1
Lk. 16:10
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ngwokhulupirikanso pa zazikulu. Ndipo wonyenga pa zazing'ono, amanyenganso pa zazikulu.
Compare
Lk. 16:10 ખોજ કરો
2
Lk. 16:13
“Palibe wantchito amene angathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkunyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.”
Lk. 16:13 ખોજ કરો
3
Lk. 16:11-12
Tsono ngati mwakhala osakhulupirika pa chuma chonyengachi, ndani nanga adzakusungizeni chuma chenicheni? Ndipo ngati mwakhala osakhulupirika ndi za wina, ndani adzakupatseni zimene zili zanuzanu?
Lk. 16:11-12 ખોજ કરો
4
Lk. 16:31
Koma Abrahamu adamuuza kuti, ‘Ngatitu iwo samvera Mose ndi aneneri, sangathekenso ngakhale wina auke kwa akufa.’ ”
Lk. 16:31 ખોજ કરો
5
Lk. 16:18
“Aliyense amene asudzula mkazi wake, nakwatira wina, akuchita chigololo. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo.”
Lk. 16:18 ખોજ કરો
હોમ
બાઇબલ
યોજનાઓ
વિડિઓઝ