GENESIS 12

12
Kuitanidwa kwa Abramu
1 # Aheb. 11.8 Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe; 2ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso; 3#Gen. 18.18; 22.18; Mac. 3.25; Agal. 3.28ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi. 4Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka m'Harani. 5Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala m'Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani. 6#Aheb. 11.9Ndipo Abramu anapitira m'dziko kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo. 7#Gen. 13.15; 15.18; 17.8; 24.7; 26.4; Deut. 34.4Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye. 8Ndipo iye anachoka kumeneko kunka kuphiri la kum'mawa kwa Betele, namanga hema wake; Betele anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova. 9Ndipo Abramu anayenda ulendo wake, nayendayenda kunka kumwera.
Abramu atsikira ku Ejipito
10 # Gen. 26.1; 43.1 Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramu ku Ejipito kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m'dziko m'menemo. 11Ndipo panali pamene anayandikira kulowa m'Ejipito, anati kwa Sarai mkazi wake, Taonani, ndidziwa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako; 12ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aejipito, adzati, Uyu ndi mkazi wake: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo. 13#Gen. 20.12; 26.7Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti chidzakhala chabwino ndi ine, chifukwa cha iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe. 14Ndipo panali pamene Abramu analowa m'Ejipito, Aejipito anaona kuti mkazi anali wokongola kwambiri.
15Ndipo akalonga ake a Farao anamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwake kwa Farao. 16Ndipo anamchitira Abramu bwino chifukwa cha iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu akazi, ndi ngamira. 17#1Mbi. 16.21; Mas. 105.14Koma Yehova anavutitsa Farao ndi banja lake ndi nthenda zazikulu chifukwa cha Sarai mkazi wake wa Abramu. 18Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nchiyani ichi wandichitira ine? Chifukwa chanji sunandiuza ine kuti ndiye mkazi wako? 19Chifukwa chanji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nuchoke. 20Ndipo Farao analamulira anthu ake za iye; ndipo anamperekeza iye m'njira ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo.

Jelenleg kiválasztva:

GENESIS 12: BLPB2014

Kiemelés

Megosztás

Másolás

None

Szeretnéd, hogy a kiemeléseid minden eszközödön megjelenjenek? Regisztrálj vagy jelentkezz be