YouVersion Logo
Search Icon

Ntc. 20

20
Paulo apita ku Masedoniya ndi ku Grisi
1Phokoso lija litatha, Paulo adaitanitsa ophunzira aja, naŵalimbitsa mtima. Ndipo atatsazikana nawo, adachoka napita ku Masedoniya. 2Adayendera madera a komweko nalimbitsa mtima anthu ndi mau ambiri. Pambuyo pake adapita ku Grisi, 3nakakhalako miyezi itatu. Pamene anali pafupi kupita ku Siriya pa chombo, Ayuda adamchita chiwembu. Tsono iye adatsimikiza zodzera ku Masedoniya. 4Adamperekeza ndi Sopatere, mwana wa Piro, wa ku Berea; Aristariko ndi Sekundo a ku Tesalonika; Gayo wa ku Deribe; Timoteo; ndi Tikiko ndi Trofimo a ku Asiya. 5Iwoŵa adatsogola nakatidikira ku Troasi. 6Koma ife tidayenda pa chombo kuchokera ku Filipi, itatha Paska, chikondwerero cha mikate yosafufumitsa.#20.6: Paska…yosafufumitsa: Onani mau ofotokozera Ntc. 12.3. Ndipo patapita masiku asanu, tidakumana nawo ku Troasi. Kumeneko tidakhalako masiku asanu ndi aŵiri.
Paulo aukitsa Yutiko ku Troasi
7Pa tsiku loyamba la sabata, tidasonkhana kuti tidye Mgonero,#20.7: tidye Mgonero: Onani mau ofotokozera Ntc. 2.42,46. ndipo Paulo ankakamba ndi anthu. Popeza kuti ankayembekeza kupita m'maŵa mwake, adapitiriza kulankhula mpaka pakati pa usiku. 8M'chipinda cham'mwamba chimene tidaasonkhanamo munali nyale zambiri. 9Mnyamata wina, dzina lake Yutiko, adaakhala pa windo. Tsono Paulo akukambabe ndi anthu aja, Yutikoyo ankaodzera kwambiri, mpaka adagona tulo ndithu, nagwa pansi kuchokera pa nyumba yam'mwamba. Ndipo adamtola ali wakufa. 10Pamenepo Paulo adatsika, nadziponya pa mnyamatayo nkumufungatira nati, “Musavutike, ali moyo.” 11Kenaka Paulo adakweranso, nakanyema nao mkate, nkudya nao. Pambuyo pake adapitiriza kulankhula nao nthaŵi yaitali, nangochoka kutacha kale. 12Anthu aja adatenga mnyamata uja ali moyo, ndipo onse adasangalala kwambiri.
Za ulendo wochokera ku Troasi kupita ku Mileto
13Ife tidatsogola nkukakwera chombo kupita ku Aso, kumene tinkayembekeza kukatengako Paulo. Iye adaakonza motero, chifukwa adaafuna kudzera pa mtunda. 14Pamene iye adakumana nafe ku Aso, adakwera nafe m'chombomo, ndipo tidakafika ku Mitilene. 15Tidachokanso kumeneko m'chombo, ndipo m'maŵa mwake tidakafika pafupi ndi Kiyo. M'maŵa mwakenso tidawolokera ku Samo, ndipo mkucha wake tidakafika ku Mileto. 16Paulo anali atatsimikiza zolambalala Efeso, kuwopa kutaya nthaŵi ku dziko la Asiya. Ankafulumira kuti ngati nkotheka akakhale ali ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste.
Paulo alaŵirana ndi akulu a mpingo a ku Efeso
17Paulo ali ku Mileto, adatumiza mau ku Efeso kuitana akulu a mpingo. 18Iwo atafika, adaŵauza kuti, “Inu nomwe mukudziŵa m'mene ndidakhalira nanu masiku onse, kuyambira tsiku loyamba lija ndidafika ku Asiya. 19Ndinkatumikira Ambuye modzichepetsa kwenikweni, pakati pa chisoni ndi zovuta zimene zidandigwera chifukwa cha ziwembu za Ayuda. 20Mukudziŵa kuti sindidakubisireni kanthu kalikonse koti nkukuthandizani. Ndidakulalikirani ndi kukuphunzitsani poyera ndiponso m'nyumba zanu. 21Ayuda ndi Agriki omwe ndidaŵapempha kolimba kuti atembenukire kwa Mulungu molapa, ndi kumakhulupirira Ambuye athu Yesu.
22“Ndipo tsopano, onani ndikupita ku Yerusalemu, popeza kuti Mzimu Woyera akundilamula. Zimene zikandigwere kumeneko sindikuzidziŵa konse. 23Chokhachi ndikudziŵa kuti Mzimu Woyera wandichenjeza mu mzinda uliwonse kuti ndende ndi mazunzo zikundidikira. 24#2Tim. 4.7Koma sindilabada konse za moyo wanga, ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malinga ndikatsirize ntchito yanga, ndi utumiki umene Ambuye Yesu adandipatsa, ndiye kuti kulalika poyera Uthenga Wabwino wonena za kukoma mtima kwa Mulungu.
25“Tsopano ndikudziŵa kuti inu nonse amene ndidakuyenderani kumakulalikirani za ufumu wa Mulungu, simudzaonanso nkhope yanga ai. 26Nchifukwa chake ndikukuuzani monenetsa lero, kuti ngati ena mwa inu atayike, izo nzao, ine ndilibepo mlandu. 27Pajatu sindidakubisireni kanthu ai, koma ndidakulalikirani zonse zimene Mulungu afuna. 28Mzimu Woyera adakuikani kuti muziyang'anira mpingo wonse. Tsono mudzisamale nokha, ndipo musamalenso mpingowo. Ŵetani nkhosa za mpingo wa Ambuye umene Iwo adauwombola ndi magazi aoao. 29Ndikudziŵa kuti ndikadzachoka ine, padzaloŵa mimbulu yoopsa pakati panu, imene siidzalekerera nkhosazo. 30Ngakhale pakati pa inu nomwe, padzauka ena olankhula zonama nkumakopa ophunzira kuti aŵatsate. 31Ndiye inu khalani maso. Kumbukirani kuti pa zaka zitatu usana ndi usiku sindidaleke kulangiza aliyense mwa inu ndi misozi.
32“Choncho tsopano ndikukuikani m'manja mwa Mulungu, mau ake oonetsa kukoma mtima kwake akusungeni bwino. Mauwo ali ndi mphamvu zakukulitsa mpingo, ndi kukupatsani madalitso onse aja amene Mulungu akusungira anthu ake. 33Sindidasirire ndalama kapena zovala za munthu aliyense ai. 34Inu nomwe mukudziŵa kuti manja angaŵa adagwira ntchito kuti ndipeze zimene ine ndi anzanga tinkasoŵa. 35Pa zonse ndakuwonetsani kuti pakugwira ntchito kolimba motere, tiyenera kuthandiza ofooka. Kumbukirani mau aja a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupatsa kumadalitsa munthu koposa kulandira.’ ”
36Paulo atanena zimenezi, adagwada pansi napemphera nawo pamodzi ena onse aja. 37Onsewo adalira kwambiri. Adamkumbatira Pauloyo namumpsompsona polaŵirana naye. 38Makamaka adachita chisoni chifukwa cha mau ake aja onena kuti iwo sadzaonanso nkhope yake. Pambuyo pake adamperekeza kuchombo.

Currently Selected:

Ntc. 20: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in