1
Gen. 18:14
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Kodi chilipo china choti chingakanike Chauta? Tsono pa nthaŵi yake, ndidzachitadi zimene ndalonjezazi, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
Confronta
Esplora Gen. 18:14
2
Gen. 18:12
Motero Sara adangoseka, namati, “Ha, monga ndakalambira inemu, kodi nkuthekanso kuti ndikondwe ndi mwamuna wanga? Komanso mwamuna wanga ndi wokalamba zedi.”
Esplora Gen. 18:12
3
Gen. 18:18
Zidzukulu zake zidzakhala mtundu waukulu wamphamvu. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadalitsidwa chifukwa cha iye.
Esplora Gen. 18:18
4
Gen. 18:23-24
Apo Abrahamu adayandikira kwa Chauta namufunsa kuti, “Kodi monga mudzaonongadi anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa? Nanga patakhala kuti pali anthu 50 osachimwa mumzindamo, kodi mudzaonongabe mzinda wonse? Kodi simudzauleka kuti musunge anthu 50 amenewo?
Esplora Gen. 18:23-24
5
Gen. 18:26
Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 50 osachimwa m'Sodomu, ndidzauleka mzinda wonsewo osauwononga, chifukwa cha anthu 50 amenewo.”
Esplora Gen. 18:26
Home
Bibbia
Piani
Video