1
Lk. 19:10
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Pajatu Mwana wa Munthu adabwera kudzafunafuna ndi kudzapulumutsa amene adatayika.”
Comparer
Explorer Lk. 19:10
2
Lk. 19:38
Adati, “Ndi yodala Mfumu imene ilikudza m'dzina la Ambuye. Mtendere Kumwamba, ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.”
Explorer Lk. 19:38
3
Lk. 19:9
Apo Yesu adamuuza kuti, “Chipulumutso chafika m'banja lino lero, popeza kuti ameneyunso ndi mwana wa Abrahamu.
Explorer Lk. 19:9
4
Lk. 19:5-6
Ndiye pamene Yesu adafika pamalopo, adayang'ana m'mwamba, namuuza kuti, “Zakeyo, fulumira, tsika, chifukwa lero ndikuyenera kukakhala nao kunyumba kwako.” Pompo Zakeyo adafulumira, natsika, kenaka nkukamlandiradi Yesu mokondwa kwambiri.
Explorer Lk. 19:5-6
5
Lk. 19:8
Koma Zakeyo adaimirira nauza Ambuye kuti, “Ambuye, ndithudi ndidzapereka hafu la chuma changa kwa amphaŵi. Ndipo ngati ndidalandira kanthu kwa munthu aliyense monyenga, ndidzamubwezera kanai.”
Explorer Lk. 19:8
6
Lk. 19:39-40
Apo Afarisi ena amene adaali m'khamumo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, auzeni ophunzira anuŵa aleke zimenezi.” Iye adati, “Ndikutitu iwoŵa akangokhala chete, ifuula ndi miyalayi.”
Explorer Lk. 19:39-40
Accueil
Bible
Plans
Vidéos