GENESIS 10
10
Mbumba ya Nowa
1 #
1Mbi. 1.4
Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana amuna, chitapita chigumula chija. 2Ana amuna a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Meseki ndi Tirasi. 3Ndi ana amuna a Gomeri: Asikenazi, ndi Rifati, ndi Togarima. 4Ndi ana amuna a Yavani: Elisa, ndi Tarisisi, ndi Kitimu, ndi Dodanimu. 5Amenewo ndipo anagawa zisi za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.
6Ndi ana amuna a Hamu: Kusi, ndi Ejipito, ndi Puti, ndi Kanani. 7Ndi ana amuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedani. 8Ndipo Kusi anabala Nimirodi; ndipo iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko lapansi. 9Iye ndiye mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova: chifukwa chake kunanenedwa, Monga Nimirodi mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova. 10Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara. 11M'dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Asiriya, namanga Ninive, ndi mudzi wa Rehoboti, ndi Kala, 12ndi Reseni pakati pa Ninive ndi Kala: umenewo ndi mudzi waukulu. 13Ejipito ndipo anabala Ludimu, ndi Anamimu, ndi Lehabu, ndi Nafituhimu, 14ndi Patirusimu, ndi Kasiluhimu, m'menemo ndipo anatuluka Afilisti, ndi Kafitori.
15Ndipo Kanani anabala Sidoni woyamba wake, ndi Heti: 16ndi Ayebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi; 17ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini; 18ndi Aaravadi, ndi Aazemari, ndi Ahamati; pambuyo pake pamenepo ndipo mabanja a Akanani anafalikira. 19Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa. 20Amenewa ndi ana amuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.
21Ndiponso kwa Semu atate wa ana onse a Eberi, mkulu wa Yafeti, kwa iye kunabadwa ana. 22Ana amuna a Semu; Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu. 23Ndi ana a Aramu: Uzi ndi Huli ndi Getere, ndi Masi. 24Aripakisadi ndipo anabala Sela; ndipo Sela anabala Eberi. 25Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana amuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani. 26Ndipo Yokotani anabala Alimodadi, ndi Selefi, ndi Hazara-Maveti, ndi Yera; 27ndi Hadoramu ndi Uzali, ndi Dikila; 28ndi Obala, ndi Abimaele, ndi Sheba; 29ndi Ofiri ndi Havila, ndi Yobabu; onse amenewa ndi ana a Yokotani. 30Kwao kunayamba pa Mesa pakunka ku Sefari phiri la kum'mawa. 31Amenewa ndi ana a Semu, monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.
32Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu pa dziko lapansi, chitapita chigumula.
Jelenleg kiválasztva:
GENESIS 10: BLPB2014
Kiemelés
Megosztás
Másolás
Szeretnéd, hogy a kiemeléseid minden eszközödön megjelenjenek? Regisztrálj vagy jelentkezz be
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi