MATEYU 4
4
Yesu ayesedwa m'chipululu
(Mrk. 1.12-13; Luk. 4.1-13)
1Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu kukayesedwa ndi mdierekezi. 2#Eks. 24.18; 1Maf. 19.8Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pake anamva njala. 3Ndipo woyesayo anafika nanena kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate. 4#Deut. 8.3Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa,
Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha,
koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.
5Pamenepo mdierekezi anamuka naye kumzinda woyera; namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisi, 6#Mas. 91.11-12nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti,
Adzalamula angelo ake za iwe,
ndipo pa manja ao adzakunyamula iwe,
ungagunde konse phazi lako pamwala.
7 #
Deut. 6.16
Yesu ananena naye,
Ndiponso kwalembedwa,
Usamuyese Ambuye Mulungu wako.
8Pomwepo mdierekezi anamuka naye kuphiri lalitali, namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wao; 9nati kwa Iye, Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine. 10#Deut. 6.13Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa,
Ambuye Mulungu wako udzamgwadira,
ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.
11 #
Aheb. 1.14
Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye.
Yesu m'Galileya. Ophunzira oyamba
(Mrk. 1.14-45; Luk. 4.14-44; 5.1-11)
12 #
Mat. 14.3; Mrk. 1.14; Luk. 3.19-20; Yoh. 4.43 Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya; 13ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye m'Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali: 14kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti,
15 #
Yes. 9.1-2; Luk. 2.32 Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali,
njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordani,
Galileya la anthu akunja,
16anthu akukhala mumdima
adaona kuwala kwakukulu,
ndi kwa iwo okhala m'malo a mthunzi wa imfa,
kuwala kunatulukira iwo.
17 #
Mat. 3.2; Mrk. 1.14-15 Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.
18 #
Mrk. 1.16-18; Yoh. 1.42 Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba. 19#Luk. 5.10-11Ndipo Iye ananena nao, Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu. 20#Mrk. 10.28Ndipo iwo anasiya pomwepo makokawo, namtsata Iye. 21#Mrk. 1.19-20Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, m'ngalawa, pamodzi ndi Zebedeo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo. 22Ndipo anasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wao, namtsata Iye.
23 #
Mat. 9.35; Mrk. 1.21, 34, 39; Luk. 4.15, 44 Ndipo Yesu anayendayenda m'Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu. 24Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa. 25#Mrk. 3.7-8Ndipo inamtsata mipingomipingo ya anthu ochokera ku Galileya, ndi ku Dekapoli ndi ku Yerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordani.
Currently Selected:
MATEYU 4: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi