Mt. 3
3
Za ulaliki wa Yohane Mbatizi
(Mk. 1.1-8; Lk. 3.1-18; Yoh. 1.19-28)
1Pa masiku amenewo kudaabwera Yohane Mbatizi nayamba kulalika m'chipululu cha ku Yudeya. 2#Mt. 4.17; Mk. 1.15Ankati, “Tembenukani mtima chifukwa Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano.” 3#Yes. 40.3Paja Yesaya ankanena za iyeyu pamene adaati,
“Liwu la munthu wofuula m'chipululu:
akunena kuti,
‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye,
ongolani njira zoti adzapitemo.’ ”
4 #
2Maf. 1.8
Yohaneyo ankavala zovala za ubweya wangamira, ndipo ankamangira lamba wachikopa m'chiwuno. Chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wam'thengo. 5Anthu ochokera ku Yerusalemu ndi ku dera lonse la Yudeya, ndi ku madera onse a pafupi ndi mtsinje wa Yordani ankadza kwa iye. 6Ndiye ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumaŵabatiza mu Mtsinje wa Yordaniwo.
7 #
Mt. 12.34; 23.33 Ankaona Ayuda ambiri a m'gulu la Afarisi ndi la Asaduki akubwera kuti iye aŵabatize. Tsono iyeyo ankati, “Ana a njoka inu, adakuchenjezani ndani kuti muthaŵe chilango cha Mulungu chikudzachi? 8Chitanitu ntchito zosonyeza kuti mwatembenukadi mtima. 9#Yoh. 8.33Ndipo m'mitima mwanu musayerekeze zomanena kuti, ‘Atate athu ndi Abrahamu.’ Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu angathe kusandutsa ngakhale miyala ili apayi kuti ikhale ana a Abrahamu. 10#Mt. 7.19Pali pano nkhwangwa ili kale patsinde pa mitengo. Choncho mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, adzaudula nkuuponya pa moto.
11“Ine ndimakubatizani ndi madzi, kusonyeza kuti mwatembenuka mtima. Koma amene akubwera pambuyo panga ndi wamphamvu kuposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kunyamula nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m'moto. 12#Lun. 5.14, 23Chopetera chake chili m'manja kuti apete tirigu wake. Tsono adzathira tirigu m'nkhokwe, koma mankhusu adzaŵatentha m'moto wosazimika.”
Yesu abatizidwa
(Mk. 1.9-11; Lk. 3.21, 22; Yoh. 1.32-34)
13Pa masiku amenewo Yesu adachoka ku Galileya kubwera kwa Yohane ku mtsinje wa Yordani, kuti Yohaneyo amubatize. 14Yohane poyesa kukana, adati, “Ndine amene ndiyenera kubatizidwa ndi Inuyo. Nanga mukubweranso kwa ine kodi?” 15Koma Yesu adamuyankha kuti, “Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m'mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna.” Apo Yohane adavomera.
16Yesu atangobatizidwa, adatuluka m'madzimo. Pomwepo kuthambo kudatsekuka, ndipo adaona Mzimu wa Mulungu akutsika ngati nkhunda nkutera pa Iye. 17#Gen. 22.2; Mas. 2.7; Yes. 42.1; Mt. 12.18; 17.5; Mk. 1.11; Lk. 9.35Tsono kuthamboko kudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera naye kwambiri.”
Currently Selected:
Mt. 3: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi