GENESIS 15
15
Mulungu apangana ndi Abramu
1 #
Gen. 26.24; Mas. 3.3; 18.2; Dan. 10.12; Mrk. 6.50 Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu. 2Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine chiyani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliyezere wa ku Damasiko? 3Ndipo Abramu anati, Taonani, simunandipatse ine mbeu; ndipo, taonani, wobadwa m'nyumba mwanga adzalowa m'malo mwanga. 4Ndipo, taonani, mau a Yehova anadza kwa iye kuti, Uyu sadzakhala wakulowa m'malo mwako; koma iye amene adzatuluka m'chuuno mwako, ndiye adzakhala wakulowa m'malo mwako. 5#Eks. 32.13; Aheb. 11.12; Aro. 4.18Ndipo anamtulutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeu zako. 6#Aro. 4.3; Agal. 3.6Ndipo anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye chilungamo. 7Ndipo anati kwa iye, Ine ndine Yehova amene ndinatulutsa iwe m'Uri wa kwa Akaldeya, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lakolako. 8#Ower. 6.17Ndipo anati, Ambuye Mulungu, nanga ndidzadziwa bwanji kuti lidzakhala cholowa changa? 9Ndipo anati kwa iye, Kanditengere Ine ng'ombe yaikazi ya zaka zitatu, ndi mbuzi yaikazi ya zaka zitatu, ndi tonde wa zaka zitatu, ndi njiwa, ndi bunda. 10Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzake: koma mbalame sanazidule. 11Pamene miimba inatsikira panyama, Abramu anaingitsa iyo. 12Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye. 13#Eks. 12.40; Mac. 7.6Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, nizidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai; 14#Eks. 12.35-36ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri. 15Ndipo iwe udzanka kwa makolo ako m'mtendere; nudzaikidwa ndi ukalamba wabwino. 16Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe. 17Ndipo panali pamene litalowa dzuwa ndi kudza mdima, taonani, ng'anjo yofuka utsi ndi muuni wamoto wapita pakati pa mabanduwo. 18#Gen. 12.7Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pa mtsinje wa ku Ejipito kufikira pa mtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate: 19Akeni ndi Akenizi, Akadimoni, 20ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Arefaimu, 21ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Agirigasi, ndi Ayebusi.
Jelenleg kiválasztva:
GENESIS 15: BLPB2014
Kiemelés
Megosztás
Másolás
Szeretnéd, hogy a kiemeléseid minden eszközödön megjelenjenek? Regisztrálj vagy jelentkezz be
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi