Yoh. 6

6
Yesu adyetsa anthu oposa zikwi zisanu
(Mt. 14.13-21; Mk. 6.30-44; Lk. 9.10-17)
1Pambuyo pake Yesu adaoloka nyanja ya Galileya (dzina lake lina ndi nyanja ya Tiberiasi.) 2Khamu lalikulu la anthu lidamtsatira, chifukwa lidaaona zizindikiro zozizwitsa zimene adaachita pakuchiritsa anthu odwala. 3Yesu adakwera m'phiri nakhala pansi ndi ophunzira ake. 4Chikondwerero chija chachipembedzo chotchedwa Paska chidaayandikira. 5Pamene Yesu adayang'ana, adaona khamu lalikulu la anthu lija likudza kwa Iye. Tsono Iye adafunsa Filipo kuti, “Kodi tingakagule kuti chakudya chodyetsa anthu onseŵa?” 6(Adaafunsa zimenezi dala kuti amuyese Filipoyo, koma mwiniwakeyo adaadziŵiratu choti achite.) 7Filipo adayankha kuti, “Ngakhale ndalama mazana aŵiri sizingakwanire konse kugula chakudya choti aliyense mwa anthuŵa adyeko ngakhale pang'ono.”
8Wophunzira wake wina, dzina lake Andrea, mbale wake wa Simoni Petro, adauza Yesu kuti, 9“Pali mnyamata pano, ali ndi buledi msanu wabarele, ndi tinsomba tiŵiri. Koma zimenezi zingachitenji kwa anthu onseŵa?” 10Yesu adati, “Auzeni anthu akhale pansi.” (Pamenepo panali msipu wambiri.) Anthuwo adakhaladi pansi. Amuna okha analipo ngati zikwi zisanu. 11Tsono Yesu adatenga buledi uja, ndipo atayamika Mulungu, adagaŵira anthu amene adaakhala pansiwo. Adateronso ndi tinsomba tija, naŵagaŵira monga momwe anthuwo ankafunira. 12Anthu onsewo atakhuta, Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Tolani zotsala kuti pasatayikepo kanthu.” 13Adatoladi zotsala zonse za buledi msanu uja, nadzaza madengu khumi ndi aŵiri.
14Pamene anthu aja adaona chizindikiro chozizwitsa chimene Yesu adachitacho, adati, “Zoonadi ameneyu ndi Mneneri uja amene ankanena kuti adzabwera pansi panoyu.”
15Yesu adaadziŵa kuti anthuwo ankati adzamgwire ndi kumlonga ufumu. Motero adaŵachokera nakakweranso m'phiri payekha.
Yesu ayenda pa madzi
(Mt. 14.22-27; Mk. 6.45-52)
16M'mene kunkayamba kuda, ophunzira ake a Yesu adatsikira ku nyanja. 17Kumeneko adaloŵa m'chombo, nayamba kuwoloka nyanja kupita ku Kapernao. Mdima udagwa, Yesu osafikabe kwa iwo. 18Komanso nyanja idaavwanduka, chifukwa mphepo inkaomba kwambiri. 19Atapalasa chombo ulendo wokwanira mitunda itatu kapena inai, adaona Yesu akuyenda pa madzi nkumayandikira ku chombo chao, motero iwowo adachita mantha. 20Koma Yesu adati, “Ndine, musaope.” 21Adamkweza Yesu m'chombomo mokondwa, ndipo nthaŵi yomweyo chombocho chidakocheza kumtunda kumene adaalingako.
Anthu afunafuna Yesu
22M'maŵa mwake khamu la anthu limene lidaatsalira ku tsidya lija la nyanja, lidaadziŵa kuti chombo chinalipo chimodzi chokha. Anthuwo adaadziŵanso kuti Yesu sadaloŵe m'chombomo pamodzi ndi ophunzira ake, koma kuti ophunzira akewo anali atapita okha. 23Komabe zombo zina zochokera ku Tiberiasi zidafika pafupi ndi malo amene anthu aja adaadyera chakudya Ambuye atayamika Mulungu. 24Khamu lija lidaona kuti Yesu kulibe, ophunzira ake omwe kulibenso. Tsono anthu onsewo adaloŵa m'zombo zija, napita ku Kapernao kunka nafunafuna Yesu.
Yesu ndiye chakudya chopatsa moyo
25Pamene anthu aja adampeza Yesu kutsidya kwa nyanja, adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, mudafika liti kuno?” 26Yesu adati, “Kunena zoona, inu mukundifuna osati chifukwa mudazimvetsa zizindikiro zozizwitsa zija ai, koma chifukwa mudadya chakudya chija mpaka kukhuta. 27#Mphu. 24.19-22Musamagwira ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimaonongeka, koma muzigwira ntchito kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chili cha moyo wosatha. Mwana wa Munthu ndiye adzakupatsani chakudya chimenechi, pakuti Mulungu Atate adamuvomereza motsimikiza.”
28Pamenepo anthu aja adayamba kufunsana kuti, “Titanitu tsono kuti titsate bwino zimene Mulungu afuna?” 29Yesu adaŵayankha kuti, “Chimene Mulungu afuna kuti muchite nchakuti mundikhulupirire Ineyo amene Mulungu adandituma.”
30Iwo adafunsanso kuti, “Mungatiwonetse chizindikiro chotani kuti tikachiwona tikukhulupirireni? Nanga muchitapo chiyani? 31#Eks. 16.4, 15; Mas. 78.24; Lun. 16.20, 21 Makolo athu ankadya mana m'chipululu muja, monga Malembo akunenera kuti, ‘Ankaŵapatsa chakudya chochokera Kumwamba kuti adye.’ ” 32Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti amene ankakupatsani chakudya chochokera Kumwambacho, si Mose ai. Atate anga ndiwo amene amakupatsani chakudya chenicheni chochokera Kumwamba. 33Pakuti chakudya chimene Mulungu amapereka, ndicho chimene chimatsika kuchokera Kumwamba, ndipo chimapereka moyo kwa anthu a pa dziko lonse lapansi.”
34Apo anthuwo adapempha Yesu kuti, “Ambuye, muzitipatsa chakudya chimenecho masiku onse.” 35Yesu adaŵauza kuti, “Chakudya chopatsa moyocho ndine. Munthu aliyense wodza kwa Ine, sadzamva njala. Ndipo aliyense wokhulupirira Ine, sadzamva ludzu konse.
36“Ndidakuuzani kuti inde inu mwandiwona, komabe simukhulupirira. 37Onse amene Atate andipatsa, adzabwera kwa Ine. Ndipo munthu aliyense wodza kwa Ine, sindidzamkana konse. 38Pajatu ndidatsika kuchokera Kumwamba kudzachita zofuna za Iye amene adandituma, osati kuti ndidzachite zofuna Ine ai. 39Ndipo chofuna Iye amene adandituma nchakuti ndisatayepo ndi mmodzi yemwe mwa amene Iye adandipatsa, koma onse ndidzaŵaukitse kwa akufa pa tsiku lomaliza. 40Pakuti chimene Atate anga afuna nchakuti munthu aliyense amene aona Mwanayo namkhulupirira, akhale ndi moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.”
41Pamenepo Ayudawo adayamba kung'ung'udza chifukwa Yesu adaati, “Ine ndine chakudya chotsika kuchokera Kumwamba.” 42Iwo ankanena kuti, “Kodi ameneyu si Yesu, mwana wa Yosefe uja? Bambo wake ndi mai wake suja tikuŵadziŵa? Nanga tsono anganene bwanji kuti, ‘Ndidatsika kuchokera Kumwamba?’ ” 43Yesu adaŵayankha kuti, “Musang'ung'udze inu. 44Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene adandituma samkoka. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. 45#Yes. 54.13 Paja aneneri adalemba kuti, ‘Onse adzakhala ophunzitsidwa ndi Mulungu.’ Munthu aliyense womva Atate, nkuphunzira kwa Iwo, amadza kwa Ine. 46Sindiye kutitu wina aliyense adaona Atate ai, koma Ine ndekha amene ndidachokera kwa Mulungu; Ineyo ndi amene ndidaona Atate.
47“Ndithu ndikunenetsa kuti wokhulupirira Ine, ali nawo moyo wosatha. 48Ine ndine chakudya chopatsa moyo. 49Makolo anu ankadya mana m'chipululu muja, komabe adafa. 50Koma chakudya chimene ndikunenachi ndi chimene chidatsika kuchokera Kumwamba, kuti munthu atachidya asafe. 51Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo chakudyacho chimene Ine ndidzapereka ndi thupi langa, limene ndikulipereka kuti anthu a pa dziko lonse lapansi akhale ndi moyo.”
52Pamenepo Ayuda aja adayamba kukangana okhaokha, ankati, “Munthu ameneyu angathe bwanji kutipatsa thupi lake kuti tidye?” 53Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati simudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. 54Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga, ali ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. 55Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni, ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. 56Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa iyeyo. 57Monga Atate amoyo adandituma, ndipo Ine ndili ndi moyo pokhala mwa Iwo, momwemonso aliyense wodya Ine, adzakhala ndi moyo pokhala mwa Ine. 58Chakudya chimene chidatsika kuchokera Kumwamba nchimenechi. Nchosiyana ndi mana aja amene makolo anu ankadya koma nkufabe. Wodya chakudya chimenechi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya.”
59Yesu adanena zimenezi pamene ankaphunzitsa m'nyumba yamapemphero ya ku Kapernao.
Mau opatsa moyo wosatha
60Ophunzira ambiri a Yesu atamva zimenezi adati, “Mau ameneŵa ngapatali. Angathe kuŵavomera ndani?” 61Yesu adaadziŵa mumtima mwake kuti ophunzira ake akung'ung'udza za zimenezi. Tsono adaŵafunsa kuti, “Kodi zimenezi mukukhumudwa nazo? 62Nanga mudzatani mukadzaona Mwana wa Munthu akukwera kunka kumene anali kale? 63#Lun. 9.13-18Mzimu wa Mulungu ndiwo umapatsa moyo, mphamvu ya munthu siipindula konse. Mau amene ndalankhula nanu ndiwo amapatsa mzimu wa Mulungu ndiponso moyo. 64Koma pali ena mwa inu amene sakukhulupirira.” (Pakuti Yesu adaadziŵiratu mpachiyambi pomwe amene sadzakhulupirira, adaamudziŵiratunso amene analikudzampereka kwa adani ake.) 65Tsono adati, “Nchifukwa chake ndinakuuzani kuti palibe munthu amene angabwere kwa Ine ngati Atate sampatsa mphamvu zobwerera kwa Ine.”
66Kuchokera pamenepo ophunzira ambiri a Yesu adamsiya, osayenda nayenso. 67Tsono Yesu adafunsa ophunzira khumi ndi aŵiri aja kuti, “Nanga inu, kodi inunso mukufuna kuchoka?” 68#Mt. 16.16; Mk. 8.29; Lk. 9.20Simoni Petro adati “Ambuye, nanga tingapitenso kwa yani? Muli nawo ndinu mau opatsa moyo wosatha. 69Ife ndiye tikukhulupirira ndipo tikudziŵa kuti ndinu Woyera uja wochokera kwa Mulungu.” 70Apo Yesu adati, “Paja ndidakusankhani inu khumi ndi aŵiri, si choncho? Komabe mmodzi mwa inu ndi Satana?” 71Ankanena Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote. Ngakhale anali mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi aŵiri, koma ndiye amene analikudzapereka Yesu kwa adani ake.

Chwazi Kounye ya:

Yoh. 6: BLY-DC

Pati Souliye

Pataje

Kopye

None

Ou vle gen souliye ou yo sere sou tout aparèy ou yo? Enskri oswa konekte