YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 93

93
Ufumu wa Mulungu ndiwo wa ulemerero, mphamvu, ndi chiyero
1 # Mas. 147.1 Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu;
wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno;
dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.
2 # Mas. 45.6 Mpando wachifumu wanu ukhazikika kuyambira kale lija;
Inu ndinu wosayambira ndi kale lomwe.
3Mitsinje ikweza, Yehova,
mitsinje ikweza mkokomo wao;
mitsinje ikweza mafunde ao.
4 # Mas. 65.7; 89.9 Yehova Wam'mwamba ndiye wamphamvu,
wakuposa mkokomo wa madzi ambiri,
ndi mafunde olimba a nyanja.
5Mboni zanu zivomerezeka ndithu;
chiyero chiyenera nyumba yanu,
Yehova, kunthawi za muyaya.

Currently Selected:

MASALIMO 93: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MASALIMO 93