1
Yohane 6:35
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Kenaka Yesu ananenetsa kuti, “Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.
ប្រៀបធៀប
រុករក Yohane 6:35
2
Yohane 6:63
Mzimu Woyera apereka moyo, thupi silipindula kanthu. Mawu amene ndayankhula kwa inu ndiwo mzimu ndipo ndi moyo.
រុករក Yohane 6:63
3
Yohane 6:27
Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.”
រុករក Yohane 6:27
4
Yohane 6:40
Pakuti chifuniro cha Atate anga ndi chakuti aliyense amene aona Mwanayo namukhulupirira akhale ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.”
រុករក Yohane 6:40
5
Yohane 6:29
Yesu anayankha kuti, “Ntchito ya Mulungu ndi iyi: Kukhulupirira Iye amene anamutuma.”
រុករក Yohane 6:29
6
Yohane 6:37
Zonse zimene Atate andipatsa zidzabwera kwa Ine, ndipo aliyense amene adzabwera kwa Ine sindidzamutaya kunja.
រុករក Yohane 6:37
7
Yohane 6:68
Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, “Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha.
រុករក Yohane 6:68
8
Yohane 6:51
Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.”
រុករក Yohane 6:51
9
Yohane 6:44
Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene anandituma Ine samubweretsa. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.
រុករក Yohane 6:44
10
Yohane 6:33
Pakuti chakudya cha Mulungu ndi Iye amene wabwera kuchokera kumwamba ndi kupereka moyo ku dziko la pansi.”
រុករក Yohane 6:33
11
Yohane 6:48
Ine ndine chakudya chamoyo.
រុករក Yohane 6:48
12
Yohane 6:11-12
Kenaka Yesu anatenga bulediyo, atayamika anagawira iwo amene anakhala pansi, chimodzimodzinso nsombazo monga momwe iwo anafunira. Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, “Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu.”
រុករក Yohane 6:11-12
13
Yohane 6:19-20
Iwo atayenda makilomita asanu kapena asanu ndi limodzi, anaona Yesu akuyandikira bwatolo, akuyenda pa madzi; ndipo anachita mantha. Koma Iye anawawuza kuti, “Ndine, musaope.”
រុករក Yohane 6:19-20
ទំព័រដើម
ព្រះគម្ពីរ
គម្រោងអាន
វីដេអូ