YouVersion Logo
Search Icon

RUTE 4

4
Bowazi akwatira Rute nabadwa Obedi
1 # Rut. 3.12; 2Sam. 15.2 Ndipo Bowazi anakwera kunka kuchipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Bowazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, patuka, khala pansi apa; napatuka iye, nakhala pansi. 2#1Maf. 21.8; Miy. 31.23Ndipo anatenga amuna khumi a akulu a mudzi, nati, Mukhale pansi apa. Nakhala pansi iwo. 3Pamenepo anati kwa woombolerayo, Naomi anabwerayo ku dziko la Mowabu ati agulitse kadziko kaja kadali ka mbale wathu Elimeleki; 4#Lev. 25.25; Yer. 32.7-8ndipo ndati ndikuululira ichi, ndi kuti, Ugule aka pamaso pa nzika, ndi pamaso akulu a anthu a kwathu. Ukafuna kuombola ombola; koma ukapanda kuombola, undiuze, ndidziwe; pakuti palibe woombola koma iwe, ndi ine pambuyo pako. Pamenepo anati, Ndidzaombola. 5#Rut. 3.13Nati Bowazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo pa dzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmowabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa cholowa chake. 6#Deut. 25.7-8Ndipo woombolera anati, Sindikhoza kuuombola kwa ine ndekha, ndingaononge cholowa changa; udzitengere wekha mphamvu yanga yakuombola; popeza sinditha kuombola. 7#Deut. 25.9Koma kale m'Israele pakuombola ndi pakusinthana, kutsimikiza mlandu wonse, akatero: munthu avula nsapato yake, naipereka kwa mnansi wake; ndiwo matsimikizidwe m'Israele. 8Ndipo woombolayo anati kwa Bowazi, Udzigulire wekha kadzikoko. Navula nsapato yake. 9Nati Bowazi kwa akulu, ndi kwa anthu onse, Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, pa dzanja la Naomi. 10#Rut. 4.5Ndiponso Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa cholowa chake; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ake, ndi pa chipata cha malo ake; inu ndinu mboni lero lino. 11#Mas. 127.3; 128.3Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera m'Efurata, numveke m'Betelehemu; 12ndi nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamara anambalira Yuda, ndi mbeu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu. 13Momwemo Bowazi anatenga Rute, nakhala iye mkazi wake; ndipo analowa kwa iye; nalola Yehova kuti aime, ndipo anabala mwana wamwamuna. 14#Luk. 1.58Pamenepo akazi anati kwa Naomi, Adalitsike Yehova amene sanalole kuti akusowe woombolera lero; nilimveke dzina lake m'Israele. 15#1Sam. 1.8Nakhale uyu wakukubwezera moyo, ndi wodyetsa ukalamba wako; pakuti mpongozi wako amene akukonda, amene aposa ana amuna asanu ndi awiri kukuthandiza, anambala. 16Ndipo Naomi anamtenga mwanayo, namuika pachifuwa pake, nakhala mlezi wake. 17#Luk. 1.59Ndi akazi anansi ake anamutcha dzina, ndi kuti, Kwa Naomi kwambadwira mwana; namutcha dzina lake Obedi; ndiye atate wa Yese atate wa Davide.
18 # Mat. 1.3-6 Iyo ndiyo mibadwo ya Perezi; Perezi anabala Hezironi; 19ndi Hezironi anabala Ramu, ndi Ramu anabala Aminadabu; 20ndi Aminadabu anabala Nasoni, ndi Nasoni anabala Salimoni; 21ndi Salimoni anabala Bowazi, ndi Bowazi anabala Obedi; 22ndi Obedi anabala Yese, ndi Yese anabala Davide.

Currently Selected:

RUTE 4: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in