Yoh. 7
7
Abale ake a Yesu sadamkhulupirire
1Pambuyo pake Yesu ankayendera dera la Galileya. Sadafune kukayendera dera la Yudeya, chifukwa akuluakulu a Ayuda ankafuna kumupha. 2#Lev. 23.34; Deut. 16.13Nthaŵiyo nkuti chikondwerero cha Misasa#7.2: Chikondwerero cha Misasa: Onani ku Matanthauzo a Mau. Onaninso Lev. 23.33-43. chili pafupi. 3Tsono abale ake a Yesu adamuuza kuti, “Bwanji muchokeko kuno, mupite ku Yudeya kuti ophunzira anu kumeneko nawonso akaone ntchito zamphamvu zimene mukuchitazi. 4Munthu sachita kanthu m'seri akafuna kudziŵika ndi anthu. Popeza kuti Inu mukuchita ntchito zoterezi, mudziwonetse poyera pamaso pa anthu onse.” 5(Ndiye kuti abale akewo ankatero chifukwa ngakhale iwo omwe sankamukhulupirira.) 6Yesu adaŵauza kuti, “Nthaŵi yanga siinafikebe, koma yanu ndi nthaŵi iliyonse. 7Anthu ongokonda zapansipano sangadane nanu, koma amadana ndi Ine, chifukwa ndimapereka umboni wosonyeza kuti ntchito zao nzoipa. 8Inuyo pitani kuchikondwereroko. Ine sindipitako ku chikondwerero chimenechi, chifukwa nthaŵi yanga yoyenera siinafike.” 9Yesu atanena zimenezo, adatsalira m'Galileya.
Yesu apita ku chikondwerero cha Misasa
10Koma abale ake atapita ku chikondwerero cha Misasa chija, Yesu nayenso adapitako. Sadapite moonekera, koma mobisika. 11Akulu a Ayuda ankamufunafuna kuchikondwereroko, nkumafunsana kuti, “Kodi amene uja ali kuti?” 12Ndipo panali manong'onong'o ambiri okamba za Iye pakati pa khamu la anthu. Ena ankanena kuti, “Ndi munthutu wabwino.” Koma ena ankati, “Iyai, amangosokeza anthu ameneyu.” 13Komabe panalibe munthu wolankhula poyera za Iye, chifukwa choopa akulu a Ayuda.
14Chikondwerero chija chikali pakati, Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu nayamba kuphunzitsa. 15Akulu a Ayuda adadabwa nati, “Bwanji munthu ameneyu ali ndi nzeru zotere, pamene sadaphunzire konse?” 16Yesu adati, “Zimene ndimaphunzitsa si zangatu ai, ndi za Atate amene adandituma. 17Aliyense wofuna kuchita kufuna kwa Mulungu, adzadziŵa ngati zimene Ine ndimalankhula nzochokera kwa Mulungu kapena kwa Ine ndekha. 18Amene amangolankhula zakezake, amadzifunira yekha ulemu. Koma yemwe amafunira ulemu amene adamtuma, ameneyo ndiye woona, ndipo mumtima mwake mulibe chinyengo. 19Kodi suja Mose adakupatsani Malamulo a Mulungu? Komabe palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene akuŵatsata. Nanga mukufuniranji kundipha?” 20Koma khamu la anthu lidamuyankha kuti, “Wagwidwa ndi mizimu yoipa Iwe. Akufuna kukupha ndani?” 21Yesu adati, “Ndinangochita ntchito yozizwitsa imodzi yokha, nonsenu nkumadabwa. 22#Lev. 12.3; Gen. 17.10 Mose adakulamulani kuti muziwumbala ana anu aamuna (ngakhale mwambowo si wochokera kwa Mose koma kwa makolo); ndipo inu mumaumbala mwana wamwamuna ngakhale mpa tsiku la Sabata. 23#Yoh. 5.9Mwanayo mumamuumbala pa Sabata, kuwopa kuti Lamulo la Mose lingaphwanyidwe. Bwanji mukuipidwa nane chifukwa ndinachiritsa munthu kwathunthu pa tsiku la Sabata? 24Musamaweruza poyang'ana maonekedwe chabe, koma muziweruza molungama.”
Zoti Yesu ndiyedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja
25Pamenepo anthu ena a ku Yerusalemu adati, “Kodi munthu akufuna kumupha uja, si ameneyu? 26Si uyu akulankhula poyerayu, popandanso wonenapo kanthu! Kodi kapenatu ndiye kuti akuluakulu akuzindikiradi kuti ameneyu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja eti? 27Komatu Mpulumutsi wolonjezedwa uja akadzabwera, palibe amene adzadziŵe kumene wachokera. Koma uyu tonse tikudziŵa kumene adachokera.”
28Pamene Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, adalankhula mokweza mau kuti, “Ine mukundidziŵa, ndipo kumene ndidachokera mukudziŵakonso. Koma sindidabwere mwa kufuna kwanga ai. Atate amene ali wokhulupirika ndiwo adandituma. Inu simukuŵadziŵa. 29Koma Ine ndikuŵadziŵa, chifukwa ndine wochokera kwa Iwo, ndipo ndiwo adandituma.”
30Pamenepo anthu adafuna kumgwira Yesu, koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene adamkhudza, chifukwa nthaŵi yake inali isanafike. 31Koma anthu ambiri a m'khamu limenelo adamkhulupirira, ndipo ankati, “Kodi akadzabwera Mpulumutsi wolonjezedwa uja, adzachita zizindikiro zozizwitsa zoposa zimene munthuyu wachita?”
Asilikali atumidwa kudzagwira Yesu
32Afarisi adamva manong'onong'o a chikhamu cha anthu okamba za Yesu. Tsono iwo pamodzi ndi akulu a ansembe adatuma asilikali a ku Nyumba ya Mulungu kuti akamgwire. 33Apo Yesu adati, “Ndili nanube kanthaŵi pang'ono ndisanapite kwa Atate amene adandituma. 34Mudzandifunafuna, koma simudzandipeza. Ndipo kumene ndizikakhala Ine, inu simungathe kufikako.”
35Pamenepo akulu a Ayudawo adayamba kufunsana kuti, “Kodi iyeyu afuna kupita kuti kumene ife sitingakampeze? Kodi kapena akufuna kupita kwa anzathu amene adabalalikira kwa anthu a mitundu ina? Monga nkuti afuna kukaphunzitsa anthu akunja? 36Akunena kuti, ‘Mudzandifunafuna koma simudzandipeza,’ ndiponso kuti, ‘Kumene ndizikakhala Ine, inu simungakafikeko.’ Kodi mau ameneŵa akutanthauza chiyani?”
Mitsinje ya madzi opatsa moyo
37 #
Lev. 23.36
Tsiku lotsiriza la chikondwerero chija linali lalikulu. Pa tsikulo Yesu adaimirira nkunena mokweza kuti, “Ngati pali munthu ali ndi ludzu, abwere kwa Ine kuti adzamwe. 38#Ezek. 47.1; Zek. 14.8Paja Malembo akuti, ‘Munthu wokhulupirira Ine, mtima wake udzakhala ngati gwelo la mitsinje ya madzi opatsa moyo.’ ” 39(Pakutero Yesu ankanena za Mzimu Woyera amene anthu okhulupirira Iye analikudzalandira. Nthaŵi imeneyo nkuti Mzimu Woyera asanafike, chifukwa Yesu anali asanalandire ulemerero wake.)
Anthu agaŵikana
40Pamene khamu la anthu lidamva mau ameneŵa, ena mwa iwo ankati, “Zoonadi munthuyu ndiye Mneneri uja.”#7.40: Mneneri uja: Onani mau ofotokozera Yoh. 1.21. 41Ena ankanena kuti, “Ameneyu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.” Koma ena ankanena kuti, “Kodi Mpulumutsiyo nkuchokera ku Galileya ngati? 42#2Sam. 7.12; Mik. 5.2 Suja Malembo akuti kholo lake ndi mfumu Davide? Ndipo sujanso akuti adzachokera ku mudzi wa Betelehemu kumene Davideyo anali?”
43Choncho khamu la anthu lidagaŵikana chifukwa cha Iye. 44Ena ankafuna kumgwira, koma panalibe amene adamkhudza.
Kusakhulupirira kwa akulu a Ayuda
45Asilikali a ku Nyumba ya Mulungu aja adabwerera kwa akulu a ansembe ndi kwa Afarisi aja. Iwo adafunsa asilikaliwo kuti, “Bwanji simudabwere naye?” 46Asilikali aja adayankha kuti, “Palibenso wina amene adalankhulapo ngati munthu ameneyo nkale lonse.” 47Apo Afarisi adati, “Kani inunso wakunyengani? 48Kodi mudamvapo kuti pakati pa akuluakulu kapena pakati pa Afarisi alipo wokhulupirira amene uja? 49Koma anthu wambaŵa sadziŵa Malamulo a Mose; ngotembereredwa basi!”
50 #
Yoh. 3.1, 2 Tsono Nikodemo, mmodzi mwa Afarisi, yemwe uja amene kale adaapita kwa Yesu, adafunsa anzakewo kuti, 51“Kodi Malamulo athu amatilola kuweruza munthu tisanamve mau ake kuti tidziŵe zimene wachita?” 52Iwo adati, “Kani iwenso ndiwe wa ku Galileya? Kafunefune m'Malembo ndipo udzaona kuti palibe mneneri wochokera ku Galileya.”
[ 53Pamenepo anthu onse adabwerera kwao.]
Currently Selected:
Yoh. 7: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi