YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 1

1
Makolo a Yesu Khristu monga mwa thupi
1 # Gen. 22.18; Mas. 132.11; Luk. 3.23-38; Yoh. 7.42; Agal. 3.16 Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.
2 # Gen. 21.2-3; 25.26; 29.35 Abrahamu anabala Isaki; ndi Isaki anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake; 3#Gen. 38ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu; 4ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni; ndi Nasoni anabala Salimoni; 5#Rut. 4.18-22ndi Salimoni anabala Bowazi mwa Rahabu; ndi Bowazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Yese; 6#2Sam. 12.24ndi Yese anabala Davide mfumuyo.
Ndipo Davide anabala Solomoni mwa mkazi wa Uriya; 7#1Mbi. 3.10-17ndi Solomoni anabala Rehobowamu; ndi Rehobowamu anabala Abiya; ndi Abiya anabala Asa; 8ndi Asa anabala Yehosafati; ndi Yehosafati anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Uziya; 9ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Hezekiya; 10ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya; 11ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ake pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babiloni.
12Ndipo pambuyo pake pa kutengedwako ku Babiloni, Yekoniya anabala Sealatiele; ndi Sealatiele anabala Zerubabele; 13ndi Zerubabele anabala Abihudi; ndi Abihudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro; 14ndi Azoro anabala Zadoki; ndi Zadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliudi; 15ndi Eliudi anabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo; 16ndi Yakobo anabala Yosefe, mwamuna wake wa Maria, amene Yesu, wotchedwa Khristu, anabadwa mwa iye.
17Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babiloni mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babiloni kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inai.
Kubadwa kwa Yesu Khristu
18 # Luk. 1.27, 35 Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera. 19Koma Yosefe, mwamuna wake, anali wolungama, ndiponso sanafune kunyazitsa iye, nayesa m'mtima kumleka iye m'tseri. 20#Luk. 1.35Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera. 21#Luk. 1.31; Mac. 4.12Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao. 22Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,
23 # Yes. 7.14 Onani namwali adzaima,
nadzabala mwana wamwamuna,
ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele.
Ndilo losandulika, Mulungu nafe. 24Ndipo Yosefe anauka tulo take, nachita monga anamuuza mngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wake; 25#Luk. 2.7, 21ndipo sanamdziwe iye kufikira atabala mwana wake; namutcha dzina lake Yesu.

Currently Selected:

MATEYU 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in