Gen. 19
19
Kuchimwa kwa anthu a ku Sodomu
1Angelo aŵiri aja adaloŵa m'Sodomumo madzulo ndi kachisisira, Loti atakhala pafupi ndi chipata cha mzindawo. Tsono Lotiyo atangoŵaona anthuwo, adaimirira nakaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu, nati, 2“Chonde ambuye anga, tiyeni mukafike kunyumba, mukatsuke mapazi ndi kugona komweko. M'maŵa kukacha, mungathe kupitirira ndi ulendo wanu.” Koma iwo adayankha kuti, “Iyai, ife tigona panja mumzinda mommuno.” 3Loti adaumirirabe kuŵapempha, ndipo pambuyo pake iwo adavomera, napita kunyumba kwa Loti. Tsono Loti adaŵachitira phwando. Adaŵaphikira buledi wosafufumitsa naŵakonzera chakudya chokoma kwambiri, anthuwo nkudya. 4Alendowo asanakagone, anthu onse amumzindamo, achinyamata ndi okalamba omwe, adadzazinga nyumbayo. 5#Owe. 19.22-24 Adaitana Loti namufunsa kuti, “Kodi anthu abwera kwanu usiku uno aja ali kuti? Atulutse, abwere kuno kuti tigone nawo.” 6Loti adatuluka panja natseka chitseko. 7Tsono adaŵapempha kuti, “Inu abwenzi anga, musachite zimenezi chifukwa nkulakwa kwambiri kuchita zotere. 8Onani, ine ndili ndi ana aakazi aŵiri, anamwali osadziŵa mwamuna. Bwanji ndikupatseni ana ameneŵa kuti muchite nawo zomwe mukufuna. Koma alendoŵa, musaŵachite kanthu kena kalikonse chifukwa ndi alendo anga, ndipo ndiyenera kuŵatchinjiriza.” 9Koma iwowo adati, “Choka apa, wakudza iwe! Ndiwe yani iwe kuti ungatiwuze zoti tichite? Tachoka apa! Mwina mwake tingathe kukuzunza kwambiri kupambana iwowo.” Motero adamkankha Lotiyo, nasendera kuti akathyole chitseko. 10Koma anthu aŵiri anali m'kati aja adamkokera Lotiyo m'nyumba, natseka chitseko. 11#2Maf. 6.18Kenaka adaŵachititsa khungu anthu onse amene adaaima pabwalowo, achinyamata ndi okalamba omwe, kotero kuti sadathenso kuwona khomo.
12Anthu aŵiriwo adafunsa Loti kuti, “Kodi aliponso wina aliyense amene uli naye kuno? Tenga ana ako aamuna, ana ako aakazi, akamwini ako ndi wina aliyense wachibale amene ali mumzinda muno, mutuluke, 13chifukwa ife tikuti tiwononge malo ano. Chauta waziona zoipa zonse zimene anthu okhala mumzinda muno akuchita, ndipo tatumidwa kuti tiuwononge mzindawu.” 14Pamenepo Loti adapita kwa anyamata amene ankafuna kukwatira ana akewo naŵauza kuti, “Fulumirani, tiyeni tituluke kuno, chifukwa patsala pang'ono kuti Chauta aononge malo ano.” Koma iwowo ankangoyesa nthabwala chabe.
15M'mamaŵa, angelo aja adayesa kumufulumizitsa Loti namuuza kuti, “Fulumira! Iweyo ndi mkazi wako ndi ana ako aakazi aŵiri, mutuluke kupita kunja kwa mzinda, kuti mupulumutse moyo wanu pamene mzinda uno ukukaonongedwa.” 16#2Pet. 2.7 Koma Loti ankakayikabe, tsono Chauta adamumvera chifundo. Motero anthuwo adatenga Loti, mkazi wake ndi ana ake aŵiri aja moŵagwira pa dzanja, naŵatulutsa mumzindamo, nkuŵasiya panja pomwepo. 17Ataŵatulutsira kunja kwa mzindawo, mmodzi mwa angelowo adati, “Thamangani, mupulumutse moyo wanu. Musacheukire m'mbuyo, ndipo musaime m'chigwamo. Thaŵirani ku mapiri kuti mungaphedwe.” 18Koma Loti adamuyankha kuti, “Iyai mbuyanga musatero. 19Mwandikomera mtima kwambiri pakupulumutsa moyo wanga. Komatu mapiriwo ali patali kwambiri. Kuwonongeka kwa malo ano mwanenaku kuchitika ine ndisanafike kumapiriko, ndipo ndifa. 20Apo patsidyapo pali kamzinda kakang'ono. Pamenepo mpafupi, ndingathe kukafika. Bwanji ndipite kumeneko. Nkochepa kwambiri, koma ndikhoza kupulumukirako.” 21Munthuyo adayankha kuti, “Zimenezo ndavomereza. Kamzinda kameneko sindikaononga. 22Fulumira! Thamanga! Sindichita kena kalikonse mpaka iwe utafika kumeneko.” Choncho Loti adathamanga nakafika ku kamzinda kaja. Nchifukwa chake kamzindako adakatcha Zowari.#19.22: Zowari: Ndiye kuti kakang'ono.
Kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora
23Pamene dzuŵa linkatuluka, Loti nkuti atafika kale ku Zowari. 24#Mt. 10.15; 11.23, 24; Lk. 10.12; 17.29; 2Pet. 2.6; Yuda 1.7 Tsono Chauta adagwetsa moto wa sulufule pa Sodomu ndi Gomora kuchokera kumwamba. 25Motero adaonongeratu mizinda imeneyi, pamodzi ndi chigwa chonse ndi anthu onse am'mizindamo, kuphatikizapo zomera zonse za m'dziko limenelo. 26#Lun. 10.7; Lk. 17.32 Koma mkazi wa Loti adaacheukira m'mbuyo, ndiye pomwepo adasanduka mwala wamchere. 27M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abrahamu adathamangira ku malo omwe aja, kumene adaaimirira pamaso pa Chauta. 28Adayang'ana ku mizinda ya Sodomu ndi Gomora ndi ku chigwa chija. Ndipo adangoona utsi uli tolotolo kutuluka m'chigwamo ngati utsi wotuluka m'ng'anjo ya moto.
29Motero pamene Chauta ankaononga mizinda yam'chigwayo, adakumbukira pemphero la Abrahamu, ndipo adapulumutsa Loti ku chiwonongeko chimene chidasakaza mizinda ija m'mene Loti ankakhala.
Chiyambi chake cha Amowabu ndi Aamori
30Popeza kuti Loti ankaopa kukhala ku Zowari, iyeyo pamodzi ndi ana ake aakazi aŵiri aja, adapita ku dziko lamapiri, onsewo nkumakakhala m'mapanga. 31Mwana wamkulu adauza mng'ono wake kuti, “Bambo athuŵa akukalamba tsopano, ndipo palibe munthu ndi mmodzi yemwe pa dziko lapansi woti angatikwatire, kuti tibale ana monga momwe zimachitikira zinthu pa dziko lapansi. 32Tiye tiŵaledzeretse abamboŵa kuti agone nafe, kuti mtundu usathe. 33Choncho usiku womwewo anawo adampatsa vinyo bambo waoyo. Zitatero, mwana wamkuluyo adagona ndi bambo wake. Pamenepo nkuti bamboyo ataledzera kwambiri, kotero kuti sankadziŵa zimene zinkachitika.” 34M'maŵa mwake mwana wamkuluyo adauza mng'ono wake uja kuti, “Ine dzulo ndidagona ndi atate. Tiye tsono tiŵaledzeretsenso kuti iwenso ugone nawo, kuti choncho mtundu wathu usathe.” 35Motero usiku umenewo adamledzeretsanso, ndipo mwana wamng'onoyo adagona ndi bambo wake. Nthaŵi imeneyinso nkuti bamboyo ataledzera, kotero kuti sadadziŵe zochitikazo. 36Mwa njira imeneyi, ana onse aŵiriwo a Loti adatenga pathupi pa bambo wao. 37Mwana wamkuluyo adabala mwana wamwamuna, namutcha Mowabu. Iyeyo ndiye kholo la Amowabu onse. 38Mwana wamng'onoyo nayenso adabala mwana wamwamuna, namutcha Benami. Iyeyo ndiye kholo la Aamoni.
Currently Selected:
Gen. 19: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi