1
Gen. 4:7
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Ukadachita zabwino, ndikadakondwera nawe. Koma chifukwa choti wachita zoipa, tchimo lakukhalirira pa khomo ngati chilombo cholusa. Likulakalaka kuti likugwire, koma iweyo uligonjetse tchimolo.”
Confronta
Esplora Gen. 4:7
2
Gen. 4:26
Seti adabereka mwana namutcha Enosi. Nthaŵi imeneyo anthu adayamba kutama dzina la Chauta mopemba.
Esplora Gen. 4:26
3
Gen. 4:9
Tsono Chauta adafunsa Kainiyo kuti, “Kodi mng'ono wako Abele ali kuti?” Iye adayankha kuti, “Sindikudziŵa. Kodi ndi ntchito yanga kusamala mng'ono wangayo?”
Esplora Gen. 4:9
4
Gen. 4:10
Chauta adamufunsanso kuti, “Kodi wachita chiyani? Magazi a mng'ono wako akulira kwa Ine kuchokera m'nthaka.
Esplora Gen. 4:10
5
Gen. 4:15
Koma Chauta adamuyankha kuti, “Iyai, aliyense wopha iwe Kaini adzalangidwa, ndipo Ineyo ndidzamulipsira kasanunkaŵiri.” Motero Chauta adaika chizindikiro pa Kaini kuchenjeza aliyense kuti asamuphe Kainiyo.
Esplora Gen. 4:15
Home
Bibbia
Piani
Video