YouVersion Logo
Search Icon

NEHEMIYA 9:19-21

NEHEMIYA 9:19-21 BLPB2014

koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiya m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokera usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo. Munawapatsanso mzimu wanu wokoma kuwalangiza, ndipo simunawamana mana anu pakamwa pao; munawapatsanso madzi pa ludzu lao. Ndipo munawalera zaka makumi anai m'chipululu, osasowa kanthu iwo; zovala zao sizinatha, ndi mapazi ao sanatupe.