Lk. 14
14
Yesu achiritsa munthu wambulu
1Pa tsiku lina la Sabata Yesu adakadya kwa mkulu wina wa m'gulu la Afarisi, ndipo Afarisi anzake ankamupenyetsetsa. 2Pomwepo pamaso pake panali munthu wina wambulu. 3Yesu adafunsa akatswiri a Malamulo ndi Afarisi kuti, “Kodi Malamulo amalola kuchiritsa munthu pa tsiku la Sabata, kapena ai?” 4Koma iwo adangoti chete. Tsono Yesu adatenga munthuyo, ndipo atamchiritsa, adamuuza kuti azipita. 5#Mt. 12.11Kenaka adaŵafunsa kuti, “Ndani mwa inu, bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime pa tsiku la Sabata, sangaitulutse pa Sabata pomwepo?” 6Iwo adasoŵa poyankha.
Za kudzichepetsa ndi za kulandira alendo
7Yesu adaaona kuti anthu amene adaaitanidwa kudzadya nao ankadzisankhira malo aulemu. Tsono adaŵaphera fanizo, adati, 8#Miy. 25.6, 7“Wina akakuitana ku phwando la ukwati, usamakhala pa malo aulemu ai, chifukwa mwina kapena adaitananso wina waulemu kuposa iwe. 9Ndiye iye uja amene adaitana aŵiri nonsenu nkudzakuuza kuti, ‘Pepani, patsani aŵa maloŵa.’ Apo iweyo udzachita manyazi pokakhala pa malo otsika. 10Koma akakuitana, kakhale pa malo otsika, kuti amene adakuitana uja adzakuuze kuti, ‘Bwenzi langa, dzakhale pa malo aulemu pano.’ Apo udzalandira ulemu pamaso pa onse amene uli nao podyera. 11#Mt. 23.12; Lk. 18.14Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.”
12Yesu adauzanso Mfarisi uja amene adaamuitana kudzadya naye kuti, “Ukamakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamaitana abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anzako achuma, chifukwa mwina iwonso adzakuitanako, motero udzalandiriratu mphotho yako. 13Koma iwe ukamakonza phwando, uziitana amphaŵi, otsimphina, opunduka ndi akhungu. 14Apo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe kanthu koti nkukubwezera. Mulungu ndiye adzakubwezera, pamene anthu olungama adzauka kwa akufa.”
Fanizo la phwando lalikulu
(Mt. 22.1-10)
15Munthu wina amene ankadya nao, atamva zimenezi, adauza Yesu kuti, “Ngwodala munthu amene adzadye nao mu Ufumu wa Mulungu.” 16Koma Yesu adamuphera fanizo, adati, “Munthu wina adaakonza phwando lalikulu, naitana anthu ambiri. 17Nthaŵi ya phwando itakwana adatuma wantchito wake kukauza oitanidwa aja kuti, ‘Bwerani, pakuti zonse zakonzeka.’ 18Koma onsewo mmodzimmodzi adayamba kupereka zifukwa zokanira. Woyamba adati, ‘Ndidagula munda, tsono ndikuyenera kupita kuti ndikauwone. Pepani sindibwera.’ 19Wina adati, ‘Ndidagula ng'ombe khumi zapagoli, ndiye ndikukaziyesa. Pepani sindibwera.’ 20Ndipo wina adati, ‘Ndangokwatira tsopano apa, choncho sinditha kubwera.’ 21Tsono wantchitoyo atabwerako adadzasimbira mbuye wake zonsezo. Apo mwini nyumbayo adapsa mtima, nauza wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msanga ku miseu yaikulu ndi yaing'ono ya mumzinda muno ukapeze anthu osauka, otsimphina, akhungu ndi opunduka, ukabwere nawo kuno.’ 22Atabwerako wantchito uja adati, ‘Bwana, ndachita zija munandilamulazi, koma malo akalipobe.’ 23Apo mbuye uja adamuuza wantchitoyo kuti, ‘Pita ku miseu ndi ku njira za kunja kwa mudzi, ukaŵakakamize anthu kubwera kuno, kuti nyumba yanga idzaze. 24Kunena zoona, mwa anthu amene ndidaaŵaitana aja palibe ndi mmodzi yemwe amene adzalilaŵe phwando langali.’ ”
Za kutsata Yesu
25Chikhamu cha anthu chinkatsagana ndi Yesu. Tsono Iye adatembenuka naŵauza kuti, 26#Mt. 10.37“Aliyense wofuna kukhala wophunzira wanga, azikonda Ine koposa atate ake ndi amai ake, mkazi wake ndi ana ake, abale ake ndi alongo ake, ndiponso koposa ngakhale moyo wake womwe. 27#Mt. 10.38; 16.24; Mk. 8.34; Lk. 9.23Aliyense amene sasenza mtanda wake nkumanditsata, sangakhale wophunzira wanga.
28“Wina mwa inu akafuna kumanga nyumba yosanja, kodi suja amayamba wakhala pansi nkuŵerenga ndalama zofunika, kuti aone ngati ali nazo zokwanira kuitsiriza? 29Akapanda kutero, mwina adzaika maziko, nkulephera kuitsiriza. Apo anthu onse, poona zimenezi, adzayamba kumseka. 30Adzati, ‘Mkulu uyu adaayamba kumanga nyumba, koma adalephera kuitsiriza.’
31“Chimodzimodzinso kodi ndi mfumu iti, popita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, siiyamba yakhala pansi nkuganiza bwino? Imaganiziratu ngati ndi asilikali zikwi khumi ingathe kukamenyana ndi mfumu ina ija, imene ikubwera ndi asilikali zikwi makumi aŵiri. 32Tsono ngati siingathe, idzatuma nthumwi kukapempha mtendere, mfumu ina ija ikali kutali.
33“Chonchonso aliyense mwa inu amene sasiya zonse zimene ali nazo, sangakhale wophunzira wanga.”
Za mchere wotha mphamvu
(Mt. 5.13; Mk. 9.50)
34“Mchere ndi wabwino. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? 35Ulibenso ntchito ngakhale pa munda, kapena pa dzala. Amangoutaya basi. Amene ali ndi makutu akumva, amve!”
Currently Selected:
Lk. 14: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi