NYIMBO YA SOLOMONI Mau Oyamba
Mau Oyamba
Nyimbo ya Solomoni ndi mndandanda wa ndakatulo za chikondi, ndipo zambiri mwa izo zili ngati nyimbo zimene mwamuna amalankhula kwa mkazi, kapena mkazi kwa mwamuna. Ambiri amakhulupirira kuti Solomoni ndiye analemba nyimboyi.
Ayuda amakhulupirira kuti nyimbozi zikuonetsa za ubale wa Mulungu ndi anthu ake, pamene akhristu amakhulupirira kuti zikuonetsa za ubale wa Yesu ndi mpingo. Nyimbo zake zilipo zisanu ndi imodzi.
Za mkatimu
Nyimbo yoyamba 1.1—2.7
Nyimbo yachiwiri 2.8—3.5
Nyimbo yachitatu 3.6—5.1
Nyimbo yachinai 5.2—6.3
Nyimbo yachisanu 6.4—8.4
Nyimbo yachisanu ndi chimodzi 8.5-14
Currently Selected:
NYIMBO YA SOLOMONI Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi