1
Lk. 23:34
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Yesu adati, “Atate, muŵakhululukire anthuŵa, chifukwa sakudziŵa zimene akuchita.” Iwo aja adagaŵana zovala zake pakuchita maere.
Comparer
Explorer Lk. 23:34
2
Lk. 23:43
Yesu adamuyankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, Kumwamba.”
Explorer Lk. 23:43
3
Lk. 23:42
Ndipo adati, “Inu, mukandikumbikire mukakafika mu Ufumu wanu.”
Explorer Lk. 23:42
4
Lk. 23:46
Tsono Yesu adanena mokweza mau kuti, “Atate ndikupereka mzimu wanga m'manja mwanu.” Atanena zimenezi, adatsirizika.
Explorer Lk. 23:46
5
Lk. 23:33
Pamene adafika ku malo otchedwa Chibade cha Mutu, adapachika Yesu komweko pa mtanda. Komwekonso adapachika zigaŵenga zija, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere.
Explorer Lk. 23:33
6
Lk. 23:44-45
Nthaŵi itakwana ngati 12 koloko masana, padaagwa mdima pa dziko lonse mpaka pa 3 koloko, dzuŵa litangoti bii kuda. Pamenepo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati.
Explorer Lk. 23:44-45
7
Lk. 23:47
Mkulu wa asilikali ataona zimene zidaachitikazo, adatamanda Mulungu, adati, “Ndithudi munthuyu adaalidi wosalakwa konse.”
Explorer Lk. 23:47
Accueil
Bible
Plans
Vidéos