ZEKARIYA 12
12
Ukulu wa Israele m'tsogolo
1 #
Yes. 42.5
Katundu wa mau a Yehova wakunena Israele.
Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m'kati mwake; 2#Yes. 51.17, 22-23Taonani, ndidzaika Yerusalemu akhale chipanda chodzandiritsa kwa mitundu yonse ya anthu yozungulirapo, ndipo chidzafikira Yuda yemwe pomangira misasa Yerusalemu. 3Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a pa dziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao. 4Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzakantha kavalo aliyense ndi kumdabwitsa, ndi womkwera adzayaluka; ndipo ndidzatsegulira maso anga nyumba ya Yuda, ndi kukantha kavalo aliyense wa mitundu ya anthu akhale wakhungu. 5Ndipo akalonga a Yuda adzanena m'mtima mwao, Okhala m'Yerusalemu ndiwo mphamvu yanga m'Yehova wa makamu Mulungu wao. 6#Oba. 18Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, kudzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwake, m'Yerusalemu. 7Ndipo Yehova adzayamba kupulumutsa mahema a Yuda, kuti ulemerero wa nyumba ya Davide ndi ulemerero wa okhala m'Yerusalemu usakulire Yuda. 8#Yow. 3.10Tsiku ilo Yehova adzatchinjiriza okhala m'Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao. 9#Hag. 2.22Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzayesa kuononga amitundu onse akudza kuyambana ndi Yerusalemu. 10#Yow. 2.28; Yoh. 19.34, 37; Chiv. 1.7Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala m'Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba. 11#2Mbi. 35.24Tsiku lomwelo kudzakhala maliro akulu m'Yerusalemu, ngati maliro a Hadadirimoni m'chigwa cha Megido. 12#Mat. 24.30Ndipo dziko lidzalira, banja lililonse pa lokha; banja la nyumba ya Davide pa lokha, ndi akazi ao pa okha; banja la nyumba ya Natani pa lokha, ndi akazi ao pa okha; 13banja la nyumba ya Levi pa lokha, ndi akazi ao pa lokha; banja la Asimei pa okha, ndi akazi ao pa okha; 14mabanja onse otsala, banja lililonse pa lokha, ndi akazi ao pa okha.
Currently Selected:
ZEKARIYA 12: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi