Gen. 12
12
Mulungu aitana Abramu
1 #
Lun. 10.5; Ntc. 7.2, 3; Ahe. 11.8 Tsiku lina Chauta adauza Abramu kuti, “Choka kudziko kwako kuno. Usiye abale ako ndi banja la bambo wako, ndipo upite ku dziko limene nditi ndikusonyeze. 2Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena.
3“#Aga. 3.8Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe,
koma ndidzatemberera aliyense wokutemberera.
Mitundu yonse ya pa dziko lapansi
idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.”
4Abramu anali wa zaka 75 pamene ankachoka ku Harani monga Chauta adaamlamulira, ndipo Loti adapita naye limodzi. 5Abramu adatenga mkazi wake Sarai, Loti mwana wa mng'ono wake, pamodzi ndi chuma chake chonse, ndi antchito amene adaali nawo ku Harani. Adayamba ulendo wonka ku Kanani. Atafika ku Kanani, 6Abramuyo adayendera dziko lonselo mpaka adakafika ku Sekemu, ku mtengo wa thundu wa ku More. Pa nthaŵi imeneyo nkuti Akanani akadalimo m'dzikomo. 7#Ntc. 7.5; Aga. 3.16 Chauta adaonekera Abramu namuuza kuti, “Dziko limeneli ndidzapatsa zidzukulu zako.” Choncho pa malo amenewo Abramu adamanga guwa, kumangira Chauta amene adaamuwonekera. 8Pambuyo pake adasendera ku mapiri a kuvuma kwa Betele, ndipo adamanga hema lake pakati pa Betele chakuzambwe ndi Ai chakuvuma. Kumenekonso adamangako guwa, ndipo adatama dzina la Chauta mopemba. 9Adapitirira ulendo wake pang'onopang'ono, kuloŵera ku Negebu, chigawo chakumwera.
Abramu ku Ejipito
10Koma m'dziko limenelo mudagwa njala. Ndipo chifukwa choti njala idaakula kwambiri, Abramu adapitirira ndithu chakumwera, mpaka kukafika ku Ejipito, nakhala kumeneko kanthaŵi. 11Pamene anali pafupi kuwoloka malire a Ejipito, adauza mkazi wake Sarai kuti, “Ndikudziŵa kuti iwetu ndiwe mkazi wokongola. 12Ndipo Aejipito akakupenya, aziti, ‘Ameneyu ndi mkazi wake,’ tsono kuti akukwatire iwe, andipha ineyo. 13#Gen. 20.2; 26.7 Chonde, uzikaŵauza kuti, ‘Ndi mlongo wanga.’ Motero zonse zidzandiyendera bwino chifukwa cha iwe, ndipo ndidzapulumuka.” 14Abramu ataoloka malire kuloŵa mu Ejipito, Aejipito adaonadi kuti mkazi wake ndi wokongola kwambiri. 15Akalonga a mfumu ya ku Ejipito atamuwona mkaziyo, adakauza Farao za kukongola kwake. Pomwepo anthu aja adamtenga mkaziyo kukamuika ku nyumba ya mfumu. 16Ndipo Farao adamchitira zabwino Abramu uja chifukwa cha mkaziyo, nampatsa nkhosa, mbuzi, ng'ombe, abulu, ngamira ndiponso akapolo aamuna ndi aakazi.
17Koma Chauta adagwetsa nthenda zoopsa pa Farao ndi pa anthu a m'nyumba mwake omwe, chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu. 18Apo Farao adaitana Abramu namufunsa kuti, “Kodi iwe, wandichita zotani? Bwanji osandiwuza kuti ameneyu ndi mkazi wako? 19Bwanji umanena kuti ndi mlongo wako kuti ine ndimukwatire? Nayu mkazi wako. Mtenge, ndipo uchoke!” 20Farao adalamula anthu ake, ndipo iwowo adatulutsa Abramu ndi mkazi wake m'dzikomo, pamodzi ndi zonse zimene anali nazo.
Jelenleg kiválasztva:
Gen. 12: BLY-DC
Kiemelés
Megosztás
Másolás
Szeretnéd, hogy a kiemeléseid minden eszközödön megjelenjenek? Regisztrálj vagy jelentkezz be
Bible Society of Malawi