Lk. 21
21
Za chopereka cha mai wina wamasiye
(Mk. 12.41-44)
1Yesu atakweza maso, adaona anthu olemera akuponya zopereka zao m'bokosi la ndalama m'Nyumba ya Mulungu.#21.1: M'Nyumba ya Mulungu: M'Nyumba ya Mulungu munali mabokosi khumi ndi atatu oponyamo ndalama zothandizira ntchito za ku Nyumbayo. 2Adaonanso mai wina wamasiye akuponyamo tindalama tiŵiri. 3Pamenepo Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa ena onseŵa. 4Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.”
Yesu alosa za kuwonongedwa kwa Nyumba ya Mulungu
(Mt. 24.1-2; Mk. 13.1-2)
5Anthu ena ankalankhula za Nyumba ya Mulungu kuti adaikongoletsa ndi miyala yokoma, ndiponso ndi mitulo yopereka kwa Mulungu. Yesu adati, 6“Kunena za zinthu mukuziwonazi, masiku adzabwera mwakuti sipadzatsala konse mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa mwala unzake: yonse adzaigumula.”
Za mavuto ndi mazunzo
(Mt. 24.3-14; Mk. 13.3-13)
7 #
2Es. 4.51—5.19
Anthu aja adafunsa Yesu kuti, “Aphunzitsi, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti zonsezi zili pafupi kuchitika?” 8Yesu adati, “Chenjerani kuti anthu angakusokezeni. Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine.’ Azidzatinso, ‘Nthaŵi yayandikira.’ Amenewo musadzaŵatsate. 9Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi za zipoloŵe, musadzachite mantha. Zimenezi zidzayenera kuyamba zaoneka, koma sindiye kuti chimalizo chifika nthaŵi yomweyo.”
10Yesu adaŵauzanso kuti, “Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. 11Kudzachita zivomezi zazikulu. Kudzakhala njala ndi mliri ku malo osiyanasiyana. Kudzakhalanso zoopsa ndi zizindikiro zodabwitsa mu mlengalenga.
12“Koma zisanachitike zonsezi, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzapita nanu ku milandu ku nyumba zamapemphero, nadzakuponyani m'ndende. Adzakuperekani kwa mafumu ndi kwa akulu ena a Boma chifukwa chotsatira Ine. 13Umenewu udzakhala mpata wanu wondichitira umboni. 14#Lk. 12.11, 12Tsono mudziŵiretu kuti musadzachite kukonzekera mau oti mudzaŵayankhe pamlandupo. 15Ineyo ndidzakupatsani mau ndi nzeru zimene adani anuwo sadzatha konse kuzikana kapena kuzitsutsa. 16Makolo anu omwe, abale anu, anansi anu, ndi abwenzi anu, amenewo adzakuperekani kwa adani anu, ndipo ena mwa inu mudzaphedwa. 17Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. 18Koma silidzatayikapo tsitsi lanu ndi limodzi lomwe. 19Mukadzalimbikira, ndiye mudzapate moyo wanu.”
Yesu alosa za kuwonongedwa kwa Yerusalemu
(Mt. 24.15-21; Mk. 13.14-19)
20“Pamene mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, dziŵani kuti chiwonongeko chake chafika. 21Pamenepo amene ali m'Yudeya athaŵire ku mapiri, amene ali mumzinda atulukemo, ndipo amene ali ku minda asadzaloŵenso mumzindamo. 22#Hos. 9.7 Chifukwa masiku amenewo adzakhala masiku akulipsira, kuti zonse zija zimene zidaalembedwa m'Malembo zipherezere. 23Ali ndi tsoka azimai amene adzakhale ndi pathupi, ndiponso azimai oyamwitsa ana masiku amenewo. Pakuti padzagwa masautso aakulu pa dziko lino, ndipo Mulungu adzaŵakwiyira Aisraeleŵa. 24Adzaphedwa pa nkhondo yoopsa, nkutengedwa ngati akapolo a anthu a mitundu ina. Kenaka Yerusalemu akunja adzampondereza mpaka pa mapeto ake a nthaŵi ya akunjawo.” Dan. 9.26; Mika 3.12; Zak. 11.6.
Za kubwera kwa Mwana wa Munthu
(Mt. 24.29-31; Mk. 13.24-27)
25 #
Yes. 13.10; Ezek. 32.7; Yow. 2.31; Chiv. 6.12, 13 “Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuŵa, pa mwezi ndi pa nyenyezi. Pansi pano anthu a mitundu yonse adzada nkhaŵa nkutha nzeru, pomva kukokoma kwa nyanja ndi mafunde ake. 26Ena adzakomoka ndi mantha poyembekezera zimene zikudza pa dziko lonse lapansi, pakuti mphamvu zonse zakuthambo zidzagwedezeka. 27#Dan. 7.13; Chiv. 1.7Pamenepo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo, ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. 28Zimenezi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire nkukweza mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.”
Phunziro la mkuyu
(Mt. 24.32-35; Mk. 13.28-31)
29Pambuyo pake Yesu adaŵaphera fanizo adati, “Yang'anani mkuyu ndi mitengo ina yonse. 30Mukamaona kuti masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira kale. 31Momwemonso, mukadzaona zija ndanenazi zikuchitika, mudzadziŵe kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi. 32Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse. 33Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse.”
Yesu aŵachenjeza kuti akhale maso
34“Chenjerani kuti mitima yanu ingapusitsidwe ndi maphwando, kuledzera, ndi kudera nkhaŵa za moyo uno, kuti tsikulo lingakufikireni modzidzimutsa. 35Pajatu lidzaŵagwera ngati msampha anthu onse okhala pa dziko lonse lapansi. 36Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.”
37 #
Lk. 19.47
Masiku onse Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, koma usiku ankatuluka kukakhala ku phiri lotchedwa Phiri la Olivi. 38Tsono anthu onse ankalaŵirira m'mamaŵa kubwera kwa Iye ku Nyumba ya Mulungu kudzamva mau ake.
Currently Selected:
Lk. 21: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi