Ntc. 4
4
Petro ndi Yohane ku bwalo la akulu a Ayuda
1Petro ndi Yohane akulankhulabe ndi anthu aja, kudadza ansembe ena pamodzi ndi mkulu wa asilikali a ku Nyumba ya Mulungu,#4.1: asilikali a ku Nyumba ya Mulungu: Mkulu wao anali ndi udindo woyang'ana kuti zonse zichitike molongosoka ku Nyumba ya Mulungu (Ntc. 5.24,26.). ndi Asaduki. 2Iwoŵa anali okwiya chifukwa chakuti atumwi aŵiriwo ankaphunzitsa anthu ndi kulalika kuti, “Popeza kuti Yesu adauka kwa akufa, ndiye kuti akufa adzaukanso.” 3Tsono adaŵagwira, ndipo poti kunali kutada kale, adaŵaika m'ndende kufikira m'maŵa. 4Koma ambiri mwa anthu amene adamva mau aja a atumwi adakhulupirira. Chiŵerengero cha okhulupirirawo chidaakwanira ngati zikwi zisanu.
5M'maŵa mwake atsogoleri a Ayuda, akulu ao, ndiponso aphunzitsi a Malamulo adasonkhana ku Yerusalemu. 6Kunalinso Anasi mkulu wa ansembe onse, pamodzi ndi Kayafa, Yohane, Aleksandro ndi ena onse a kubanja kwa mkulu wa ansembe onse. 7Tsono adaimiritsa Petro ndi Yohane pakati pao naŵafunsa kuti, “Kodi zija mudachitazi, mudazichita ndi mphamvu yanji, kaya mudazichita m'dzina la yani?”
8Petro, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adaŵayankha kuti, “Inu atsogoleri ndi akuluakulu muli apa, 9kodi mukutifunsa ife lero za ntchito yabwino imene idachitika pa munthu wopunduka uja, ndi kuchira kwake? 10Mudziŵetu tsono inu nonse, ndi Aisraele ena onse, kuti munthuyu akuima wamoyo pamaso panu chifukwa cha mphamvu ya dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete. Amene uja inu mudaampachika pa mtanda, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa. 11#Mas. 118.22 Za Yesuyo mau a Mulungu akuti,
“ ‘Mwala umene inu amisiri omanga nyumba mudaukana,
womwewo wasanduka mwala wapangodya,
wofunika koposa.’
12Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”
13Abwalo aja adazizwa poona kulimba mtima kwa Petro ndi Yohane, ndiponso podziŵa kuti anali anthu wamba, osaphunzira kwambiri. Apo adazindikira kuti anali anzake a Yesu. 14Tsono poonanso munthu wochiritsidwa uja ataimirira pafupi ndi Petro ndi Yohane, adasoŵa poŵatsutsira. 15Choncho adaŵalamula kuti atuluke m'bwalo la milandu lija, kenaka abwalowo adayamba kukambirana. 16Adati, “Kodi tiŵachite chiyani anthu ameneŵa? Pajatu anthu onse okhala m'Yerusalemu muno akudziŵa kuti iwoŵa adachitadi chizindikiro chozizwitsa, ndipo ife zimenezo sitingathe kukana. 17Koma kuwopa kuti mbiriyi ingaŵande ponseponse, tiyeni tiwachenjeze moopseza kuti polankhula ndi munthu aliyense asatchulenso dzina la Yesu.” 18Atatero adaŵaitana, naŵalamula kuti asatchule konse kapena kuphunzitsa za dzina la Yesu.
19Koma Petro ndi Yohane adaŵayankha kuti, “Weruzani nokha, kodi pamaso pa Mulungu nkwabwino kumvera inuyo koposa kumvera Mulunguyo? 20Ife ndiye sitingaleke kulankhula za zimene tidaziwona ndi kuzimva.” 21Abwalowo adaŵachenjezanso moopseza koposa kale, naŵamasula. Sadapeze njira yoti nkuŵalangira, popeza kuti anthu onse ankatamanda Mulungu chifukwa cha zimene zidaachitikazo. 22Ndipo munthu wochiritsidwa mododometsayo anali wa zaka zopitirira makumi anai.
Okhulupirira apemphera pamodzi
23Petro ndi Yohane atamasulidwa, adapita kwa anzao naŵasimbira zonse zimene akulu a ansembe ndi akulu ena a Ayuda adaaŵauza. 24#Eks. 20.11; Neh. 9.6; Mas. 146.6Pamene iwo adamva zimenezi, onse adayamba kupemphera ndi mtima umodzi. Adati, “Ambuye, ndinu amene mudalenga dziko lakumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi zonse zili m'menemo. 25#Mas. 2.1, 2 Mwa Mzimu Woyera mudalankhulitsa kholo lathu Davide, mtumiki wanu, pamene adati,
“ ‘Chifukwa chiyani anthu akunja adakalipa,
anthu a mitundu ina adaganiziranji zopandapake?
26Mafumu a dziko lapansi adakonzekera,
akulu a Boma adasonkhana pamodzi
kulimbana ndi Chauta, ndiponso ndi wodzozedwa wake uja?’
27 #
Lk. 23.7-11;
Mt. 27.1, 2; Mk. 15.1; Lk. 23.1; Yoh. 18.28, 29 “Zoonadi, Herode ndi Ponsio Pilato adasonkhana mumzinda muno pamodzi ndi anthu akunja, ndiponso ndi anthu a Israele, kuti alimbane ndi Yesu, Mtumiki wanu wopatulika amene mudamdzoza. 28Motero iwo adachitadi zonse zija zimene Inu mudaakonzeratu kale mwa mphamvu zanu ndi nzeru zanu kuti zichitike. 29Ndiye tsono Ambuye, onani zimene akutiwopsezazi, ndipo mutithandize atumiki anufe, kuti tilankhule mau anu molimba mtima ndithu. 30Tambalitsani dzanja lanu kuti anthu achire, ndipo pachitike zizindikiro ndi zozizwitsa m'dzina la Mtumiki wanu wopatulika.”
31Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.
Okhulupirira agaŵana zinthu zao
32 #
Ntc. 2.44, 45 Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi. Panalibe munthu amene ankati, “Zimene ndiri nazo nzangazanga,” koma aliyense ankapereka zake zonse kuti zikhale za onse. 33Atumwi ankachita umboni ndi mphamvu yaikulu kuti Ambuye Yesu adaukadi kwa akufa, ndipo onse Mulungu ankaŵakomera mtima kwambiri. 34Panalibe munthu wosoŵa kanthu pakati pao, chifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankazigulitsa, namabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi. 35Ndipo ndalamazo ankagaŵira munthu aliyense malinga ndi kusoŵa kwake.
36Panali munthu wina dzina lake Yosefe, wa fuko la Levi, mbadwa ya ku Kipro, amene atumwi adaamutcha Barnabasi, ndiye kuti Wolimbitsa mtima. 37Nayenso adagulitsa munda wake, nabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi.
Currently Selected:
Ntc. 4: BLY-DC
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi