayankha kuti, “Pita. Mwana wako adzakhala ndi moyo.”
Munthuyo anakhulupirira mawu a Yesu ndipo ananyamuka. 51Iye ali pa njira, antchito ake anakumana naye, namuwuza kuti mwana wanu uja wachira. 52Iye atafunsa kuti ndi nthawi yanji imene mwana wake anapeza bwino, iwo anati kwa iye, “Malungo anamusiya iye dzulo pa ora lachisanu ndi chiwiri.”
53Ndipo bamboyo anazindikira kuti iyi inali nthawi yomweyo imene Yesu anati kwa iye, “Mwana wako adzakhala ndi moyo.” Choncho iye ndi onse a pa banja lake anakhulupirira.
54Ichi ndiye chinali chizindikiro chodabwitsa chachiwiri chimene Yesu anachita atafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya.
ទើបបានជ្រើសរើសហើយ៖
Yohane 4: CCL
គំនូសចំណាំ
ចែករំលែក
ចម្លង
ចង់ឱ្យគំនូសពណ៌ដែលបានរក្សាទុករបស់អ្នក មាននៅលើគ្រប់ឧបករណ៍ទាំងអស់មែនទេ? ចុះឈ្មោះប្រើ ឬចុះឈ្មោះចូល
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.