Lk. 6
6
Za tsiku la Sabata
(Mt. 12.1-8; Mk. 2.23-28)
1 #
Deut. 23.25
Pa tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa m'minda ya tirigu. Ophunzira ake ankathyolako ngala za tirigu, namazifikisa ndi manja, nkumadya. 2Apo Afarisi ena adafunsa kuti, “Bwanji mukuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata?” 3Yesu adati, “Kani simudaŵerenge zimene adaachita Davide, pamene iye ndi anzake adaazingwa nayo njala? 4#Lev. 24.9#1Sam. 21.1-6 Suja adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, natenga buledi woperekedwa kwa Mulungu, naadya, nkupatsakonso anzake aja? Chonsecho nkosaloledwa kuti buledi ameneyo wina aliyense nkumudya kupatula ansembe okha.” 5Tsono Yesu popitiriza adaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro wonse pa zokhudza tsiku la Sabata.”
Yesu achiritsa munthu wopuwala dzanja
(Mt. 12.9-14; Mk. 3.1-6)
6Pa tsiku lina la Sabata Yesu adaloŵa m'nyumba yamapemphero nkumaphunzitsa. M'menemo munali munthu wina wopuwala dzanja lamanja. 7Aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, motero ankamuyang'anitsitsa kuti aone ngati achiritse munthu pa tsiku la Sabata. 8Koma Yesu adaadziŵa maganizo ao, tsono adalamula munthu wopuwala dzanja uja kuti, “Tabwera, udzaime kutsogolo kuno.” Iye adanyamuka nakaima kutsogoloko. 9Pamenepo Yesu adauza anthu aja kuti, “Ntakufunsani, kodi Malamulo amalola chiti pa tsiku la Sabata, kuchitira munthu zabwino, kapena kumchita zoipa? Kupulumutsa moyo wa munthu, kapena kuuwononga?” 10Adaŵayang'ana onsewo, kenaka adalamula munthu uja kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino. 11Koma akuluakulu aja adakwiya kwambiri, nayamba kukambirana zoti achite naye Yesu.
Yesu asankha atumwi khumi ndi aŵiri
(Mt. 10.1-4; Mk. 3.13-19)
12Masiku amenewo Yesu adapita ku phiri kukapemphera, ndipo adachezera usiku wonse akupemphera kwa Mulungu. 13Kutacha adaitana ophunzira ake, nasankhapo khumi ndi aŵiri. Adaŵatcha “atumwi.” 14Anthu ake anali aŵa: Simoni (amene Yesu adamutcha dzina loti Petro) ndi mbale wake Andrea; Yakobe ndi Yohane; Filipo ndi Bartolomeo; 15Mateyo ndi Tomasi; Yakobe (mwana wa Alifeyo) ndi Simoni (wa m'chipani chandale cha Azelote;) 16Yudasi (mwana wa Yakobe) ndiponso Yudasi Iskariote (amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.)
Yesu ayamba kuphunzitsa ndi kumachiritsa odwala
(Mt. 4.23-25)
17Yesu adatsika phiri pamodzi ndi ophunzira ake, naima pa chidikha. Panali khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi anthu ena ambirimbiri ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi ku Yerusalemu, ndi ku mbali yakunyanja, ku Tiro, ndi ku Sidoni. 18Iwo adabwera kudzamva mau ake, ndiponso kuti Iye aŵachiritse. Anthu amene ankasautsidwa ndi mizimu yoipa, amenewonso Iye ankaŵachiritsa. 19Anthu onsewo ankafuna kumkhudza, chifukwa mphamvu zinkatuluka mwa Iye ndi kuŵachiritsa onse.
Za anthu odala ndi anthu atsoka
(Mt. 5.1-12)
20Yesu adayang'ana ophunzira ake, naŵauza kuti,
“Ndinu odala, inu osaukanu, Ufumu wa Mulungu ndi wanu.
21“Ndinu odala, inu amene mukumva njala tsopano, chifukwa mudzakhuta.
“Ndinu odala, inu amene mukulira tsopano, chifukwa mudzakondwa.
22 #
1Pet. 4.14
“Ndinu odala anthu akamadana nanu, akamakusalani ndi kukuchitani chipongwe, ndipo akamaipitsa dzina lanu chifukwa cha Ine Mwana wa Munthu. 23#2Mbi. 36.16; Ntc. 7.52Nthaŵi imeneyo sangalalani ndi kuvina ndi chimwemwe, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi zomwenso makolo ao ankaŵachita aneneri kale.
24“Koma ndinu atsoka, anthu achumanu,
chifukwa mwalandiriratu zokusangalatsani.
25Ndinu atsoka, amene mukukhuta tsopanonu,
chifukwa mudzamva njala.
Ndinu atsoka, amene mukukondwa tsopanonu,
chifukwa mudzamva chisoni ndiponso mudzalira.
26“Ndinu atsoka, anthu onse akamakuyamikani. Paja makolo ao ankachitira aneneri onama akale zomwezi.”
Za kukonda adani
(Mt. 5.38-48; 7.12)
27“Koma inu amene mukumva mau anga, ndikukuuzani kuti, Muzikonda adani anu, muziŵachitira zabwino amene amadana nanu. 28Muziŵafunira madalitso amene amakutembererani, muziŵapempherera amene amakuvutitsani. 29Ngati munthu akumenya pa tsaya, uperekere linalonso. Ndipo munthu akakulanda mwinjiro wako, umlole atenge ndi mkanjo womwe. 30Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akatenga zinthu zako, usamlamule kuti abweze. 31#Tob. 4.15; Mt. 7.12Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo.
32“Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakondanso amene amaŵakonda. 33Ngati muchitira zabwino okhawo amene amakuchitirani zabwino, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amachita chimodzimodzi. 34Ndipo ngati mukongoza okhawo amene mukudziŵa kuti adzakubwezerani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakongoza anzao ochimwa, kuti akalandirenso momwemo. 35#Mphu. 4.10, 11Iyai, inu muzikonda adani anu, muzichita zabwino, ndipo muzikongoza osayembekeza kulandirapo kanthu. Mukatero mudzalandira mphotho yaikulu, ndiye kuti mudzakhala ana a Mulungu Wopambanazonse. Pajatu Iye amachitira zabwino anthu osayamika ndi oipa omwe. 36Monga Atate anu akumwamba ali achifundo, inunso mukhale achifundo.”
Za kuweruza ena
(Mt. 7.1-5)
37“Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani. 38Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”
39 #
Mt. 15.14
Yesu adaŵapheranso fanizo, adati, “Kodi wakhungu nkutsogolera wakhungu mnzake? Nanga onse aŵiri sadzagwa m'dzenje kodi? 40#Mt. 10.24, 25; Yoh. 13.16; 15.20Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense pamene watsiriza maphunziro ake, adzafanafana ndi mphunzitsi wake.
41“Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? 42Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Mbale wanga, taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene iweyo sukuchiwona chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.”
Za mtengo ndi zipatso zake
(Mt. 7.17-20; 12.34-35)
43“Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapenanso mtengo woipa kubala zipatso zabwino. 44#Mt. 12.33Mtengo uliwonse umadziŵika ndi zipatso zake. Sathyola nkhuyu pa minga, kapenanso mphesa pa mtula. 45#Mt. 12.34Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake. Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.”
Za anthu aŵiri omanga nyumba
(Mt. 7.24-27)
46“Bwanji mumangoti, ‘Ambuye, Ambuye,’ koma chonsecho simuchita zimene ndimanena? 47Munthu aliyense wodza kwa ine, namva mau anga nkumaŵagwiritsa ntchito, ndikuuzani amene amafanafana naye. 48Amafanafana ndi munthu womanga nyumba, amene adaakumba mozama, naika maziko pa thanthwe. Tsono chigumula chitafika, madzi ake adagunda nyumbayo, koma sadaigwedeze, chifukwa adaaimanga bwino. 49Koma munthu wongomva mau anga, osaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu amene adaamanga nyumba pamwamba pa nthaka, osakumba maziko. Pamene madzi a chigumula adagunda nyumbayo, pompo idagwa, ndipo kuwonongeka kwake kunali kotheratu.”
Currently Selected:
Lk. 6: BLY-DC
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi