ZEKARIYA 3
3
Masomphenya achinai: Satana atsutsana ndi Yoswa, Mulungu amuyesa wolungama
1 #
Ezr. 3.2; Hag. 1.1; Chiv. 12.10 Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima pa dzanja lake lamanja, atsutsana naye. 2#Amo. 4.11; Aro. 11.5; Yud. 9Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto? 3#Yud. 23Koma Yoswa analikuvala nsalu zonyansa naima pamaso pa mthenga. 4#Yes. 61.10; Luk. 15.22Ndipo Iye anayankha nanena ndi iwo akuima pamaso pake, ndi kuti, Mumvule nsalu zonyansazi. Nati kwa iye, Taona, ndakuchotsera mphulupulu zako, ndipo ndidzakuveka zovala za mtengo wake. 5#Eks. 29.6Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pake. Naika nduwira yoyera pamutu pake, namveka ndi zovala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo. 6Ndipo mthenga wa Yehova anamchitira Yoswa umboni, ndi kuti, 7#1Maf. 2.3Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo. 8#Yes. 42.1; Ezk. 3.3Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira. 9#Chiv. 5.6Pakuti taona mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pa mwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzalocha malochedwe ake, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzachotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi. 10#Mik. 4.4Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wake patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.
Currently Selected:
ZEKARIYA 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi