YOHANE 6

6
Yesu achulukitsa mikate
(Mat. 14.13-21; Mrk. 6.30-44; Luk. 9.10-17)
1 # Mat. 14.15 Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi. 2Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala. 3Koma Yesu anakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndi ophunzira ake. 4#Lev. 23.5, 7Ndipo Paska, chikondwerero cha Ayuda, anayandikira. 5#Mat. 14.14Pamenepo Yesu, pokweza maso ake, ndi kuona kuti khamu lalikulu lilinkudza kwa Iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa? 6Koma ananena ichi kuti amuyese; pakuti anadziwa yekha chimene adzachita. 7#Num. 11.21-22Filipo anayankha Iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang'ono. 8Mmodzi wa ophunzira ake, Andrea, mbale wake wa Simoni Petro, ananena ndi Iye, 9#2Maf. 4.43Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zifikira bwanji ambiri otere? 10Nati Yesu, Akhalitseni anthu pansi. Ndipo panali udzu wambiri pamalopo. Pamenepo amunawo anakhala pansi, kuwerenga kwao monga zikwi zisanu. 11Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna. 12Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu. 13Pomwepo anasonkhanitsa, nadzaza madengu khumi ndi awiri ndi makombo a mikate isanuyo yabarele, amene anatsalira anadyawo. 14#Deut. 18.15, 18Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.
15Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira Iye, kuti amlonge ufumu, anachokanso kunka kuphiri pa yekha.
Yesu ayenda panyanja
(Mat. 14.22-34; Mrk. 6.45-46)
16 # Mat. 14.23 Koma pofika madzulo, ophunzira ake anatsikira kunyanja; 17ndipo pamene adalowa m'ngalawa, analikuoloka nyanja kunka ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu asanadze kwa iwo. 18Ndipo nyanja inalikuuka chifukwa cha mphepo yaikulu yakuombako. 19Ndipo pamene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anachita mantha. 20Koma Iye ananena nao, Ndine; musaope. 21Pamenepo analola kumlandira m'ngalawa; ndipo pomwepo ngalawayo inafika kumtunda kumene analikunkako.
Yesu mkate wamoyo wa okhulupirira
22M'mawa mwake khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa ina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowe pamodzi ndi ophunzira ake m'ngalawamo, koma ophunzira ake adachoka pa okha; 23koma zinachokera ngalawa zina ku Tiberiasi, pafupi pa malo pomwe adadyapo mkate m'mene Ambuye Yesu adayamika; 24chifukwa chake pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi ophunzira ake palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu. 25Ndipo pamene anampeza Iye tsidya lina la nyanja, anati kwa Iye, Rabi, munadza kuno liti? 26Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta. 27#Mat. 3.17; Yoh. 6.54Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro. 28Pamenepo anati kwa Iye, Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu? 29#1Yoh. 3.23Yesu anayankha nati kwa iwo, Ntchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iye amene Iyeyo anamtuma. 30#Mat. 12.38Chifukwa chake anati kwa Iye, Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? Muchita chiyani? 31#Eks. 16.15; Mas. 78.24-25Atate athu anadya mana m'chipululu; monga kwalembedwa, Mkate wochokera m'mwamba anawapatsa iwo kudya. 32#Eks. 16.15; Mas. 78.24-25Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba. 33Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi. 34Pamenepo anati kwa Iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umene nthawi zonse. 35#Yoh. 4.14; 6.48, 58; 7.37Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse. 36Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira. 37#Yoh. 6.45; 10.28-29; 2Tim. 2.19; 1Yoh. 2.19Chinthu chonse chimene anandipatsa Ine Atate chidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja. 38#Mat. 26.39; Yoh. 5.30Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine. 39#Yoh. 10.28; 17.12Koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi ichi, kuti za ichi chonse Iye anandipatsa Ine ndisatayeko kanthu, koma ndichiukitse tsiku lomaliza. 40#Yoh. 3.15-16; 6.27, 47, 54Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.
41 # 6.33, 50 Chifukwa chake Ayuda anang'ung'udza za Iye, chifukwa anati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba. 42#Mat. 13.55Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wake ndi amai wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba? 43Yesu anayankha nati kwa iwo, Musang'ung'udze wina ndi mnzake. 44#Yoh. 6.65Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza. 45#Yes. 54.13; Yoh. 6.37Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine. 46#Mat. 11.27; Yoh. 5.37; 1.18Sikuti munthu wina waona Atate, koma Iye amene ali wochokera kwa Mulungu, ameneyo waona Atate. 47#Yoh. 3.15-16, 36Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wokhulupirira ali nao moyo wosatha. 48#Yoh. 6.35Ine ndine mkate wamoyo. 49#Yoh. 6.31Makolo anu adadya m'chipululu, ndipo adamwalira. 50#Yoh. 6.33Mkate wotsika Kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira. 51#Yoh. 6.33; Aheb. 10.5, 10Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.
52Pamenepo Ayuda anatetana wina ndi mnzake ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake? 53#Mat. 26.26, 28Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha. 54#Yoh. 6.27, 63Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza. 55Pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu. 56#1Yoh. 3.24Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye. 57Monga Atate wamoyo anandituma Ine, ndipo Inenso ndili ndi moyo chifukwa cha Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine. 58#Yoh. 6.49-51Mkate wotsika Kumwamba ndi umenewu: si monga makolowo, anadya namwalira; iye wakudya mkate umene adzakhala ndi moyo nthawi zonse. 59Izi ananena m'sunagoge, pakuphunzitsa m'Kapernao.
Ophunzira ambiri aleka kutsata Yesu
60 # Yoh. 6.66 Pamenepo ambiri a ophunzira ake, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani? 61Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti ophunzira ake alikung'ung'udza chifukwa cha ichi, anati kwa iwo, Ichi mukhumudwa nacho? 62#Mrk. 16.19; Yoh. 3.13; Mac. 1.9Nanga bwanji ngati mukaona Mwana wa Munthu alikukwera kumene anali kale lomwe? 63#2Ako. 3.6Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo. 64#Yoh. 6.66, 71Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira. Pakuti Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupirira, ndi amene adzampereka. 65#Yoh. 6.44-45Ndipo ananena, Chifukwa cha ichi ndinati kwa inu, kuti palibe munthu angathe kudza kwa Ine, koma ngati kupatsidwa kwa iye ndi Atate.
Chivomerezo cha Petro
(Mat. 16.13-20; Mrk. 8.27-30; Luk. 9.18-21)
66 # Yoh. 6.60 Pa ichi ambiri a ophunzira ake anabwerera m'mbuyo, ndipo sanayendeyendenso ndi Iye. 67Chifukwa chake Yesu anati kwa khumi ndi awiriwo, Nanga inunso mufuna kuchoka? 68Simoni Petro anamyankha Iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nao mau a moyo wosatha. 69#Mat. 16.16Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu. 70#Luk. 6.13; Yoh. 13.27Yesu anayankha iwo, Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu mmodzi ali mdierekezi? 71Koma adanena za Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, pakuti iye ndiye amene akampereka Iye, ali mmodzi wa khumi ndi awiri.

वर्तमान में चयनित:

YOHANE 6: BLPB2014

हाइलाइट

शेयर

कॉपी

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in