NEHEMIYA 6:15-16
NEHEMIYA 6:15-16 BLPB2014
Ndipo linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lachisanu la mwezi wa Eluli, titalimanga masiku makumi asanu mphambu awiri. Ndipo kunali atachimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti ntchitoyi inachitika ndi Mulungu wathu.