Yoh. 8
8
Za mkazi wachigololo
1[Koma Yesu adapita ku Phiri la Olivi. 2M'mamaŵa adabweranso ku Nyumba ya Mulungu. Anthu onse adadza kwa Iye, Iyeyo nkukhala pansi nayamba kuŵaphunzitsa. 3Aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adabwera ndi mai amene adaamugwira akuchita chigololo, nkumukhalitsa pakati pao. 4Tsono adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, mai uyu wagwidwa ali m'kati mochita chigololo. 5#Lev. 20.10; Deut. 22.22-24 Paja m'buku la Malamulo Mose adatilamula kuti munthu wotere tizipha pakumponya miyala. Nanga Inuyo mukuti chiyani pamenepa?” 6Adaamufunsa funsoli kuti amuyese ndi kumpeza chifukwa. Koma Yesu adaŵerama, nayamba kulemba pansi ndi chala chake. 7#Sus. 1.34Popeza kuti iwo adaapitirirabe kumufunsa, Yesu adaŵeramuka naŵauza kuti, “Pakati panupa amene sadachimwepo konse, ayambe ndiye kumponya mwala maiyu.” 8Atatero, adaŵeramanso namalemba pansi. 9Koma iwo atamva zimenezi, adayamba kuchokapo mmodzimmodzi, kuyambira akuluakulu; Yesu nkutsalira yekha, mai uja ali chikhalire pakati pompaja. 10Kenaka Yesu adaŵeramuka namufunsa kuti, “Kodi mai, ali kuti anthu aja? Kodi palibe ndi mmodzi yemwe amene wakuzengani mlandu?” 11Maiyo adati, “Inde Ambuye, palibe.” Tsono Yesu adamuuza kuti, “Inenso sindikukuzengani mlandu. Pitani koma kuyambira tsopano musakachimwenso.”]
Yesu ndiye kuŵala kounikira anthu onse
12 #
Lun. 7.26; Mt. 5.14; Yoh. 9.5 Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.”
13 #
Yoh. 5.31
Apo Afarisi adamuuza kuti, “Ukudzichitira wekha umboni. Umboni wakowo ngwosakwanira.” 14Yesu adati, “Ngakhale ndikudzichitira ndekha umboni, komabe umboni wangawo ngwoona, pakuti ndikudziŵa kumene ndidachokera, ndiponso kumene ndikupita. Koma inu simukudziŵa kumene ndidachokera, kapenanso kumene ndikupita. 15Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu aliyense. 16Koma ndikati ndiweruze, ndimaweruza molungama, pakuti sindili ndekha ai, palinso Atate amene adandituma. 17#Deut. 19.15 Ndipo m'Malamulo anu mudalembedwa kuti umboni wa anthu aŵiri ngwokwanira. 18Ine ndimadzichitira ndekha umboni, nawonso Atate amene adandituma amandichitira umboni.” 19Apo iwo adamufunsa kuti, “Atate akowo ali kuti?” Yesu adati, “Ine simundidziŵa, Atate anganso simuŵadziŵa. Mukadandidziŵa, bwenzi mutaŵadziŵanso Atate anga.”
20Yesu adanena mau ameneŵa pamene ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, m'chipinda cholandiriramo zopereka za anthu. Panalibe amene adamgwira, chifukwa nthaŵi yake inali isanafike.
21Pambuyo pake Yesu adaŵauzanso kuti, “Ine ndikupita. Mudzandifunafuna koma mudzafera m'machimo anu. Kumene ndikupita Ine, inu simungathe kufikako.” 22Apo Ayuda adati, “Kodi kapena akufuna kukadzipha, umo akunena kuti, ‘Kumene ndikupita Ine, inu simungathe kufikako?’ ” 23Yesu adaŵauza kuti, “Inu ndinu ochokera pansi pano, Ine ndine wochokera Kumwamba. Inu ndinu a dziko lino lapansi, Ine sindine wa dziko lino lapansi ai. 24Nchifukwa chake ndakuuzani kuti mudzafera m'machimo anu. Pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine Ndilipo,#8.24, 28: Ine ndine Ndilipo: Mau oti NDILIPO amamveka ngati dzina lachihebri loti YAHWEH. Onani pa Eksodo 3.14. Onaninso ku Matanthauzo a Mau. mudzaferadi m'machimo anu.” 25Apo iwo adamufunsa kuti, “Iweyo ndiwe yani?” Yesu adati, “Nchomwe ndakhala ndikukuuzani chiyambire ndithu. 26Ndili ndi zambiri zoti ndinene za inu, ndiponso zoti ndikutsutsireni. Koma amene adandituma ngwoona, ndipo ndimauza anthu a pansi pano zimene Iyeyo adandiwuza.”
27Anthu aja sadazindikire kuti Yesu akunena za Atate. 28Tsono Yesu adaŵauza kuti, “Mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Ndilipo. Mudzadziŵanso kuti sindichita kanthu pandekha, ndimalankhula zimene Atate adandiphunzitsa. 29Ndipo amene adandituma, ali nane pamodzi. Iye sadandisiye ndekha, chifukwa nthaŵi zonse ndimachita zomkondweretsa.”
30Pamene Yesu ankalankhula zimenezi, anthu ambiri adamkhulupirira.
Zoona zenizeni zopatsa ufulu
31Yesu adauza anthu amene adamkhulupirirawo kuti, “Ngati mumvera mau anga nthaŵi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. 32#1Es. 4.38Mudzadziŵa zoona zenizeni, ndipo zoonazo zidzakusandutsani aufulu.” 33#Mt. 3.9; Lk. 3.8Iwo adati, “Ife ndife ana a Abrahamu, ndipo chikhalire chathu sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Nanga bwanji ukuti, ‘Mudzasanduka aufulu?’ ” 34Yesu adaŵayankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo. 35Kapolo sakhala nao m'banja nthaŵi zonse, koma mwana. 36Tsono ngati Mwana akumasulani, mudzakhaladi mfulu. 37Ndikudziŵa kuti ndinu ana a Abrahamu, komabe mukufuna kundipha, chifukwa simukuvomereza mau anga m'mitima mwanu. 38Ine ndimalankhula zimene ndidaziwona kwa Atate anga, koma inu mumachita zimene mudamva kwa atate anu.”
39Iwo adati, “Ifetu atate athu ndi Abrahamu.” Yesu adaŵauza kuti, “Mukadakhala ana a Abrahamu, bwenzi mukuchita zimene Abrahamuyo ankachita. 40Koma tsopano mukufuna kundipha Ine, amene ndakuuzani zoona zimene ndidamva kwa Mulungu. Abrahamu sadachite zotere. 41Inu mukuchita zimene tate wanu amachita.” Iwo adamuuza kuti, “Ife ndiye sindife ana am'chigololotu ai. Tili ndi Tate mmodzi yekha, ndiye Mulungu.” 42Yesu adati, “Mulungu akadakhaladi Atate anu, bwenzi mutandikonda Ine, chifukwa ndidafumira kwa Mulungu, ndipo tsopano ndili kuno. Sindidabwere ndi ulamuliro wa Ine ndekha ai, koma Iyeyo adachita kundituma. 43Nanga chifukwa chiyani simukumvetsa zimene ndikunena? Chifukwa chake nchakuti simungakonde konse kumva mau anga. 44#Lun. 1.13; 2.24 Inu ndinu ana a Satana. Iye ndiye tate wanu, ndipo mukufuna kumachita zimene tate wanuyo amalakalaka. Iye uja chikhalire ngwopha anthu. Sadakhazikike m'zoona, chifukwa mwa iye mulibe zoona. Kunena bodza ndiye khalidwe lake, pakuti ngwabodza, nkukhalanso chimake cha mabodza onse. 45Koma Ine ndimalankhula zoona, nchifukwa chake simundikhulupirira. 46Kodi ndani mwa inu anganditsimikize kuti ndine wochimwa? Nanga ngati ndikunena zoona, mukulekeranji kundikhulupirira? 47Munthu wochokera kwa Mulungu amatchera khutu ku mau a Mulungu. Koma inu simuchokera kwa Mulungu ai, nchifukwa chake simutchera khutu.”
Yesu anena za Abrahamu
48Ayuda aja pomuyankha Yesu, adati, “Kodi ife sitikunena zoona kuti Iwe ndiwe Msamariya, ndipo kuti ndiwe wogwidwa ndi mizimu yoipa?” 49Yesu adati, “Ine sindidagwidwe ndi mizimu yoipa. Ndimalemekeza Atate anga, koma inu mumandipeputsa. 50Komabe Ine sindidzifunira ndekha ulemu. Alipo wina wondifunira ulemu, ndiye amaweruza. 51Ndithu ndikunenetsa kuti munthu akamvera mau anga, sadzafa konse.” 52Ayudawo adamuuza kuti, “Tsopano tadziŵadi kuti ndiwe wogwidwa ndi mizimu yoipa. Abrahamu adamwalira, aneneri nawonso adamwalira. Ndiye Iwe ukuti, ‘Munthu akamvera mau anga sadzafa konse.’ 53Monga Iweyo nkupambana atate athu Abrahamu amene adamwalira? Anenerinso adamwalira. Kodi umadziyesa yani?”
54Yesu adati, “Ndikadzilemekeza ndekha, ulemu wangawo ngwachabe. Alipo ondilemekeza. Amenewo ndi Atate anga, omwe inuyo mumati ndi Mulungu wanu. 55Inu simudaŵadziŵe, koma Ine ndimaŵadziŵa, mwakuti ndikadati sindiŵadziŵa ndikadakhala wonama ngati inuyo. Koma ndimaŵadziŵa, ndipo ndimamvera mau ao. 56Atate anu Abrahamu adaasekera poyembekeza kuti adzaona tsiku la kubwera kwanga. Adaliwonadi nakondwa.” 57Apo Ayuda adamufunsa kuti, “Zaka zako sizinakwane ndi makumi asanu omwe, ndiye nkukhala utaona Abrahamu?” 58Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti Abrahamu asanabadwe, Ine ndilipo.” 59Pamenepo Ayuda aja adayamba kutola miyala kuti amlase. Koma Yesu adazemba natuluka m'Nyumba ya Mulunguyo.
Currently Selected:
Yoh. 8: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi