AROMA Mau Oyamba
Mau Oyamba
Kalata ya Paulo kwa Aroma inalembedwa pofuna kukonzekera za ulendo wa Paulo wopita ku mpingo wa ku Roma. Cholinga chake chinali chakuti akagwire ntchito ndi Akhristu a kumeneko kwa kanthawi, kenaka mothandizidwa ndi iwo, akapitirire mpaka ku Speini. Iye analemba kalatayi pofuna kufotokozera za m'mene iye amachidziwira Chikhristu komanso m'mene Chikhristucho chimayenera kuwongolera moyo okhulupirira. Uthenga wonse umene Paulo amalalikira ukupezeka mu bukuli.
Atatha kuwalonjera anthu a ku mpingo wa ku Roma ndi kuwapempherera, Paulo akunena za mutu wa kalatayi umene uli woti, “Pakuti m'menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.” (1.17)
Kenaka Paulo akutambasula mutu wake wa nkhani. Anthu onse, Ayuda ndi akunja omwe, afunika kuti alungamitsidwe ndi Mulungu, popeza onse ali pansi pa mphamvu ya uchimo. Anthu amalungamitsidwa ndi Mulungu kudzera mu kukhulupirira Yesu Khristu. Kenaka Paulo akulongosola za moyo watsopano umene upezeka polumikizana ndi Yesu. Izi zimachokera mu ubale watsopano ndi Mulungu umene munthu amakhala nao. Okhulupirira ali ndi mtendere ndi Mulungu ndipo Mzimu wa Mulungu amawamasula kuchokera ku mphamvu ya uchimo ndi ya imfa. Mu mutu 5—8 Paulo akunena za cholinga cha lamulo la Mulungu ndi mphamvu ya Mzimu wa Mulungu pa moyo wa okhulupirira. Kenaka mtumwiyu akulimbana ndi funso lakuti kodi Ayuda ndi akunja akulowa bwanji mu cholinga cha Mulungu pa anthu onse. Kenaka akumaliza ponena kuti zimene adachita Ayuda pomukana Yesu chinali chikonzero cha Mulungu pofuna kuti anthu ena onse alandire chisomo cha Mulungu chimene chipezeka mwa Khristu Yesu, ndipo iye akukhulupirira kuti Ayuda sadzakana Khristu mpaka kalekale. Potsiriza penipeni, Paulo akulemba za makhalidwe abwino a Chikhristu, makamaka za kukondana wina ndi mnzake. Akulembanso za mitu ina monga kutumikira Mulungu, udindo wa akhristu m'dziko lao komanso kwa anzao, ndi nkhani yokhudza chikumbumtima. Iye akumaliza kalata yakeyo ndi uthenga wolembera anzake komanso mau oyamika Mulungu.
Za mkatimu
Mau oyamba komanso mutu wa kalata 1.1-17
Kufunikira kwa chipulumutso 1.18—3.20
Njira ya Mulungu ya chipulumutso 3.21—4.25
Moyo watsopano mwa Khristu 5.1—8.39
Cholinga cha Mulungu pa fuko la Israele 9.1—11.36
Makhalidwe abwino a Chikhristu 12.1—15.13
Mau omaliza komanso malonje 15.14—16.27
Currently Selected:
AROMA Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi