Mal. 2
2
Chauta akonda Aisraele
1Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsono ansembe inu, lamulo ili nlokhalira inu. 2Mukapanda kundimvera, mukapanda kulemekeza dzina langa, ndidzakutembererani. Zabwino zimene mumazilandira nazonso ndidzazitemberera. Ndithu, ndazitemberera kale chifukwa simudamvere ndi mtima wonse.
3“Ndidzalanga zidzukulu zanu. Ndidzakupakani ndoŵe za nsembe zanu kumaso, ndipo ndidzakutayani ku nkhuti ya ndoŵe. 4#Num. 3.11-13 Apo mudzadziŵa kuti ndakupatsani lamulo ili kuti chipangano changa ndi ansembe, zidzukulu za Levi, chisaphwanyike. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. 5#Num. 25.12 Ndidapangana nawo chipangano chopatsa moyo ndi mtendere. Ndidaŵapatsa zimenezi kuti azindiwopa, ndipo adandiwopadi namalemekeza dzina langa. 6Malangizo amene ankapereka anali oona, pakamwa pao sipankatuluka zosalungama. Ankamvana nane, ndipo ankayenda mokhulupirika ndi Ine, motero ankabweza anthu ambiri m'njira zao zoipa.
7“Pajatu ndi ntchito ya ansembe kuphunzitsa nzeru zoona za Mulungu, anthu ayenera kupita kwa iwo kuti akaphunzire zimene Ine ndifuna, chifukwa ansembewo ndiwo amithenga a Chauta Wamphamvuzonse. 8Koma inu ansembe mudasiya njira yanga. Mudaphunthwitsa anthu ambiri ndi zophunzitsa zanu. Mudaipitsa chipangano changa ndi Alevi. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. 9Nchifukwa chake Inenso ndakusandutsani onyozeka ndi achabechabe pamaso pa anthu, popeza kuti simudatsate njira zanga, ndipo mwakhala mukukondera poweruza milandu.”
Kusakhulupirika kwa anthu
10Kodi tonsefe suja tili ndi bambo mmodzi? Kodi suja adatilenga ndi Mulungu mmodzi? Chifukwa chiyani tsono tikuphwanya chipangano cha Mulungu ndi makolo athu posamakhulupirirana? 11Anthu a ku Yuda akhala osakhulupirika, ku Israele ndi ku Yerusalemu akhala akuchita zinthu zonyansa. Anthu a ku Yuda aipitsa Nyumba ya Chauta imene Iye amaikonda. Akhala akukwatira akazi opembedza milungu yachikunja. 12Wina aliyense wochita zimenezi Chauta amchotse ku banja la Yakobe. Asakhale nawonso ndi anthu opereka nsembe kwa Chauta Wopambanazonse.
13Zina zimene mumachita ndi izi: mumadandaula ndi kulira kwambiri mpaka kukhathamiza guwa la Chauta ndi misozi, chifukwa Iye amakana kuyang'ana nsembe zanu, osafuna kulandira mphatso iliyonse yodzatula inu. 14Mumafunsa kuti, “Chifukwa chake nchiyani?” Chifukwa chake nchakuti Chauta anali mboni ya chipangano chimene udachita ndi mkazi wako woyamba. Sudakhulupirike kwa iye, ngakhale iyeyo ndiye mnzako ndi mkazi wako potsata chipanganocho. 15Kodi suja Mulungu adakulenga, iwe ndi mkazi wako, kukhala mmodzi, thupi ndi mzimu womwe? Nanga pakutero Mulunguyo ankafuna chiyani? Ankafunatu ana ompembedza Iye. Motero samala moyo wako ndipo khala wokhulupirika kwa mkazi wako woyamba. 16Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Ndimadana ndi kusudzulana. Ndimadana ndi munthu wochita zankhalwe zotere kwa mkazi wake. Choncho chenjerani, musakhale osakhulupirika. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”
Za tsiku la chiweruzo
17Mwatopetsa Chauta ndi zolankhula zanu. Komabe mumati, “Kodi tamtopetsa bwanji?” Mwamtopetsa ponena kuti, “Aliyense wochita zoipa ndi wabwino pamaso pa Chauta, ndipo Iye amakondwera naye.” Kapenanso pofunsa kuti, “Ali kuti Mulungu wochita zolungamayo?”
Currently Selected:
Mal. 2: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi