YouVersion Logo
Search Icon

Gen. 21

21
Za kubadwa kwa Isaki
1Chauta adakumbukira Sara namchitira zimene adaamulonjeza. 2#Ahe. 11.11 Choncho Sarayo adatenga pathupi, nabalira Abrahamu mwana wamwamuna pamene Abrahamuyo anali nkhalamba. Mwana ameneyu adabadwa pa nthaŵi yeniyeni imene Mulungu adaanena. 3Ndipo mwana wa Abrahamuyo, mwana amene Sara adamubalirayo, Abrahamu adamutcha Isaki. 4#Gen. 17.12; Ntc. 7.8 Abrahamu adamuumbala mwanayo ali wa masiku asanu ndi atatu, monga momwe Mulungu adaalamulira. 5Abrahamu nkuti ali wa zaka 100 pamene Isakiyo adabadwa. 6Tsono Sara adati, “Mulungu wandikondweretsa ndi kundiseketsa. Aliyense amene adzamve zimenezi, adzakondwera nane.” 7Ndipo adati, “Akadadziŵa ndani kuti Sara nkuyamwitsa mwana? Komabe ndamubalira mwana wamwamuna Abrahamu pamene ali nkhalamba.”
8Mwanayo adakula, ndipo pa tsiku lakuti amuletsa kuyamwa, Abrahamu adachita phwando lalikulu.
Hagara ndi Ismaele achotsedwa
9Tsiku lina Ismaele, amene Hagara Mwejipito uja adabalira Abrahamu, ankamunyoza Isaki mwana wa Sara. 10#Aga. 4.29, 30 Sara ataona, adauza Abrahamu kuti, “Mchotseni mdzakaziyu pamodzi ndi mwana wake yemweyu. Mwana wa mdzakazi asadzalandireko chuma chanu chimene adzalandire mwana wanga Isaki.” 11Zimenezi zidamuvuta kwambiri Abrahamu, chifukwa chakuti Ismaele nayenso anali mwana wake. 12#Aro. 9.7; Ahe. 11.18 Koma Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Mtima wako usavutike chifukwa cha mwanayo ndi mzikazi wako Hagara. Zonse zimene akukuuza Sara uchite, chifukwa Isakiyu ndi amene adzakhala kholo la zidzukulu zako monga momwe ndidakulonjezera. 13Mwana wa mdzakaziyunso ndidzampatsa ana ambiri, ndipo adzasanduka mtundu ndithu, popeza kuti iyeyunso ndi mwana wako.” 14M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abrahamu adapatsa Hagara chakudya ndi thumba lachikopa la madzi. Kenaka adatenga mwanayo nabereketsa Hagara, ndipo atatero adamuuza kuti azipita. Hagara adachokadi, nkumangoyendayenda m'chipululu cha Beereseba.
15Tsono madzi aja atamthera, adangosiya mwanayo pa chitsamba. 16Iye adakakhala pansi poteropo, pa mtunda wa mamita 100, chifukwa ankati, “Ine sindingathe kumaonerera mwana wanga alikufa chotere.” Ali pansi pomwepo, mwanayo adayamba kulira. 17Mulungu adamumva mwanayo akulira, ndipo mngelo wa Mulungu adalankhula ndi Hagara kuchokera kumwamba, adati, “Kodi iwe Hagara, chikukuvuta nchiyani? Usachite mantha. Mulungu wamva kulira kwa mwanayu. 18Dzuka, pita, ukamnyamule ndi kumgwiritsa ndi dzanja lako. Zidzukulu zako zidzakhala mtundu waukulu.” 19Apo Mulungu adatsekula maso a Hagara, ndipo adaona chitsime. Iye adapita pachitsimepo, nakadzaza thumba lachikopa lija ndi madzi, nkumwetsako mwanayo. 20Mulungu adakhala naye mwanayo mpaka kukula. Adakulira m'chipululu cha Perani, nasanduka katswiri wa uta. 21Mai wakeyo adampezera mkazi wa ku Ejipito.
Abrahamu ndi Abimeleki achita chipangano
22 # Gen. 26.26 Pa nthaŵi imeneyo Abimeleki, pamodzi ndi Fikolo, mkulu wa gulu lake la ankhondo, adapita kwa Abrahamu kukamuuza kuti, “Inu, Mulungu ali nanu pa zonse zimene mumachita. 23Nchifukwa chake tsono, lumbirani pano pamaso pa Mulungu kuti simudzandinyenga ineyo, kapena ana anga, kapenanso zidzukulu zanga. Ine ndakhala wokhulupirika kwa inu, ndiye inunso mulonjeze kuti mudzakhala wokhulupirika kwa ine, m'dziko limene mukukhalamolo.” 24Abrahamu adati, “Ndikulumbira.”
25Pambuyo pake Abrahamu adamdandaulira Abimeleki za chitsime chimene antchito ake adaalanda. 26Abimeleki adati, “Sindikudziŵa amene adachita zimenezi. Ngakhale inu nomwe simudandiwuze, ndipo ine kumva nkomweku.” 27Abrahamu adapatsa Abimeleki nkhosa ndi ng'ombe, ndipo onse aŵiriwo adachita chipangano. 28Abrahamu adapatulako anaankhosa asanu ndi aŵiri kuchotsa pa zoŵeta zake. 29Abimeleki adamufunsa kuti “Chifukwa chiyani mukuchita zimenezi?” 30Abrahamu adayankha kuti, “Inu landirani nkhosa zisanu ndi ziŵirizi, chifukwa mukatero mukuvomereza kuti chitsimechi ndidakumba ndine.” 31Motero malo amenewo adatchedwa Beereseba chifukwa kumeneko ndiko kumene anthu aŵiriwo adachita chipangano. 32Atachita chipangano chimenechi ku Beereseba kuja, Abimeleki ndi Fikolo mkulu wa gulu la ankhondo, adabwerera kwao ku dziko la Afilisti. 33Tsono Abrahamu adabzala mtengo wa mbwemba ku Beereseba, natama dzina la Chauta, Mulungu Wamuyaya, mopemba. 34Ndipo adakhala m'dziko la Afilisti nthaŵi yaitali.

Currently Selected:

Gen. 21: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in