Yoh. 19
19
1Pamenepo Pilato adalamula kuti atenge Yesu ndi kumkwapula. 2Tsono asilikali adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake. Adamuveka chovala chofiirira, 3nadza kwa Iye nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda!” Ndipo adayamba kumuwomba makofi.
4Pilato adatulukanso nauza Ayudawo kuti, “Onani, ndikumtulutsira kuli inu kuno kuti mudziŵe kuti sindikumpeza chifukwa chilichonse.” 5Pamene Yesu adatuluka, atavala nsangamutu ija ndi chovala chofiirira chija, Pilato adati, “Nayutu munthu uja.” 6Akulu a ansembe ndi asilikali a ku Nyumba ya Mulungu aja ataona Yesu, adafuula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” Pilato adaŵauza kuti, “Mtengeni inuyo mukampachike, ine ndiye sindikumpeza chifukwa.” 7Anthuwo adati, “Ife tili ndi lamulo, ndipo potsata lamulolo ayenera kufa, chifukwa ankati, ‘Ndine Mwana wa Mulungu.’ ”
8Pamene Pilato adamva mau ameneŵa, adachita mantha kwabasi. 9Tsono adaloŵanso m'nyumba ya bwanamkubwa ija nafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, kwanu nkuti?” Koma Yesu sadayankhe kanthu. 10Pamenepo Pilato adamufunsa kuti, “Sukundiyankha? Kodi sukudziŵa kuti ine ndili ndi mphamvu zokumasula, ndiponso mphamvu zokupachika?” 11#Lun. 6.3Yesu adati, “Akadapanda kukupatsani mphamvu zimenezo Mulungu, sibwenzi mutakhala nazo konse mphamvu pa Ine. Nchifukwa chake amene wandipereka kwa inu ali ndi tchimo lalikulu koposa.”
12Atamva mau ameneŵa, Pilato adafuna ndithu kummasula Yesu. Koma Ayuda adafuula kuti, “Mukammasula ameneyu, sindinu bwenzi la Mfumu ya ku Roma. Aliyense wodziyesa mfumu, ngwoukira Mfumu ya ku Romayo.” 13Pilato atamva zimenezo, adatulutsa Yesu, nakakhala pa mpando woweruzira milandu, pa malo otchedwa “Bwalo lamiyala” (pa Chiyuda amati “Gabata.”) 14Linali tsiku lokonzekera chikondwerero cha Paska, ndipo nkuti nthaŵi ili ngati 12 koloko masana. Pilato adauza Ayuda kuti, “Nayitu Mfumu yanu.” 15Koma iwo adafuula kuti, “Mchotseni! Mchotseni! Kampachikeni pa mtanda!” Pilato adaŵafunsa kuti, “Ndipachike Mfumu yanu kodi?” Akulu a ansembe adati, “Tilibe mfumu ina ai, koma Mfumu ya ku Roma yokha.” 16Pamenepo Pilato adapereka Yesu kwa iwo kuti akampachike pa mtanda.
Yesu apachikidwa pa mtanda
(Mt. 27.32-44; Mk. 15.21-32; Lk. 23.26-43)
Asilikali aja adamtenga Yesu. 17Iye atasenza mtanda wake, adatuluka naye mu mzinda kupita ku malo otchedwa “Malo a Chibade cha Mutu” (pa Chiyuda amati “Gologota.”) 18Kumeneko adampachika pa mtanda. Adapachikanso anthu ena aŵiri, wina ku dzanja lake lamanja, wina ku dzanja lake lamanzere, Yesu pakati. 19Pilato adalemba chidziŵitso nachiika pamtandapo. Adaalembapo kuti, “Yesu wa ku Nazarete, Mfumu ya Ayuda.” 20Ayuda ambiri adachiŵerenga chidziŵitsocho, chifukwa pamalo pamene Yesu adaapachikidwapo panali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Chidziŵitsocho chidalembedwa m'chilankhulo cha Ayuda, cha Aroma, ndiponso cha Agriki. 21Akulu a ansembe a Ayuda adauza Pilato kuti, “Musalembe kuti, ‘Mfumu ya Ayuda’ ai, koma kuti, ‘Iyeyu ankati Ndine Mfumu ya Ayuda.’ ” 22Koma Pilato adati, “Zimene ndalemba, ndalemba ndatha basi.”
23Asilikali aja atapachika Yesu, adatenga zovala zake, nazigaŵa panai, msilikali aliyense chigawo chake. Adatenganso mkanjo wake. Mkanjowo unali wolukidwa kuyambira pamwamba mpaka pansi, opanda msoko. 24#Mas. 22.18Tsono asilikaliwo adauzana kuti, “Tisaung'ambe, koma tichite mayere kuti tiwone ukhala wa yani.” Zidaayenda choncho kuti zipherezere zimene Malembo adanena kuti,
“Adagaŵana zovala zanga,
ndipo mkanjo wanga adauchitira mayere.”
Zimenezi adachitadi asilikali aja.
25Pafupi ndi mtanda wa Yesu padaaimirira amai ake, ndi mbale wa amai akewo, Maria mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa ku Magadala. 26Pamene Yesu adaona amai ake ndi wophunzira uja amene Iye ankamukonda kwambiri, akuimirira pafupi, adauza amai ake kuti, “Mai, nayu mwana wanu.” 27Adauzanso wophunzirayo kuti, “Naŵa amai ako.” Ndipo kuyambira pamenepo wophunzirayo adaŵatenga amaiwo kumakaŵasamala kwao.
Kufa kwa Yesu
(Mt. 27.45-46; Mk. 15.33-41; Lk. 23.44-49)
28 #
Mas. 69.21; 22.15 Yesu adaadziŵa kuti tsopano zonse wakwaniritsa. Tsono kuti zipherezere zimene Malembo adaanena, Iye adati, “Ndili ndi ludzu.” 29Pomwepo panali mbiya yodzaza ndi vinyo wosasa. Asilikali aja adaviika chinkhupule m'vinyo wosasayo, nkuchitsomeka ku kamtengo ka hisope, nachifikitsa pakamwa pake. 30Yesu atalandira vinyo wosasayo adati, “Zonse ndakwaniritsa.” Kenaka adaŵeramitsa mutu, napereka mzimu.
Amubaya Yesu m'nthiti
31Linali tsiku lokonzekera chikondwerero cha Paska. Akulu a Ayuda sadafune kuti mitemboyo ikhalebe pa mtanda#19.31: …sadafune kuti mitemboyo ikhalebe pa mtanda: Onani pa Deut. 21.22-23. pa tsiku la Sabata, chifukwa Lasabata limenelo linali lalikulu. Nchifukwa chake adakapempha Pilato kuti alamule kuti akathyole miyendo#19.31: …akathyole miyendo: Aroma ankathyola miyendo ya anthu opachikidwa, kuti afe msanga. ya anthu opachikidwa aja, nkuŵachotsa. 32Tsono asilikali adabwera, nathyola miyendo ya mmodzi mwa aŵiri aja amene adaapachikidwa pamodzi ndi Yesu. Adateronso ndi mnzake uja. 33Koma pamene adafika pa Yesu, poona kuti wafa kale, sadathyole miyendo yake. 34Koma mmodzi mwa asilikali aja adamubaya m'nthiti mwake ndi mkondo, ndipo nthaŵi yomweyo mudatuluka magazi ndi madzi. 35Amene adaona zimenezi ndiye akuzichitira umboni, kuti inunso mukhulupirire. Umboni wakewo ngwoona, ndipo mwiniwakeyo akudziŵa kuti zimene akunena nzoona. 36#Eks. 12.46; Num. 9.12; Mas. 34.20 Izi zidaatero kuti zipherezere zimene Malembo adanena kuti, “Sadzathyola fupa lake ndi limodzi lomwe.” 37#Zek. 12.10; Chiv. 1.7 Ndipo penanso Malembo akuti, “Anthu azidzamuyang'ana amene iwo adamubaya.”
Yesu aikidwa m'manda
(Mt. 27.57-61; Mk. 15.42-47; Lk. 23.50-56)
38Pambuyo pake Yosefe wa ku Arimatea adapempha Pilato kuti amlole kukachotsa mtembo wa Yesu. (Yosefeyo anali wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa choopa akulu a Ayuda.) Tsono Pilato atamlola, iye adakachotsa mtembowo. 39#Yoh. 3.1, 2 Kudabweranso Nikodemo, yemwe uja amene adaabwera kwa Yesu usiku poyamba paja. Iye adabwera ndi mafuta onunkhira a mure osanganiza ndi aloe, kulemera kwake ngati makilogaramu 32. 40Anthu aŵiriwo adatenga mtembo wa Yesu, naukulunga m'nsalu zoyera zabafuta pamodzi ndi zonunkhira zija, potsata mwambo wamaliro wachiyuda. 41Kumene Yesu adaapachikidwako kunali munda. Ndipo m'mundamo munali manda atsopano, amene anali asanaikemo munthu. 42Tsono popeza kuti linali tsiku la Ayuda lokonzekera chikondwerero cha Paska, ndipo mandawo anali pafupi, adaika Yesu m'menemo.
Currently Selected:
Yoh. 19: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi