GENESIS 8
8
Nowa atuluka m'chingalawa
1 #
Gen. 19.29; Eks. 2.24; 14.21 Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo pa dziko lapansi, naphwa madzi; 2ndipo anatsekedwa akasupe a madzi aakulu ndi mazenera a kumwamba, niletsedwa mvula ya kumwamba; 3ndipo madzi anaphweraphwerabe pa dziko lapansi: pamene anatha masiku zana limodzi kudza makumi atatu madzi anachepa. 4Ndipo chingalawa chinaima pa mapiri a Ararati, mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi awiri la mwezi. 5Ndipo madzi analinkuchepa kufikira mwezi wakhumi; mwezi wakhumi tsiku loyamba mwezi ndipo padaoneka mitu ya mapiri.
6Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la chingalawa limene analipanga: 7ndipo anatulutsa khungubwi, ndipo anatuluka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi pa dziko lapansi. 8Ndipo anatulutsa njiwa imchokere, kuti aone kapena madzi anaphwa pamwamba pa dziko lapansi; 9koma njiwayo siinapeza popondapo phazi lake, nibwera kwa iye kuchingalawako, pakuti madzi analipo pa dziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m'chingalawamo. 10Ndipo analinda masiku ena asanu ndi awiri; natulutsanso njiwayo m'chingalawamo; 11ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, taonani, m'kamwa mwake munali tsamba la azitona lothyoledwa: ndipo anadziwa Nowa kuti madzi analimkuphwa pa dziko lapansi. 12Ndipo analindanso masiku ena asanu ndi awiri; natulutsa njiwayo: ndipo siinabweranso konse kwa iye. 13Ndipo panali chaka cha mazana asanu ndi limodzi kudza chimodzi, mwezi woyamba, tsiku loyamba mwezi, madzi anaphwa pa dziko lapansi; ndipo Nowa anachotsa chindwi lake pachingalawa, nayang'ana, ndipo taonani, padauma pa dziko lapansi. 14Mwezi wachiwiri tsiku la makumi awiri kudza asanu ndi awiri la mwezi, lidauma dziko lapansi.
15Mulungu ndipo ananena kwa Nowa, kuti, 16Tulukamoni m'chingalawamo, iwe ndi ana ako, ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe. 17#Gen. 1.22, 28; 9.1Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse zili ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi; kuti ziswane pa dziko lapansi, zibalane, zichuluke pa dziko lapansi, zibalane, zichuluke pa dziko lapansi. 18Ndipo anatuluka Nowa ndi ana ake, ndi mkazi wake, ndi akazi a ana ake, pamodzi naye: 19zinyama zonse, zokwawa zonse, zouluka zonse, ndi zonse zokwawa pa dziko lapansi, monga mwa mitundu yao, zinatuluka m'chingalawamo.
Nowa amanga guwa la nsembe
20 #
Lev. 11
Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo. 21#Eks. 29.18, 25; Yes. 54.9; Ezk. 16.19; Aef. 5.2; Afi. 4.18Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo. 22#Yer. 5.24; 33.20, 25Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.
Valgt i Øjeblikket:
GENESIS 8: BLPB2014
Markering
Del
Kopiér
Vil du have dine markeringer gemt på tværs af alle dine enheder? Tilmeld dig eller log ind
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi