Gen. 6
6
Kuipa kwa mtundu wa anthu
1 #
Yob. 1.6; 2.1 Nthaŵi imeneyo anthu anali atayamba kuchuluka pa dziko lonse lapansi, ndipo adabereka ana aakazi. 2Ana aamuna a Mulungu adaona kuti ana aakazi a anthu anali okongola, nayamba kukwatira amene ankaŵakonda. 3Tsono Chauta adati, “Sindidzalola anthu kukhala ndi moyo mpaka muyaya, popeza kuti munthu ndi thupi limene limafa. Kuyambira tsopano adzangokhala zaka 120.” 4#Num. 13.33; Mphu. 16.7; Bar. 3.26 Pa masiku amenewo, ngakhale pambuyo pakenso, panali anthu amphamvu ataliatali pa dziko lapansi. Anthu ameneŵa ndi amene ankabadwa mwa akazi omwe adaakwatiwa ndi ana a Mulungu aja. Iwoŵa anali ngwazi zomveka ndiponso anthu otchuka pa masiku akalewo.
5 #
Mt. 24.37; Lk. 17.26; 1Pet. 3.20 Pamene Chauta adaona kuti anthu a pa dziko lapansi aipa koopsa, ndiponso kuti mitima yao inali yodzaza ndi maganizo oipa, 6adamva chisoni kuti adalenga anthu ndi kuŵakhazika pa dziko lapansi, ndipo adavutika mu mtima. 7Tsono adati, “Anthu onse amene ndaŵalenga, ndidzaŵaononga kotheratu. Ndidzaononganso nyama zonse ndi zokwaŵa zomwe pamodzi ndi mbalame, chifukwa ndikumva chisoni kuti ndidalenga zimenezi.” 8Koma Nowa yekha anali wangwiro pamaso pa Chauta.
Nowa apanga chombo
9 #
Mphu. 44.17, 18; 2Pet. 2.5 Nayi mbiri ya Nowa. Nowa anali munthu wochita zokondweretsa Mulungu, wopanda cholakwa, ndipo pa nthaŵi imeneyo adaali yekhayo amene anali wabwino pamaso pa Mulungu. 10Anali ndi ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti. 11Koma anthu ena onse anali oipa pamaso pa Mulungu, ndipo kuipa kwao kudawanda ponseponse. 12Mulungu atayang'ana dziko lapansi, adaona kuti ndi lonyansa, chifukwa anthu onse anali oipa kwambiri.
13Choncho Mulungu adauza Nowa kuti, “Ndatsimikiza mu mtima kuti ndiwononge anthu onse. Ndidzaŵaononga kotheratu chifukwa dziko lonse lapansi ladzaza ndi ntchito zao zoipa. 14Udzipangire chombo ndipo uchipange ndi matabwa a mtengo wa mnjale. Upange zipinda m'menemo, ndipo uchimate phula kunja kwake ndi m'kati momwe. 15M'litali mwake mwa chombocho mukhale mamita 140. M'mimba mwake mukhale mamita 23, ndipo msinkhu wake ukhale wa mamita 13 ndi theka. 16Upange denga la chombocho, ndipo usiye mpata wa masentimita 50 pakati pa dengalo ndi mbali zake. Uchimange mosanjikiza, chikhale cha nyumba zitatu, ndipo m'mbali mwake mukhale chitseko. 17Ndidzagwetsa mvula yachigumula pa dziko lapansi, kuti iwononge zamoyo zonse. Zonse zapadziko zidzafa, 18koma iweyo ndidzachita nawe chipangano. Udzaloŵe m'chombomo iwe pamodzi ndi mkazi wako, ndi ana ako pamodzi ndi akazi ao. 19Ndipo udzatengenso nyama za mtundu uliwonse, yaimuna ndi yaikazi, kuti zisungidwe ndi moyo. 20Mbalame za mtundu uliwonse ndi nyama zazikulu ndi zokwaŵa zomwe, zidzaloŵe m'chombo kuti zisungidwe ndi moyo. 21Udzatengenso zakudya za mtundu uliwonse kuti inu ndi nyamazo muzidzadya.” 22#Ahe. 11.7Motero Nowa adachitadi zonse zimene Mulungu adamlamula.
Currently Selected:
Gen. 6: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi