Yoh. 15
15
Yesu ndiye mpesa weniweni
1“Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndi mlimi. 2Iwo amadula nthambi iliyonse mwa Ine imene siibala zipatso. Ndipo nthambi iliyonse yobala zipatso, amaitengulira kuti ibale zipatso zambiri koposa kale. 3Inu mwayera kale chifukwa cha mau amene ndakuuzani. 4Khalani mwa Ine, ndipo Inenso ndidzakhala mwa inu. Nthambi siingathe kubala zipatso payokha ngati siikhala pa mtengo wake. Momwemonso inu ngati simukhala mwa Ine.
5“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu. 6Ngati munthu sakhala mwa Ine, amamtaya kunja monga nthambi yodulidwa, ndipo amauma. Nthambi zotere amazitola, naziponya pa moto ndipo zimapsa. 7Ngati mukhala mwa Ine, ndipo mau anga akhala mwa inu, mupemphe chilichonse chimene mungachifune, ndipo mudzachilandiradi. 8Atate anga amalemekezedwa pamene mubereka zipatso zambiri, ndipo pakutero mumaonetsa kuti ndinu ophunzira anga enieni.
9“Monga momwe Atate andikondera, Inenso ndakukondani. Muzikhala m'chikondi changachi. 10Ngati mutsata malamulo anga, mudzakhala m'chikondi changa, monga momwe Ine ndatsatira malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala m'chikondi chao.
11“Ndakuuzani zimenezi kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu. 12#Yoh. 13.34; 15.17; 1Yoh. 3.23; 2Yoh. 1.5Lamulo langa ndi lakuti muzikondana monga momwe Ine ndakukonderani. 13Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene ndikulamulani. 15Sindikutchulaninso antchito ai, pakuti wantchito sadziŵa zimene mbuye wake akuchita. Koma ndikukutchulani abwenzi, chifukwa zonse zimene ndidamva kwa Atate anga, ndidakudziŵitsani. 16Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani. 17Choncho lamulo langa ndi lakuti muzikondana.”
Anthu odalira zapansipano adzadana ndi akhristu
18“Ngati anthu odalira zapansipano adana nanu, kumbukirani kuti adadana ndi Ine asanadane nanu. 19Mukadakhala a mkhalidwe wao, akadakukondani chifukwa cha kukhala anzao. Koma amadana nanu, chifukwa Ine ndidakusankhani pakati pa iwo, motero sindinu anzao. 20#Mt. 10.24; Lk. 6.40; Yoh. 13.16Kumbukirani mau aja amene ndidakuuzani kuti, ‘Wantchito saposa mbuye wake.’ Ngati Ine adandisautsa, inunso adzakusautsani. Ngati adamvera mau anga, adzamvera mau anunso. 21Koma adzakuchitirani zonsezi chifukwa cha Ine, popeza kuti samdziŵa amene adandituma. 22Ndikadapanda kubwera ndi kulankhula nawo, sakadakhala ndi mlandu. Koma tsopano alibe choti nkukanira mlandu wao. 23Munthu wodana ndi Ine, amadana ndi Atate anganso. 24Ndikadapanda kuchita pakati pao zimene wina aliyense sadazichite, sibwenzi atakhala ndi mlandu. Koma tsopano adaziwonadi, komabe akudana nane ndiponso ndi Atate anga. 25#Mas. 35.19; 69.4 Koma zatere kuti zipherezere zimene zidalembedwa m'buku lao la Malamulo kuti, ‘Adadana nane popanda chifukwa.’
26“Koma pali Nkhoswe imene ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate. Nkhosweyo ndi Mzimu wa choona wofumira mwa Atate. Iyeyo akadzabwera, adzandichitira umboni. 27Inunso mudzandichitira umboni, popeza kuti mwakhala nane kuyambira pa chiyambi.”
Currently Selected:
Yoh. 15: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi