GENESIS 2

2
1Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lao lonse. 2#Eks. 20.11; Aheb. 4.4Tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri ku ntchito yake yonse. 3Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri, naliyeretsa limenelo: chifukwa limenelo adapuma ku ntchito yake yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga.
4Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba. 5Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; chifukwa Yehova Mulungu sanavumbitsire mvula padziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka; 6koma inakwera nkhungu yotuluka padziko lapansi, nkuthirira ponse pamwamba panthaka. 7#1Ako. 15.47Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.
Pokhala pake pamunthu
8 # Yes. 51.3 Ndipo Yehova Mulungu anabzala m'munda ku Edeni chakum'mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo. 9#Chiv. 2.7Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m'nthaka mitengo yonse yokoma m'maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pamundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa. 10Ndipo unatuluka mu Edeni mtsinje wakuthirira m'mundamo, m'menemo ndipo unalekana nuchita miyendo inai. 11Dzina la woyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golide; 12golide wa dziko ali wabwino; ndimonso muli bedola ndi mwala wasohamu. 13Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Kusi. 14Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigrisi: umenewo ndiwo wakuyenda cha kum'mawa kwake kwa Asiriya. Mtsinje wachinai ndi Yufurate. 15Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Edeni kuti aulime nauyang'anire. 16Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m'munda udyeko; 17#Gen. 3.1-3, 11, 17koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.
18Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye. 19Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazitcha; ndipo maina omwe onse anazitcha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao. 20Adamu ndipo anazitcha maina zinyama zonse, ndi mbalame za m'mlengalenga ndi zamoyo zonse za m'thengo: koma kwa Adamu sanapezeke womthangatira iye. 21Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikulu, ndipo anagona; ndipo anatengako nthiti yake imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pake. 22Ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu. 23Ndipo anati Adamu, Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzatchedwa Mkazi, chifukwa anamtenga mwa mwamuna. 24#Mat. 19.5; 1Ako. 6.16Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi. 25#Gen. 3.7Onse awiri ndipo anali amaliseche, mwamuna ndi mkazi wake, ndipo analibe manyazi.

Valið núna:

GENESIS 2: BLP-2018

Áherslumerki

Deildu

Afrita

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in