Lk. 23
23
Yesu ku bwalo la Pilato
(Mt. 27.1-2, 11-14; Mk. 15.1-5; Yoh. 18.28-38)
1Gulu lonse lija lidanyamuka nkupita naye Yesu kwa Pilato. 2Iwo adayamba kuneneza Yesu kuti, “Munthu uyu tidampeza akusokeza anthu a mtundu wathu. Amatiletsa kuti tisamakhome msonkho kwa Mfumu ya ku Roma. Amanenanso kuti ati Iyeyu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndiponso mfumu.” 3Pilato adafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adati, “Mwanena nokha.” 4Pamenepo Pilato adauza akulu a ansembe ndi anthu onse aja kuti, “Sindikumpeza mlandu munthuyu.” 5Koma iwo adaumirira nati, “Ameneyu amautsa mitima ya anthu ndi zimene amaphunzitsa m'dziko lonse la Yudeya. Adayambira ku Galileya, mpaka konse kuno.”
Yesu ku bwalo la Herode
6Pamene Pilato adamva zimenezi, adaŵafunsa kuti, “Kodi munthuyu ndi wa ku Galileya?” 7Tsono atamva kuti ngwochokeradi ku dera limene Herode amalamulira, adamtumiza kwa Herodeyo, amene nayenso anali m'Yerusalemu masiku omwewo. 8Herode poona Yesu, adakondwa kwambiri, chifukwa ankamva za Iye, mwakuti kwa nthaŵi yaitali ankafuna atamuwona. Ankayembekeza kuti aone Yesu akuchita chozizwitsa china. 9Herode adamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sadamuyankhe kanthu. 10Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adaimirira pomwepo nkumaneneza Yesu kwambiri. 11Herode pamodzi ndi asilikali ake adayamba kumseka Yesu ndi kumamnyoza. Adamuveka chovala chachifumu, namubwezera kwa Pilato. 12Tsiku lomwelo Herode ndi Pilato adayamba kuyanjana, chonsecho kale ankadana.
Pilato agamula kuti Yesu aphedwe
(Mt. 27.15-26; Mk. 15.6-15; Yoh. 18.39—19.16)
13Pilato adasonkhanitsa akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda ndi anthu wamba. 14Adaŵauza kuti, “Mwadzampereka munthuyu kwa ine kuti ndi munthu wosokeza anthu. Ndipo onani, ine ndamufunsa pamaso panu, koma sindikumpeza mlandu pa zonse zimene mukumnenezazi. 15Herode yemwe sadampeze mlandu, nchifukwa chake wamubweza kwa ife. Ameneyu sadachite kanthu koyenera kumuphera. 16Motero ndingomukwapula kenaka nkumumasula.” [17Pilatoyo ankayenera kuŵamasulira mkaidi mmodzi pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska.] 18Koma anthu onse aja adayamba kufuula pamodzi kuti, “Mchotseni ameneyu, mutimasulire Barabasi.” 19Barabasi anali atamponya m'ndende chifukwa cha kuyambitsa chipolowe mu mzinda, ndiponso kupha munthu.
20Pilato adafuna kumasula Yesu, motero adakakamba nawonso anthu aja. 21Koma iwo adafuulirafuulira kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” 22Pilato adaŵafunsa kachitatu kuti, “Koma wachimwanji Iyeyu? Sindikumpeza mlandu woyenera kumuphera. Motero ndingomukwapula kenaka ndimmasula.” 23Koma iwo adamuumiriza mokweza mau kuti Yesu apachikidwe, kufuula kwao kunkakulirakulira. 24Tsono Pilato adagamula kuti zimene anthu aja ankapempha zichitike. 25Adaŵamasulira munthu amene ankamupempha uja, amene adaaponyedwa m'ndende chifukwa cha chipolowe ndi kupha munthu. Koma Yesu adampereka kwa iwo kuti akamchite zimene ankafuna.
Yesu apachikidwa pa mtanda
(Mt. 27.32-44; Mk. 15.21-32; Yoh. 19.17-27)
26Asilikali adamtenga Yesu napita naye kuti akampachike. Pa njira adagwira munthu wina wa ku Kirene, dzina lake Simoni. Iye ankachokera ku midzi. Adamsenzetsa mtanda wa Yesu kuti aunyamule, azitsatira pambuyo pa Yesuyo.
27Anthu ambirimbiri ankamutsatira. Pakati pao panalinso akazi amene ankadzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumalira chifukwa cha Iye. 28Koma Yesu adaŵacheukira naŵauza kuti, “Inu azimai a ku Yerusalemu, musandilire Ine ai, koma mulire chifukwa cha inu nomwe ndi ana anu. 29Pakuti masiku akubwera pamene anthu azidzati, ‘Ngodala azimai ouma, azimai osabala, azimai amene sadayamwitseko mwana.’ 30#Hos. 10.8; Chiv. 6.16Nthaŵi imeneyo adzapempha mapiri kuti, ‘Tigwereni,’ ndiponso magomo kuti, ‘Tiphimbeni.’ 31Pakuti ngati mtengo wauŵisi auchita zimenezi, nanga mtengo wouma ndiye adzauchita zotani?”
32Asilikali aja adaatenganso anthu ena aŵiri, amene anali zigaŵenga, kuti akaphedwe pamodzi ndi Yesu. 33Pamene adafika ku malo otchedwa Chibade cha Mutu, adapachika Yesu komweko pa mtanda. Komwekonso adapachika zigaŵenga zija, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere. 34#Mas. 22.18Yesu adati, “Atate, muŵakhululukire anthuŵa, chifukwa sakudziŵa zimene akuchita.” Iwo aja adagaŵana zovala zake pakuchita maere. 35#Mas. 22.7Anthu ena onse adaimirira pomwepo nkumaonerera. Komanso akulu a Ayuda ankamunyodola nkumanena kuti, “Adapulumutsa ena, adzipulumutse yekha ngati ndiyedi Mpulumutsi uja amene Mulungu adamsankha.” 36#Mas. 69.21Nawonso asilikali adayamba kumseka. Adadza pafupi ndi Iye, nampatsa vinyo wosasa kuti amwe. 37Adati, “Ngati ndiwedi mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.” 38Pamwamba pa mtanda panali kalata yolembedwa m'Chigriki, m'Chilatini, ndi m'Chiyuda. Mau ake anali akuti, “Uyu ndi mfumu ya Ayuda.”
39Chigaŵenga chimodzi chimene chidaapachikidwa nao, chidayamba kunyoza Yesu nkumanena kuti, “Ha! Kodi iwe sindiwe Mpulumutsi Wolonjezedwa uja? Udzipulumutse wekha ndi ife tomwe.” 40Koma mnzake uja adamdzudzula, adati, “Kodi iwe, suwopa ndi Mulungu yemwe, chidziŵirecho kuti nawenso ukulandira chilango chomwechi? 41Tsonotu ife zikutiyeneradi zimenezi, tikulandira zolingana ndi zimene tidachita. Koma aŵa sadachite cholakwa chilichonse.” 42Ndipo adati, “Inu, mukandikumbikire mukakafika mu Ufumu wanu.” 43Yesu adamuyankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, Kumwamba.”
Kufa kwa Yesu
(Mt. 27.45-56; Mk. 15.33-41; Yoh. 19.28-30)
44 #
Eks. 26.31-33
Nthaŵi itakwana ngati 12 koloko masana, padaagwa mdima pa dziko lonse mpaka pa 3 koloko, 45dzuŵa litangoti bii kuda. Pamenepo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati. 46#Mas. 31.5Tsono Yesu adanena mokweza mau kuti, “Atate ndikupereka mzimu wanga m'manja mwanu.” Atanena zimenezi, adatsirizika.
47Mkulu wa asilikali ataona zimene zidaachitikazo, adatamanda Mulungu, adati, “Ndithudi munthuyu adaalidi wosalakwa konse.” 48Anthu onse amene adaasonkhana kudzaonerera zimene zinkachitikazo, ataona zonsezi, adabwerera kwao akudzigunda pa chifuwa ndi chisoni. 49#Lk. 8.2, 3Anthu onse amene ankadziŵana ndi Yesu, ndiponso azimai amene adaamtsatira kuchokera ku Galileya, adaima patali nkumaona zimenezi.
Yesu aikidwa m'manda
(Mt. 27.57-61; Mk. 15.42-47; Yoh. 19.38-42)
50Panali munthu wina, dzina lake Yosefe, wa ku Arimatea, mudzi wina wa Ayuda. Anali munthu wabwino ndi wolungama, ndipo anali wa m'Bungwe Lalikulu la Ayuda. 51Komatu sankavomereza zimene anzake a m'Bungweli ankapangana, iye ankayembekeza kudza kwa Ufumu wa Mulungu. 52Iyeyu adapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. 53Tsono adautsitsa naukulunga m'nsalu yoyera yabafuta, nkuuika m'manda. Mandawo anali asanaikemo munthu wina aliyense. 54Linali tsiku la chikonzero, tsiku la Sabata likuti liziyamba kumene.
55Azimai aja amene adaabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, adatsatira Yosefe, naona manda ndi m'mene adaaikira mtembo wa Yesu. 56#Eks. 20.10; Deut. 5.14Kenaka adabwerera nakayamba kukonza zonunkhira ndiponso mafuta abwino. Tsono pa tsiku la Sabata adapumula malinga ndi Malamulo a Mose.
Currently Selected:
Lk. 23: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi